< דָּנִיֵּאל 11 >

וַאֲנִי֙ בִּשְׁנַ֣ת אַחַ֔ת לְדָרְיָ֖וֶשׁ הַמָּדִ֑י עָמְדִ֛י לְמַחֲזִ֥יק וּלְמָע֖וֹז לֽוֹ׃ 1
Ndipo chaka choyamba cha Dariyo Mmedi ine Mikayeli ndinabwera kumuthandiza ndi kumuteteza Gabrieli.
וְעַתָּ֕ה אֱמֶ֖ת אַגִּ֣יד לָ֑ךְ הִנֵּה־עוֹד֩ שְׁלֹשָׁ֨ה מְלָכִ֜ים עֹמְדִ֣ים לְפָרַ֗ס וְהָֽרְבִיעִי֙ יַעֲשִׁ֤יר עֹֽשֶׁר־גָּדוֹל֙ מִכֹּ֔ל וּכְחֶזְקָת֣וֹ בְעָשְׁר֔וֹ יָעִ֣יר הַכֹּ֔ל אֵ֖ת מַלְכ֥וּת יָוָֽן׃ 2
“Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi.
וְעָמַ֖ד מֶ֣לֶךְ גִּבּ֑וֹר וּמָשַׁל֙ מִמְשָׁ֣ל רַ֔ב וְעָשָׂ֖ה כִּרְצוֹנֽוֹ׃ 3
Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna.
וּכְעָמְדוֹ֙ תִּשָּׁבֵ֣ר מַלְכוּת֔וֹ וְתֵחָ֕ץ לְאַרְבַּ֖ע רוּח֣וֹת הַשָּׁמָ֑יִם וְלֹ֣א לְאַחֲרִית֗וֹ וְלֹ֤א כְמָשְׁלוֹ֙ אֲשֶׁ֣ר מָשָׁ֔ל כִּ֤י תִנָּתֵשׁ֙ מַלְכוּת֔וֹ וְלַאֲחֵרִ֖ים מִלְּבַד־אֵֽלֶּה׃ 4
Koma ufumu wake ukadzafika pachimake, udzawonongedwa ndi kugawidwa mʼzigawo zinayi. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa zidzukulu zake, ndipo olowa mʼmalo mwake sadzakhala ndi mphamvu monga anali nazo, chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.
וְיֶחֱזַ֥ק מֶֽלֶךְ־הַנֶּ֖גֶב וּמִן־שָׂרָ֑יו וְיֶחֱזַ֤ק עָלָיו֙ וּמָשָׁ֔ל מִמְשָׁ֥ל רַ֖ב מֶמְשַׁלְתּֽוֹ׃ 5
“Mfumu ya kummwera idzakhala yamphamvu, koma mmodzi mwa akalonga ake adzakhala ndi mphamvu kuposa iyo; adzalamulira ufumu wake waukulu kwambiri.
וּלְקֵ֤ץ שָׁנִים֙ יִתְחַבָּ֔רוּ וּבַ֣ת מֶֽלֶךְ־הַנֶּ֗גֶב תָּבוֹא֙ אֶל־מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֔וֹן לַעֲשׂ֖וֹת מֵישָׁרִ֑ים וְלֹֽא־תַעְצֹ֞ר כּ֣וֹחַ הַזְּר֗וֹעַ וְלֹ֤א יַעֲמֹד֙ וּזְרֹע֔וֹ וְתִנָּתֵ֨ן הִ֤יא וּמְבִיאֶ֙יהָ֙ וְהַיֹּ֣לְדָ֔הּ וּמַחֲזִקָ֖הּ בָּעִתִּֽים׃ 6
Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani.
וְעָמַ֛ד מִנֵּ֥צֶר שָׁרָשֶׁ֖יהָ כַּנּ֑וֹ וְיָבֹ֣א אֶל־הַחַ֗יִל וְיָבֹא֙ בְּמָעוֹז֙ מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֔וֹן וְעָשָׂ֥ה בָהֶ֖ם וְהֶחֱזִֽיק׃ 7
“Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana.
וְגַ֣ם אֱֽלֹהֵיהֶ֡ם עִם־נְסִֽכֵיהֶם֩ עִם־כְּלֵ֨י חֶמְדָּתָ֜ם כֶּ֧סֶף וְזָהָ֛ב בַּשְּׁבִ֖י יָבִ֣א מִצְרָ֑יִם וְהוּא֙ שָׁנִ֣ים יַעֲמֹ֔ד מִמֶּ֖לֶךְ הַצָּפֽוֹן׃ 8
Iye adzalandanso milungu yawo, mafano awo achitsulo, ndi ziwiya zawo zamtengowapatali zasiliva ndi golide ndi kubwerera nazo ku Igupto. Adzaleka osayithira nkhondo mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo.
