< תְהִלִּים 49 >
לַמְנַצֵּ֬חַ ׀ לִבְנֵי־קֹ֬רַח מִזְמֽוֹר׃ שִׁמְעוּ־זֹ֭את כָּל־הָֽעַמִּ֑ים הַ֝אֲזִ֗ינוּ כָּל־יֹ֥שְׁבֵי חָֽלֶד׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
גַּם־בְּנֵ֣י אָ֭דָם גַּם־בְּנֵי־אִ֑ישׁ יַ֝֗חַד עָשִׁ֥יר וְאֶבְיֽוֹן׃ | 2 |
anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka:
פִּ֭י יְדַבֵּ֣ר חָכְמ֑וֹת וְהָג֖וּת לִבִּ֣י תְבוּנֽוֹת׃ | 3 |
Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
אַטֶּ֣ה לְמָשָׁ֣ל אָזְנִ֑י אֶפְתַּ֥ח בְּ֝כִנּ֗וֹר חִידָתִֽי׃ | 4 |
Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.
לָ֣מָּה אִ֭ירָא בִּ֣ימֵי רָ֑ע עֲוֹ֖ן עֲקֵבַ֣י יְסוּבֵּֽנִי׃ | 5 |
Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira.
הַבֹּטְחִ֥ים עַל־חֵילָ֑ם וּבְרֹ֥ב עָ֝שְׁרָ֗ם יִתְהַלָּֽלוּ׃ | 6 |
Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
אָ֗ח לֹא־פָדֹ֣ה יִפְדֶּ֣ה אִ֑ישׁ לֹא־יִתֵּ֖ן לֵאלֹהִ֣ים כָּפְרֽוֹ׃ | 7 |
Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
וְ֭יֵקַר פִּדְי֥וֹן נַפְשָׁ֗ם וְחָדַ֥ל לְעוֹלָֽם׃ | 8 |
Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire,
וִֽיחִי־ע֥וֹד לָנֶ֑צַח לֹ֖א יִרְאֶ֣ה הַשָּֽׁחַת׃ | 9 |
kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda.
כִּ֤י יִרְאֶ֨ה ׀ חֲכָ֘מִ֤ים יָמ֗וּתוּ יַ֤חַד כְּסִ֣יל וָבַ֣עַר יֹאבֵ֑דוּ וְעָזְב֖וּ לַאֲחֵרִ֣ים חֵילָֽם׃ | 10 |
Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
קִרְבָּ֤ם בָּתֵּ֨ימוֹ ׀ לְֽעוֹלָ֗ם מִ֭שְׁכְּנֹתָם לְדֹ֣ר וָדֹ֑ר קָֽרְא֥וּ בִ֝שְׁמוֹתָ֗ם עֲלֵ֣י אֲדָמֽוֹת׃ | 11 |
Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo.
וְאָדָ֣ם בִּ֭יקָר בַּל־יָלִ֑ין נִמְשַׁ֖ל כַּבְּהֵמ֣וֹת נִדְמֽוּ׃ | 12 |
Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama.
זֶ֣ה דַ֭רְכָּם כֵּ֣סֶל לָ֑מוֹ וְאַחֲרֵיהֶ֓ם ׀ בְּפִיהֶ֖ם יִרְצ֣וּ סֶֽלָה׃ | 13 |
Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. (Sela)
כַּצֹּ֤אן ׀ לִֽשְׁא֣וֹל שַׁתּוּ֮ מָ֤וֶת יִ֫רְעֵ֥ם וַיִּרְדּ֘וּ בָ֤ם יְשָׁרִ֨ים ׀ לַבֹּ֗קֶר וְ֭צוּרָם לְבַלּ֥וֹת שְׁא֗וֹל מִזְּבֻ֥ל לֽוֹ׃ (Sheol ) | 14 |
Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu. (Sheol )
אַךְ־אֱלֹהִ֗ים יִפְדֶּ֣ה נַ֭פְשִׁי מִֽיַּד־שְׁא֑וֹל כִּ֖י יִקָּחֵ֣נִי סֶֽלָה׃ (Sheol ) | 15 |
Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini. (Sheol )
אַל־תִּ֭ירָא כִּֽי־יַעֲשִׁ֣ר אִ֑ישׁ כִּֽי־יִ֝רְבֶּה כְּב֣וֹד בֵּיתֽוֹ׃ | 16 |
Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
כִּ֤י לֹ֣א בְ֭מוֹתוֹ יִקַּ֣ח הַכֹּ֑ל לֹא־יֵרֵ֖ד אַחֲרָ֣יו כְּבוֹדֽוֹ׃ | 17 |
Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
כִּֽי־נַ֭פְשׁוֹ בְּחַיָּ֣יו יְבָרֵ֑ךְ וְ֝יוֹדֻ֗ךָ כִּי־תֵיטִ֥יב לָֽךְ׃ | 18 |
Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
תָּ֭בוֹא עַד־דּ֣וֹר אֲבוֹתָ֑יו עַד־נֵ֝֗צַח לֹ֣א יִרְאוּ־אֽוֹר׃ | 19 |
iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala.
אָדָ֣ם בִּ֭יקָר וְלֹ֣א יָבִ֑ין נִמְשַׁ֖ל כַּבְּהֵמ֣וֹת נִדְמֽוּ׃ | 20 |
Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo.