< קֹהֶלֶת 3 >
לַכֹּל זְמָן וְעֵת לְכָל־חֵפֶץ תַּחַת הַשָּׁמָֽיִם׃ | 1 |
Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
עֵת לָלֶדֶת וְעֵת לָמוּת עֵת לָטַעַת וְעֵת לַעֲקוֹר נָטֽוּעַ׃ | 2 |
Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
עֵת לַהֲרוֹג וְעֵת לִרְפּוֹא עֵת לִפְרוֹץ וְעֵת לִבְנֽוֹת׃ | 3 |
Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa, nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
עֵת לִבְכּוֹת וְעֵת לִשְׂחוֹק עֵת סְפוֹד וְעֵת רְקֽוֹד׃ | 4 |
Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala, nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
עֵת לְהַשְׁלִיךְ אֲבָנִים וְעֵת כְּנוֹס אֲבָנִים עֵת לַחֲבוֹק וְעֵת לִרְחֹק מֵחַבֵּֽק׃ | 5 |
Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala, nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
עֵת לְבַקֵּשׁ וְעֵת לְאַבֵּד עֵת לִשְׁמוֹר וְעֵת לְהַשְׁלִֽיךְ׃ | 6 |
Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna, nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
עֵת לִקְרוֹעַ וְעֵת לִתְפּוֹר עֵת לַחֲשׁוֹת וְעֵת לְדַבֵּֽר׃ | 7 |
Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka, nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
עֵת לֶֽאֱהֹב וְעֵת לִשְׂנֹא עֵת מִלְחָמָה וְעֵת שָׁלֽוֹם׃ | 8 |
Nthawi yokondana ndi nthawi yodana, nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.
מַה־יִּתְרוֹן הָֽעוֹשֶׂה בַּאֲשֶׁר הוּא עָמֵֽל׃ | 9 |
Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa?
רָאִיתִי אֶת־הָֽעִנְיָן אֲשֶׁר נָתַן אֱלֹהִים לִבְנֵי הָאָדָם לַעֲנוֹת בּֽוֹ׃ | 10 |
Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu.
אֶת־הַכֹּל עָשָׂה יָפֶה בְעִתּוֹ גַּם אֶת־הָעֹלָם נָתַן בְּלִבָּם מִבְּלִי אֲשֶׁר לֹא־יִמְצָא הָאָדָם אֶת־הַֽמַּעֲשֶׂה אֲשֶׁר־עָשָׂה הָאֱלֹהִים מֵרֹאשׁ וְעַד־סֽוֹף׃ | 11 |
Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.
יָדַעְתִּי כִּי אֵין טוֹב בָּם כִּי אִם־לִשְׂמוֹחַ וְלַעֲשׂוֹת טוֹב בְּחַיָּֽיו׃ | 12 |
Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo.
וְגַם כָּל־הָאָדָם שֶׁיֹּאכַל וְשָׁתָה וְרָאָה טוֹב בְּכָל־עֲמָלוֹ מַתַּת אֱלֹהִים הִֽיא׃ | 13 |
Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa.
יָדַעְתִּי כִּי כָּל־אֲשֶׁר יַעֲשֶׂה הָאֱלֹהִים הוּא יִהְיֶה לְעוֹלָם עָלָיו אֵין לְהוֹסִיף וּמִמֶּנּוּ אֵין לִגְרֹעַ וְהָאֱלֹהִים עָשָׂה שֶׁיִּֽרְאוּ מִלְּפָנָֽיו׃ | 14 |
Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
מַה־שֶּֽׁהָיָה כְּבָר הוּא וַאֲשֶׁר לִהְיוֹת כְּבָר הָיָה וְהָאֱלֹהִים יְבַקֵּשׁ אֶת־נִרְדָּֽף׃ | 15 |
Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale, ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba; Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.
וְעוֹד רָאִיתִי תַּחַת הַשָּׁמֶשׁ מְקוֹם הַמִּשְׁפָּט שָׁמָּה הָרֶשַׁע וּמְקוֹם הַצֶּדֶק שָׁמָּה הָרָֽשַׁע׃ | 16 |
Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano: ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko, ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.
אָמַרְתִּֽי אֲנִי בְּלִבִּי אֶת־הַצַּדִּיק וְאֶת־הָרָשָׁע יִשְׁפֹּט הָאֱלֹהִים כִּי־עֵת לְכָל־חֵפֶץ וְעַל כָּל־הַֽמַּעֲשֶׂה שָֽׁם׃ | 17 |
Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti; “Mulungu adzaweruza olungama pamodzi ndi oyipa omwe, pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse, nthawi ya ntchito iliyonse.”
אָמַרְתִּֽי אֲנִי בְּלִבִּי עַל־דִּבְרַת בְּנֵי הָאָדָם לְבָרָם הָאֱלֹהִים וְלִרְאוֹת שְׁהֶם־בְּהֵמָה הֵמָּה לָהֶֽם׃ | 18 |
Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama.
כִּי מִקְרֶה בְֽנֵי־הָאָדָם וּמִקְרֶה הַבְּהֵמָה וּמִקְרֶה אֶחָד לָהֶם כְּמוֹת זֶה כֵּן מוֹת זֶה וְרוּחַ אֶחָד לַכֹּל וּמוֹתַר הָאָדָם מִן־הַבְּהֵמָה אָיִן כִּי הַכֹּל הָֽבֶל׃ | 19 |
Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake.
הַכֹּל הוֹלֵךְ אֶל־מָקוֹם אֶחָד הַכֹּל הָיָה מִן־הֶֽעָפָר וְהַכֹּל שָׁב אֶל־הֶעָפָֽר׃ | 20 |
Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko.
מִי יוֹדֵעַ רוּחַ בְּנֵי הָאָדָם הָעֹלָה הִיא לְמָעְלָה וְרוּחַ הַבְּהֵמָה הַיֹּרֶדֶת הִיא לְמַטָּה לָאָֽרֶץ׃ | 21 |
Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”
וְרָאִיתִי כִּי אֵין טוֹב מֵאֲשֶׁר יִשְׂמַח הָאָדָם בְּֽמַעֲשָׂיו כִּי־הוּא חֶלְקוֹ כִּי מִי יְבִיאֶנּוּ לִרְאוֹת בְּמֶה שֶׁיִּהְיֶה אַחֲרָֽיו׃ | 22 |
Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?