< מַלְאָכִי 2 >
וְעַתָּ֗ה אֲלֵיכֶ֛ם הַמִּצְוָ֥ה הַזֹּ֖את הַכֹּהֲנִֽים׃ | 1 |
“Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.”
אִם־לֹ֣א תִשְׁמְע֡וּ וְאִם־לֹא֩ תָשִׂ֨ימוּ עַל־לֵ֜ב לָתֵ֧ת כָּב֣וֹד לִשְׁמִ֗י אָמַר֙ יְהוָ֣ה צְבָא֔וֹת וְשִׁלַּחְתִּ֤י בָכֶם֙ אֶת־הַמְּאֵרָ֔ה וְאָרוֹתִ֖י אֶת־בִּרְכֽוֹתֵיכֶ֑ם וְגַם֙ אָרוֹתִ֔יהָ כִּ֥י אֵינְכֶ֖ם שָׂמִ֥ים עַל־לֵֽב׃ | 2 |
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu.”
הִנְנִ֨י גֹעֵ֤ר לָכֶם֙ אֶת־הַזֶּ֔רַע וְזֵרִ֤יתִי פֶ֙רֶשׁ֙ עַל־פְּנֵיכֶ֔ם פֶּ֖רֶשׁ חַגֵּיכֶ֑ם וְנָשָׂ֥א אֶתְכֶ֖ם אֵלָֽיו׃ | 3 |
“Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.”
וִֽידַעְתֶּ֕ם כִּ֚י שִׁלַּ֣חְתִּי אֲלֵיכֶ֔ם אֵ֖ת הַמִּצְוָ֣ה הַזֹּ֑את לִֽהְי֤וֹת בְּרִיתִי֙ אֶת־לֵוִ֔י אָמַ֖ר יְהוָ֥ה צְבָאֽוֹת׃ | 4 |
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire.
בְּרִיתִ֣י ׀ הָיְתָ֣ה אִתּ֗וֹ הַֽחַיִּים֙ וְהַ֨שָּׁל֔וֹם וָאֶתְּנֵֽם־ל֥וֹ מוֹרָ֖א וַיִּֽירָאֵ֑נִי וּמִפְּנֵ֥י שְׁמִ֖י נִחַ֥ת הֽוּא׃ | 5 |
Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa.
תּוֹרַ֤ת אֱמֶת֙ הָיְתָ֣ה בְּפִ֔יהוּ וְעַוְלָ֖ה לֹא־נִמְצָ֣א בִשְׂפָתָ֑יו בְּשָׁל֤וֹם וּבְמִישׁוֹר֙ הָלַ֣ךְ אִתִּ֔י וְרַבִּ֖ים הֵשִׁ֥יב מֵעָוֹֽן׃ | 6 |
Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.
כִּֽי־שִׂפְתֵ֤י כֹהֵן֙ יִשְׁמְרוּ־דַ֔עַת וְתוֹרָ֖ה יְבַקְשׁ֣וּ מִפִּ֑יהוּ כִּ֛י מַלְאַ֥ךְ יְהוָֽה־צְבָא֖וֹת הֽוּא׃ | 7 |
“Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse.
וְאַתֶּם֙ סַרְתֶּ֣ם מִן־הַדֶּ֔רֶךְ הִכְשַׁלְתֶּ֥ם רַבִּ֖ים בַּתּוֹרָ֑ה שִֽׁחַתֶּם֙ בְּרִ֣ית הַלֵּוִ֔י אָמַ֖ר יְהוָ֥ה צְבָאֽוֹת׃ | 8 |
Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
וְגַם־אֲנִ֞י נָתַ֧תִּי אֶתְכֶ֛ם נִבְזִ֥ים וּשְׁפָלִ֖ים לְכָל־הָעָ֑ם כְּפִ֗י אֲשֶׁ֤ר אֵֽינְכֶם֙ שֹׁמְרִ֣ים אֶת־דְּרָכַ֔י וְנֹשְׂאִ֥ים פָּנִ֖ים בַּתּוֹרָֽה׃ פ | 9 |
“Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”
הֲל֨וֹא אָ֤ב אֶחָד֙ לְכֻלָּ֔נוּ הֲל֛וֹא אֵ֥ל אֶֽחָ֖ד בְּרָאָ֑נוּ מַדּ֗וּעַ נִבְגַּד֙ אִ֣ישׁ בְּאָחִ֔יו לְחַלֵּ֖ל בְּרִ֥ית אֲבֹתֵֽינוּ׃ | 10 |
Kodi sitili naye Atate mmodzi tonsefe? Kodi anatilenga si Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tikudetsa pangano la makolo athu posamakhulupirirana wina ndi mnzake?
בָּגְדָ֣ה יְהוּדָ֔ה וְתוֹעֵבָ֛ה נֶעֶשְׂתָ֥ה בְיִשְׂרָאֵ֖ל וּבִירֽוּשָׁלִָ֑ם כִּ֣י ׀ חִלֵּ֣ל יְהוּדָ֗ה קֹ֤דֶשׁ יְהוָה֙ אֲשֶׁ֣ר אָהֵ֔ב וּבָעַ֖ל בַּת־אֵ֥ל נֵכָֽר׃ | 11 |
Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo.
יַכְרֵ֨ת יְהוָ֜ה לָאִ֨ישׁ אֲשֶׁ֤ר יַעֲשֶׂ֙נָּה֙ עֵ֣ר וְעֹנֶ֔ה מֵאָהֳלֵ֖י יַֽעֲקֹ֑ב וּמַגִּ֣ישׁ מִנְחָ֔ה לַֽיהוָ֖ה צְבָאֽוֹת׃ פ | 12 |
Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse.
וְזֹאת֙ שֵׁנִ֣ית תַּֽעֲשׂ֔וּ כַּסּ֤וֹת דִּמְעָה֙ אֶת־מִזְבַּ֣ח יְהוָ֔ה בְּכִ֖י וַֽאֲנָקָ֑ה מֵאֵ֣ין ע֗וֹד פְּנוֹת֙ אֶל־הַמִּנְחָ֔ה וְלָקַ֥חַת רָצ֖וֹן מִיֶּדְכֶֽם׃ | 13 |
China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu.
וַאֲמַרְתֶּ֖ם עַל־מָ֑ה עַ֡ל כִּי־יְהוָה֩ הֵעִ֨יד בֵּינְךָ֜ וּבֵ֣ין ׀ אֵ֣שֶׁת נְעוּרֶ֗יךָ אֲשֶׁ֤ר אַתָּה֙ בָּגַ֣דְתָּה בָּ֔הּ וְהִ֥יא חֲבֶרְתְּךָ֖ וְאֵ֥שֶׁת בְּרִיתֶֽךָ׃ | 14 |
Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano.
וְלֹא־אֶחָ֣ד עָשָׂ֗ה וּשְׁאָ֥ר ר֙וּחַ֙ ל֔וֹ וּמָה֙ הָֽאֶחָ֔ד מְבַקֵּ֖שׁ זֶ֣רַע אֱלֹהִ֑ים וְנִשְׁמַרְתֶּם֙ בְּר֣וּחֲכֶ֔ם וּבְאֵ֥שֶׁת נְעוּרֶ֖יךָ אַל־יִבְגֹּֽד׃ | 15 |
Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
כִּֽי־שָׂנֵ֣א שַׁלַּ֗ח אָמַ֤ר יְהוָה֙ אֱלֹהֵ֣י יִשְׂרָאֵ֔ל וְכִסָּ֤ה חָמָס֙ עַל־לְבוּשׁ֔וֹ אָמַ֖ר יְהוָ֣ה צְבָא֑וֹת וְנִשְׁמַרְתֶּ֥ם בְּרוּחֲכֶ֖ם וְלֹ֥א תִבְגֹּֽדוּ׃ ס | 16 |
Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.
הוֹגַעְתֶּ֤ם יְהוָה֙ בְּדִבְרֵיכֶ֔ם וַאֲמַרְתֶּ֖ם בַּמָּ֣ה הוֹגָ֑עְנוּ בֶּאֱמָרְכֶ֗ם כָּל־עֹ֨שֵׂה רָ֜ע ט֣וֹב ׀ בְּעֵינֵ֣י יְהוָ֗ה וּבָהֶם֙ ה֣וּא חָפֵ֔ץ א֥וֹ אַיֵּ֖ה אֱלֹהֵ֥י הַמִּשְׁפָּֽט׃ | 17 |
Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu. Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?” Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”