< תְהִלִּים 79 >

מִזְמ֗וֹר לְאָ֫סָ֥ף אֱֽלֹהִ֡ים בָּ֤אוּ גוֹיִ֨ם ׀ בְּֽנַחֲלָתֶ֗ךָ טִ֭מְּאוּ אֶת־הֵיכַ֣ל קָדְשֶׁ֑ךָ שָׂ֖מוּ אֶת־יְרוּשָׁלִַ֣ם לְעִיִּֽים׃ 1
Salimo la Asafu. Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu; ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.
נָֽתְנ֡וּ אֶת־נִבְלַ֬ת עֲבָדֶ֗יךָ מַ֭אֲכָל לְע֣וֹף הַשָּׁמָ֑יִם בְּשַׂ֥ר חֲ֝סִידֶ֗יךָ לְחַיְתוֹ־אָֽרֶץ׃ 2
Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya, matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.
שָׁפְכ֬וּ דָמָ֨ם ׀ כַּמַּ֗יִם סְֽבִ֘יב֤וֹת יְֽרוּשָׁלִָ֗ם וְאֵ֣ין קוֹבֵֽר׃ 3
Akhetsa magazi monga madzi kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.
הָיִ֣ינוּ חֶ֭רְפָּה לִשְׁכֵנֵ֑ינוּ לַ֥עַג וָ֝קֶ֗לֶס לִסְבִיבוֹתֵֽינוּ׃ 4
Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu, choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.
עַד־מָ֣ה יְ֭הוָה תֶּאֱנַ֣ף לָנֶ֑צַח תִּבְעַ֥ר כְּמוֹ־אֵ֝֗שׁ קִנְאָתֶֽךָ׃ 5
Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?
שְׁפֹ֤ךְ חֲמָתְךָ֨ אֶֽל־הַגּוֹיִם֮ אֲשֶׁ֪ר לֹא־יְדָ֫ע֥וּךָ וְעַ֥ל מַמְלָכ֑וֹת אֲשֶׁ֥ר בְּ֝שִׁמְךָ֗ לֹ֣א קָרָֽאוּ׃ 6
Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina amene sakudziwani Inu, pa maufumu amene sayitana pa dzina lanu;
כִּ֭י אָכַ֣ל אֶֽת־יַעֲקֹ֑ב וְֽאֶת־נָוֵ֥הוּ הֵשַֽׁמּוּ׃ 7
pakuti iwo ameza Yakobo ndi kuwononga dziko lawo.
אַֽל־תִּזְכָּר־לָנוּ֮ עֲוֹנֹ֪ת רִאשֹׁ֫נִ֥ים מַ֭הֵר יְקַדְּמ֣וּנוּ רַחֲמֶ֑יךָ כִּ֖י דַלּ֣וֹנוּ מְאֹֽד׃ 8
Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe, pakuti tili ndi chosowa chachikulu.
עָזְרֵ֤נוּ ׀ אֱלֹ֘הֵ֤י יִשְׁעֵ֗נוּ עַל־דְּבַ֥ר כְּבֽוֹד־שְׁמֶ֑ךָ וְהַצִּילֵ֥נוּ וְכַפֵּ֥ר עַל־חַ֝טֹּאתֵ֗ינוּ לְמַ֣עַן שְׁמֶֽךָ׃ 9
Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.
לָ֤מָּה ׀ יֹאמְר֣וּ הַגּוֹיִם֮ אַיֵּ֪ה אֱֽלֹהֵ֫יהֶ֥ם יִוָּדַ֣ע בַּגּוֹיִ֣ם לְעֵינֵ֑ינוּ נִ֝קְמַ֗ת דַּֽם־עֲבָדֶ֥יךָ הַשָּׁפֽוּךְ׃ 10
Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti, “Ali kuti Mulungu wawo?” Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.
תָּ֤ב֣וֹא לְפָנֶיךָ֮ אֶנְקַ֪ת אָ֫סִ֥יר כְּגֹ֥דֶל זְרוֹעֲךָ֑ ה֝וֹתֵ֗ר בְּנֵ֣י תְמוּתָֽה׃ 11
Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu; ndi mphamvu ya dzanja lanu muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.
וְהָ֘שֵׁ֤ב לִשְׁכֵנֵ֣ינוּ שִׁ֭בְעָתַיִם אֶל־חֵיקָ֑ם חֶרְפָּ֘תָ֤ם אֲשֶׁ֖ר חֵרְפ֣וּךָ אֲדֹנָֽי׃ 12
Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.
וַאֲנַ֤חְנוּ עַמְּךָ֨ ׀ וְצֹ֥אן מַרְעִיתֶךָ֮ נ֤וֹדֶ֥ה לְּךָ֗ לְע֫וֹלָ֥ם לְדֹ֥ר וָדֹ֑ר נְ֝סַפֵּ֗ר תְּהִלָּתֶֽךָ׃ 13
Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu, tidzakutamandani kwamuyaya, kuchokera mʼbado ndi mʼbado tidzafotokoza za matamando anu.

< תְהִלִּים 79 >