< קֹהֶלֶת 10 >
זְבוּבֵי מָוֶת יַבְאִישׁ יַבִּיעַ שֶׁמֶן רוֹקֵחַ יָקָר מֵחָכְמָה מִכָּבוֹד סִכְלוּת מְעָֽט׃ | 1 |
Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira, choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
לֵב חָכָם לִֽימִינוֹ וְלֵב כְּסִיל לִשְׂמֹאלֽוֹ׃ | 2 |
Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
וְגַם־בַּדֶּרֶךְ כשהסכל כְּשֶׁסָּכָל הֹלֵךְ לִבּוֹ חָסֵר וְאָמַר לַכֹּל סָכָל הֽוּא׃ | 3 |
Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu, zochita zake ndi zopanda nzeru ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
אִם־רוּחַ הַמּוֹשֵׁל תַּעֲלֶה עָלֶיךָ מְקוֹמְךָ אַל־תַּנַּח כִּי מַרְפֵּא יַנִּיחַ חֲטָאִים גְּדוֹלִֽים׃ | 4 |
Ngati wolamulira akukwiyira, usachoke pa ntchito yako; kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.
יֵשׁ רָעָה רָאִיתִי תַּחַת הַשָּׁמֶשׁ כִּשְׁגָגָה שֶׁיֹּצָא מִלִּפְנֵי הַשַּׁלִּֽיט׃ | 5 |
Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano, kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
נִתַּן הַסֶּכֶל בַּמְּרוֹמִים רַבִּים וַעֲשִׁירִים בַּשֵּׁפֶל יֵשֵֽׁבוּ׃ | 6 |
Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba, pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
רָאִיתִי עֲבָדִים עַל־סוּסִים וְשָׂרִים הֹלְכִים כַּעֲבָדִים עַל־הָאָֽרֶץ׃ | 7 |
Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
חֹפֵר גּוּמָּץ בּוֹ יִפּוֹל וּפֹרֵץ גָּדֵר יִשְּׁכֶנּוּ נָחָֽשׁ׃ | 8 |
Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha; amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
מַסִּיעַ אֲבָנִים יֵעָצֵב בָּהֶם בּוֹקֵעַ עֵצִים יִסָּכֶן בָּֽם׃ | 9 |
Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo; amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.
אִם־קֵהָה הַבַּרְזֶל וְהוּא לֹא־פָנִים קִלְקַל וַחֲיָלִים יְגַבֵּר וְיִתְרוֹן הכשיר הַכְשֵׁר חָכְמָֽה׃ | 10 |
Ngati nkhwangwa ili yobuntha yosanoledwa, pamafunika mphamvu zambiri potema, koma luso limabweretsa chipambano.
אִם־יִשֹּׁךְ הַנָּחָשׁ בְּלוֹא־לָחַשׁ וְאֵין יִתְרוֹן לְבַעַל הַלָּשֽׁוֹן׃ | 11 |
Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka ngati njokayo yakuluma kale.
דִּבְרֵי פִי־חָכָם חֵן וְשִׂפְתוֹת כְּסִיל תְּבַלְּעֶֽנּוּ׃ | 12 |
Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa, koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
תְּחִלַּת דִּבְרֵי־פִיהוּ סִכְלוּת וְאַחֲרִית פִּיהוּ הוֹלֵלוּת רָעָֽה׃ | 13 |
Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa; potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
וְהַסָּכָל יַרְבֶּה דְבָרִים לֹא־יֵדַע הָאָדָם מַה־שֶׁיִּֽהְיֶה וַאֲשֶׁר יִֽהְיֶה מֵֽאַחֲרָיו מִי יַגִּיד לֽוֹ׃ | 14 |
ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu. Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo, ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?
עֲמַל הַכְּסִילִים תְּיַגְּעֶנּוּ אֲשֶׁר לֹֽא־יָדַע לָלֶכֶת אֶל־עִֽיר׃ | 15 |
Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa; ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.
אִֽי־לָךְ אֶרֶץ שֶׁמַּלְכֵּךְ נָעַר וְשָׂרַיִךְ בַּבֹּקֶר יֹאכֵֽלוּ׃ | 16 |
Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
אַשְׁרֵיךְ אֶרֶץ שֶׁמַּלְכֵּךְ בֶּן־חוֹרִים וְשָׂרַיִךְ בָּעֵת יֹאכֵלוּ בִּגְבוּרָה וְלֹא בַשְּׁתִֽי׃ | 17 |
Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake, kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
בַּעֲצַלְתַּיִם יִמַּךְ הַמְּקָרֶה וּבְשִׁפְלוּת יָדַיִם יִדְלֹף הַבָּֽיִת׃ | 18 |
Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka; ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.
לִשְׂחוֹק עֹשִׂים לֶחֶם וְיַיִן יְשַׂמַּח חַיִּים וְהַכֶּסֶף יַעֲנֶה אֶת־הַכֹּֽל׃ | 19 |
Phwando ndi lokondweretsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo, koma ndalama ndi yankho la chilichonse.
גַּם בְּמַדָּֽעֲךָ מֶלֶךְ אַל־תְּקַלֵּל וּבְחַדְרֵי מִשְׁכָּבְךָ אַל־תְּקַלֵּל עָשִׁיר כִּי עוֹף הַשָּׁמַיִם יוֹלִיךְ אֶת־הַקּוֹל וּבַעַל הכנפים כְּנָפַיִם יַגֵּיד דָּבָֽר׃ | 20 |
Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena.