< אִיּוֹב 10 >
נָֽקְטָ֥ה נַפְשִׁ֗י בְּחַ֫יָּ֥י אֶֽעֶזְבָ֣ה עָלַ֣י שִׂיחִ֑י אֲ֝דַבְּרָה֗ בְּמַ֣ר נַפְשִֽׁי׃ | 1 |
“Ine ndatopa nawo moyo wanga; choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.
אֹמַ֣ר אֶל־אֱ֭לוֹהַּ אַל־תַּרְשִׁיעֵ֑נִי הֽ֝וֹדִיעֵ֗נִי עַ֣ל מַה־תְּרִיבֵֽנִי׃ | 2 |
Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa, koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.
הֲט֤וֹב לְךָ֨ ׀ כִּֽי־תַעֲשֹׁ֗ק כִּֽי־תִ֭מְאַס יְגִ֣יעַ כַּפֶּ֑יךָ וְעַל־עֲצַ֖ת רְשָׁעִ֣ים הוֹפָֽעְתָּ׃ | 3 |
Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?
הַעֵינֵ֣י בָשָׂ֣ר לָ֑ךְ אִם־כִּרְא֖וֹת אֱנ֣וֹשׁ תִּרְאֶֽה׃ | 4 |
Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?
הֲכִימֵ֣י אֱנ֣וֹשׁ יָמֶ֑יךָ אִם־שְׁ֝נוֹתֶ֗יךָ כִּ֣ימֵי גָֽבֶר׃ | 5 |
Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu, kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,
כִּֽי־תְבַקֵּ֥שׁ לַעֲוֹנִ֑י וּ֭לְחַטָּאתִ֥י תִדְרֽוֹשׁ׃ | 6 |
kuti Inu mufufuze zolakwa zanga ndi kulondola tchimo langa,
עַֽל־דַּ֭עְתְּךָ כִּי־לֹ֣א אֶרְשָׁ֑ע וְאֵ֖ין מִיָּדְךָ֣ מַצִּֽיל׃ | 7 |
ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?
יָדֶ֣יךָ עִ֭צְּבוּנִי וַֽיַּעֲשׂ֑וּנִי יַ֥חַד סָ֝בִ֗יב וַֽתְּבַלְּעֵֽנִי׃ | 8 |
“Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?
זְכָר־נָ֭א כִּי־כַחֹ֣מֶר עֲשִׂיתָ֑נִי וְֽאֶל־עָפָ֥ר תְּשִׁיבֵֽנִי׃ | 9 |
Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
הֲלֹ֣א כֶ֭חָלָב תַּתִּיכֵ֑נִי וְ֝כַגְּבִנָּ֗ה תַּקְפִּיאֵֽנִי׃ | 10 |
Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?
ע֣וֹר וּ֭בָשָׂר תַּלְבִּישֵׁ֑נִי וּֽבַעֲצָמ֥וֹת וְ֝גִידִ֗ים תְּסֹכְכֵֽנִי׃ | 11 |
Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?
חַיִּ֣ים וָ֭חֶסֶד עָשִׂ֣יתָ עִמָּדִ֑י וּ֝פְקֻדָּתְךָ֗ שָֽׁמְרָ֥ה רוּחִֽי׃ | 12 |
Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu, ndipo munasamalira bwino moyo wanga.
וְ֭אֵלֶּה צָפַ֣נְתָּ בִלְבָבֶ֑ךָ יָ֝דַ֗עְתִּי כִּי־זֹ֥את עִמָּֽךְ׃ | 13 |
“Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu, ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:
אִם־חָטָ֥אתִי וּשְׁמַרְתָּ֑נִי וּ֝מֵעֲוֹנִ֗י לֹ֣א תְנַקֵּֽנִי׃ | 14 |
Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.
אִם־רָשַׁ֡עְתִּי אַלְלַ֬י לִ֗י וְ֭צָדַקְתִּי לֹא־אֶשָּׂ֣א רֹאשִׁ֑י שְׂבַ֥ע קָ֝ל֗וֹן וּרְאֵ֥ה עָנְיִֽי׃ | 15 |
Ngati ndili wolakwa, tsoka langa! Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga, pakuti ndagwidwa ndi manyazi ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.
וְ֭יִגְאֶה כַּשַּׁ֣חַל תְּצוּדֵ֑נִי וְ֝תָשֹׁ֗ב תִּתְפַּלָּא־בִֽי׃ | 16 |
Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.
תְּחַדֵּ֬שׁ עֵדֶ֨יךָ ׀ נֶגְדִּ֗י וְתֶ֣רֶב כַּֽ֭עַשְׂךָ עִמָּדִ֑י חֲלִיפ֖וֹת וְצָבָ֣א עִמִּֽי׃ | 17 |
Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.
וְלָ֣מָּה מֵ֭רֶחֶם הֹצֵאתָ֑נִי אֶ֝גְוַ֗ע וְעַ֣יִן לֹא־תִרְאֵֽנִי׃ | 18 |
“Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe? Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.
כַּאֲשֶׁ֣ר לֹא־הָיִ֣יתִי אֶהְיֶ֑ה מִ֝בֶּ֗טֶן לַקֶּ֥בֶר אוּבָֽל׃ | 19 |
Ndikanapanda kubadwa, kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!
הֲלֹא־מְעַ֣ט יָמַ֣י וַחֲדָ֑ל וְשִׁ֥ית מִ֝מֶּ֗נִּי וְאַבְלִ֥יגָה מְּעָֽט׃ | 20 |
Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha? Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha
בְּטֶ֣רֶם אֵ֭לֵךְ וְלֹ֣א אָשׁ֑וּב אֶל־אֶ֖רֶץ חֹ֣שֶׁךְ וְצַלְמָֽוֶת׃ | 21 |
ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,
אֶ֤רֶץ עֵיפָ֨תָה ׀ כְּמ֥וֹ אֹ֗פֶל צַ֭לְמָוֶת וְלֹ֥א סְדָרִ֗ים וַתֹּ֥פַע כְּמוֹ־אֹֽפֶל׃ פ | 22 |
ku dziko la mdima wandiweyani ndi chisokonezo, kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”