וּבָ֗א בְּמַלְכוּת֙ מֶ֣לֶךְ הַנֶּ֔גֶב וְשָׁ֖ב אֶל־אַדְמָתֽוֹ׃ 9
Kenaka mfumu ya kumpoto idzathira nkhondo dziko la mfumu ya kummwera koma idzalephera ndi kubwerera kwawo.
וּבָנָ֣יו יִתְגָּר֗וּ וְאָסְפוּ֙ הֲמוֹן֙ חֲיָלִ֣ים רַבִּ֔ים וּבָ֥א ב֖וֹא וְשָׁטַ֣ף וְעָבָ֑ר וְיָשֹׁ֥ב וְיִתְגָּרֶ֖ה עַד־מָעֻזּֽוֹ׃ 10
Ana ake adzakonzekera nkhondo ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, limene lidzathira nkhondo mfumu yakummwera ngati chigumula mpaka kumalo ake otetezedwa.
וְיִתְמַרְמַר֙ מֶ֣לֶךְ הַנֶּ֔גֶב וְיָצָ֕א וְנִלְחַ֥ם עִמּ֖וֹ עִם־מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֑וֹן וְהֶעֱמִיד֙ הָמ֣וֹן רָ֔ב וְנִתַּ֥ן הֶהָמ֖וֹן בְּיָדֽוֹ׃ 11
“Kenaka mfumu yakummwera idzatuluka mokwiya ndi kumenya nkhondo ndi mfumu yakumpoto, imene idzasonkhanitsa gulu lalikulu la nkhondo, koma idzayigonjetsa.
וְנִשָּׂ֥א הֶהָמ֖וֹן וְרָ֣ם לְבָב֑וֹ וְהִפִּ֛יל רִבֹּא֖וֹת וְלֹ֥א יָעֽוֹז׃ 12
Gulu la nkhondoli likadzagwidwa, mfumu yakummwera idzayamba kudzikuza ndipo idzapha anthu miyandamiyanda, koma kupambanaku sikudzapitirira.
וְשָׁב֙ מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֔וֹן וְהֶעֱמִ֣יד הָמ֔וֹן רַ֖ב מִן־הָרִאשׁ֑וֹן וּלְקֵ֨ץ הָֽעִתִּ֤ים שָׁנִים֙ יָ֣בוֹא ב֔וֹא בְּחַ֥יִל גָּד֖וֹל וּבִרְכ֥וּשׁ רָֽב׃ 13
Popeza mfumu ya kumpoto idzasonkhanitsa gulu lina lankhondo, lochulukirapo kuposa loyamba; ndipo patapita zaka zingapo idzabwera ndi chigulu chachikulu cha nkhondo chokonzekeratu ndi zida.
וּבָעִתִּ֣ים הָהֵ֔ם רַבִּ֥ים יַֽעַמְד֖וּ עַל־מֶ֣לֶךְ הַנֶּ֑גֶב וּבְנֵ֣י ׀ פָּרִיצֵ֣י עַמְּךָ֗ יִֽנַּשְּׂא֛וּ לְהַעֲמִ֥יד חָז֖וֹן וְנִכְשָֽׁלוּ׃ 14
“Nthawi imeneyo ambiri adzawukira mfumu ya kummwera. Anthu achisokonezo pakati panu nawonso adzawukira pokwaniritsa masomphenya, koma sadzapambana.
וְיָבֹא֙ מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֔וֹן וְיִשְׁפֹּךְ֙ סֽוֹלֲלָ֔ה וְלָכַ֖ד עִ֣יר מִבְצָר֑וֹת וּזְרֹע֤וֹת הַנֶּ֙גֶב֙ לֹ֣א יַעֲמֹ֔דוּ וְעַם֙ מִבְחָרָ֔יו וְאֵ֥ין כֹּ֖חַ לַעֲמֹֽד׃ 15
Kenaka mfumu ya kumpoto idzafika ndikuzinga mzinda powunda nthumbira za nkhondo ndipo idzagonjetsa mzinda wotetezedwa. Gulu lankhondo la kummwera lidzasowa mphamvu; ngakhale akatswiri awo ankhondo sadzakhala ndi mphamvu zogonjetsera ankhondo a kumpoto.
