< מִשְׁלֵי 18 >
לְֽ֭תַאֲוָה יְבַקֵּ֣שׁ נִפְרָ֑ד בְּכָל־תּ֝וּשִׁיָּ֗ה יִתְגַּלָּֽע׃ | 1 |
Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha; iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.
לֹֽא־יַחְפֹּ֣ץ כְּ֭סִיל בִּתְבוּנָ֑ה כִּ֝֗י אִֽם־בְּהִתְגַּלּ֥וֹת לִבּֽוֹ׃ | 2 |
Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.
בְּֽבוֹא־רָ֭שָׁע בָּ֣א גַם־בּ֑וּז וְֽעִם־קָל֥וֹן חֶרְפָּֽה׃ | 3 |
Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera. Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.
מַ֣יִם עֲ֭מֻקִּים דִּבְרֵ֣י פִי־אִ֑ישׁ נַ֥חַל נֹ֝בֵ֗עַ מְק֣וֹר חָכְמָֽה׃ | 4 |
Mawu a munthu ali ngati madzi akuya, kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.
שְׂאֵ֣ת פְּנֵי־רָשָׁ֣ע לֹא־ט֑וֹב לְהַטּ֥וֹת צַ֝דִּ֗יק בַּמִּשְׁפָּֽט׃ | 5 |
Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu; kapena kupondereza munthu wosalakwa.
שִׂפְתֵ֣י כְ֭סִיל יָבֹ֣אֽוּ בְרִ֑יב וּ֝פִ֗יו לְֽמַהֲלֻמ֥וֹת יִקְרָֽא׃ | 6 |
Mawu a chitsiru amautsa mkangano; pakamwa pake pamayitana mkwapulo.
פִּֽי־כְ֭סִיל מְחִתָּה־ל֑וֹ וּ֝שְׂפָתָ֗יו מוֹקֵ֥שׁ נַפְשֽׁוֹ׃ | 7 |
Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake, ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.
דִּבְרֵ֣י נִ֭רְגָּן כְּמִֽתְלַהֲמִ֑ים וְ֝הֵ֗ם יָרְד֥וּ חַדְרֵי־בָֽטֶן׃ | 8 |
Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma; amalowa mʼmimba mwa munthu.
גַּ֭ם מִתְרַפֶּ֣ה בִמְלַאכְתּ֑וֹ אָ֥ח ה֝֗וּא לְבַ֣עַל מַשְׁחִֽית׃ | 9 |
Munthu waulesi pa ntchito yake ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.
מִגְדַּל־עֹ֭ז שֵׁ֣ם יְהוָ֑ה בּֽוֹ־יָר֖וּץ צַדִּ֣יק וְנִשְׂגָּֽב׃ | 10 |
Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.
ה֣וֹן עָ֭שִׁיר קִרְיַ֣ת עֻזּ֑וֹ וּכְחוֹמָ֥ה נִ֝שְׂגָּבָ֗ה בְּמַשְׂכִּיתֽוֹ׃ | 11 |
Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba; chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.
לִפְנֵי־שֶׁ֭בֶר יִגְבַּ֣הּ לֵב־אִ֑ישׁ וְלִפְנֵ֖י כָב֣וֹד עֲנָוָֽה׃ | 12 |
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
מֵשִׁ֣יב דָּ֭בָר בְּטֶ֣רֶם יִשְׁמָ֑ע אִוֶּ֥לֶת הִיא־ל֝֗וֹ וּכְלִמָּֽה׃ | 13 |
Ukayankha usanamvetse bwino nkhani, umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.
רֽוּחַ־אִ֭ישׁ יְכַלְכֵּ֣ל מַחֲלֵ֑הוּ וְר֥וּחַ נְ֝כֵאָ֗ה מִ֣י יִשָּׂאֶֽנָּה׃ | 14 |
Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda, koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.
לֵ֣ב נָ֭בוֹן יִקְנֶה־דָּ֑עַת וְאֹ֥זֶן חֲ֝כָמִ֗ים תְּבַקֶּשׁ־דָּֽעַת׃ | 15 |
Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina; amafunafuna kudziwa bwino zinthu.
מַתָּ֣ן אָ֭דָם יַרְחִ֣יב ל֑וֹ וְלִפְנֵ֖י גְדֹלִ֣ים יַנְחֶֽנּוּ׃ | 16 |
Mphatso ya munthu imamutsekulira njira yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.
צַדִּ֣יק הָרִאשׁ֣וֹן בְּרִיב֑וֹ וּבָֽא רֵ֝עֵ֗הוּ וַחֲקָרֽוֹ׃ | 17 |
Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.
מִ֭דְיָנִים יַשְׁבִּ֣ית הַגּוֹרָ֑ל וּבֵ֖ין עֲצוּמִ֣ים יַפְרִֽיד׃ | 18 |
Kuchita maere kumathetsa mikangano; amalekanitsa okangana amphamvu.
אָ֗ח נִפְשָׁ֥ע מִקִּרְיַת־עֹ֑ז וּ֝מִדְיָנִ֗ים כִּבְרִ֥יחַ אַרְמֽוֹן׃ | 19 |
Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.
מִפְּרִ֣י פִי־אִ֭ישׁ תִּשְׂבַּ֣ע בִּטְנ֑וֹ תְּבוּאַ֖ת שְׂפָתָ֣יו יִשְׂבָּֽע׃ | 20 |
Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake. Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.
מָ֣וֶת וְ֭חַיִּים בְּיַד־לָשׁ֑וֹן וְ֝אֹהֲבֶ֗יהָ יֹאכַ֥ל פִּרְיָֽהּ׃ | 21 |
Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.
מָצָ֣א אִ֭שָּׁה מָ֣צָא ט֑וֹב וַיָּ֥פֶק רָ֝צ֗וֹן מֵיְהוָֽה׃ | 22 |
Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.
תַּחֲנוּנִ֥ים יְדַבֶּר־רָ֑שׁ וְ֝עָשִׁ֗יר יַעֲנֶ֥ה עַזּֽוֹת׃ | 23 |
Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali.
אִ֣ישׁ רֵ֭עִים לְהִתְרֹעֵ֑עַ וְיֵ֥שׁ אֹ֝הֵ֗ב דָּבֵ֥ק מֵאָֽח׃ | 24 |
Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.