< תְהִלִּים 14 >

לַמְנַצֵּ֗חַ לְדָ֫וִ֥ד אָ֘מַ֤ר נָבָ֣ל בְּ֭לִבּוֹ אֵ֣ין אֱלֹהִ֑ים הִֽשְׁחִ֗יתוּ הִֽתְעִ֥יבוּ עֲלִילָ֗ה אֵ֣ין עֹֽשֵׂה־טֽוֹב׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino.
יְֽהוָ֗ה מִשָּׁמַיִם֮ הִשְׁקִ֪יף עַֽל־בְּנֵי־אָ֫דָ֥ם לִ֭רְאוֹת הֲיֵ֣שׁ מַשְׂכִּ֑יל דֹּ֝רֵשׁ אֶת־אֱלֹהִֽים׃ 2
Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu.
הַכֹּ֥ל סָר֮ יַחְדָּ֪ו נֶ֫אֱלָ֥חוּ אֵ֤ין עֹֽשֵׂה־ט֑וֹב אֵ֝֗ין גַּם־אֶחָֽד׃ 3
Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
הֲלֹ֥א יָדְעוּ֮ כָּל־פֹּ֪עֲלֵ֫י אָ֥וֶן אֹכְלֵ֣י עַ֭מִּי אָ֣כְלוּ לֶ֑חֶם יְ֝הוָ֗ה לֹ֣א קָרָֽאוּ׃ 4
Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? Akudya anthu anga ngati chakudya chawo ndipo satamanda Yehova?
שָׁ֤ם ׀ פָּ֣חֲדוּ פָ֑חַד כִּֽי־אֱ֝לֹהִ֗ים בְּד֣וֹר צַדִּֽיק׃ 5
Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.
עֲצַת־עָנִ֥י תָבִ֑ישׁוּ כִּ֖י יְהוָ֣ה מַחְסֵֽהוּ׃ 6
Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka, koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.
מִ֥י יִתֵּ֣ן מִצִּיּוֹן֮ יְשׁוּעַ֪ת יִשְׂרָ֫אֵ֥ל בְּשׁ֣וּב יְ֭הוָה שְׁב֣וּת עַמּ֑וֹ יָגֵ֥ל יַ֝עֲקֹ֗ב יִשְׂמַ֥ח יִשְׂרָֽאֵל׃ 7
Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

< תְהִלִּים 14 >