< תְהִלִּים 4 >
לַמְנַצֵּ֥חַ בִּנְגִינ֗וֹת מִזְמ֥וֹר לְדָוִֽד׃ בְּקָרְאִ֡י עֲנֵ֤נִי ׀ אֱלֹ֘הֵ֤י צִדְקִ֗י בַּ֭צָּר הִרְחַ֣בְתָּ לִּ֑י חָ֝נֵּ֗נִי וּשְׁמַ֥ע תְּפִלָּתִֽי׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.
בְּנֵ֥י אִ֡ישׁ עַד־מֶ֬ה כְבוֹדִ֣י לִ֭כְלִמָּה תֶּאֱהָב֣וּן רִ֑יק תְּבַקְשׁ֖וּ כָזָ֣ב סֶֽלָה׃ | 2 |
Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? (Sela)
וּדְע֗וּ כִּֽי־הִפְלָ֣ה יְ֭הוָה חָסִ֣יד ל֑וֹ יְהוָ֥ה יִ֝שְׁמַ֗ע בְּקָרְאִ֥י אֵלָֽיו׃ | 3 |
Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.
רִגְז֗וּ וְֽאַל־תֶּ֫חֱטָ֥אוּ אִמְר֣וּ בִ֭לְבַבְכֶם עַֽל־מִשְׁכַּבְכֶ֗ם וְדֹ֣מּוּ סֶֽלָה׃ | 4 |
Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. (Sela)
זִבְח֥וּ זִבְחֵי־צֶ֑דֶק וּ֝בִטְח֗וּ אֶל־יְהוָֽה׃ | 5 |
Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova.
רַבִּ֥ים אֹמְרִים֮ מִֽי־יַרְאֵ֪נ֫וּ ט֥וֹב נְֽסָה־עָ֭לֵינוּ א֨וֹר פָּנֶ֬יךָ יְהוָֽה׃ | 6 |
Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
נָתַ֣תָּה שִׂמְחָ֣ה בְלִבִּ֑י מֵעֵ֬ת דְּגָנָ֖ם וְתִֽירוֹשָׁ֣ם רָֽבּוּ׃ | 7 |
Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
בְּשָׁל֣וֹם יַחְדָּו֮ אֶשְׁכְּבָ֪ה וְאִ֫ישָׁ֥ן כִּֽי־אַתָּ֣ה יְהוָ֣ה לְבָדָ֑ד לָ֝בֶ֗טַח תּוֹשִׁיבֵֽנִי׃ | 8 |
Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.