וְיַ֨עַשׂ הַבָּ֤א אֵלָיו֙ כִּרְצוֹנ֔וֹ וְאֵ֥ין עוֹמֵ֖ד לְפָנָ֑יו וְיַעֲמֹ֥ד בְּאֶֽרֶץ־הַצְּבִ֖י וְכָלָ֥ה בְיָדֽוֹ׃ 16
Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija.
וְיָשֵׂ֣ם ׀ פָּ֠נָיו לָב֞וֹא בְּתֹ֧קֶף כָּל־מַלְכוּת֛וֹ וִישָׁרִ֥ים עִמּ֖וֹ וְעָשָׂ֑ה וּבַ֤ת הַנָּשִׁים֙ יִתֶּן־ל֣וֹ לְהַשְׁחִיתָ֔הּ וְלֹ֥א תַעֲמֹ֖ד וְלֹא־ל֥וֹ תִהְיֶֽה׃ 17
Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza.
וְיָשֵׂ֧ם פָּנָ֛יו לְאִיִּ֖ים וְלָכַ֣ד רַבִּ֑ים וְהִשְׁבִּ֨ית קָצִ֤ין חֶרְפָּתוֹ֙ ל֔וֹ בִּלְתִּ֥י חֶרְפָּת֖וֹ יָשִׁ֥יב לֽוֹ׃ 18
Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye.
וְיָשֵׁ֣ב פָּנָ֔יו לְמָעוּזֵּ֖י אַרְצ֑וֹ וְנִכְשַׁ֥ל וְנָפַ֖ל וְלֹ֥א יִמָּצֵֽא׃ 19
Zikadzatha izi, mfumu idzabwerera ku malo otetezedwa a dziko la kwawo koma idzapunthwa ndi kugwa osapezekanso.
וְעָמַ֧ד עַל־כַּנּ֛וֹ מַעֲבִ֥יר נוֹגֵ֖שׂ הֶ֣דֶר מַלְכ֑וּת וּבְיָמִ֤ים אֲחָדִים֙ יִשָּׁבֵ֔ר וְלֹ֥א בְאַפַּ֖יִם וְלֹ֥א בְמִלְחָמָֽה׃ 20
“Mfumu imene idzatenga malo ake idzatumiza wokhometsa msonkho kuti chuma cha ufumu wake chichuluke. Komabe mʼzaka zochepa mfumuyo idzawonongedwa osati mu mkwiyo kapena ku nkhondo.
וְעָמַ֤ד עַל־כַּנּוֹ֙ נִבְזֶ֔ה וְלֹא־נָתְנ֥וּ עָלָ֖יו ה֣וֹד מַלְכ֑וּת וּבָ֣א בְשַׁלְוָ֔ה וְהֶחֱזִ֥יק מַלְכ֖וּת בַּחֲלַקְלַקּֽוֹת׃ 21
“Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo.
וּזְרֹע֥וֹת הַשֶּׁ֛טֶף יִשָּׁטְפ֥וּ מִלְּפָנָ֖יו וְיִשָּׁבֵ֑רוּ וְגַ֖ם נְגִ֥יד בְּרִֽית׃ 22
Kenaka adzagonetsa gulu lalikulu lankhondo kuphatikizapo Mkulu wa Ansembe wapangano.
וּמִן־הִֽתְחַבְּר֥וּת אֵלָ֖יו יַעֲשֶׂ֣ה מִרְמָ֑ה וְעָלָ֥ה וְעָצַ֖ם בִּמְעַט־גּֽוֹי׃ 23
Atatha kuchita naye pangano, iye adzachita monyenga, ndipo ngakhale adzakhale ndi anthu ochepa adzakhalabe ndi mphamvu.
בְּשַׁלְוָ֞ה וּבְמִשְׁמַנֵּ֣י מְדִינָה֮ יָבוֹא֒ וְעָשָׂ֗ה אֲשֶׁ֨ר לֹא־עָשׂ֤וּ אֲבֹתָיו֙ וַאֲב֣וֹת אֲבֹתָ֔יו בִּזָּ֧ה וְשָׁלָ֛ל וּרְכ֖וּשׁ לָהֶ֣ם יִבְז֑וֹר וְעַ֧ל מִבְצָרִ֛ים יְחַשֵּׁ֥ב מַחְשְׁבֹתָ֖יו וְעַד־עֵֽת׃ 24
Mwadzidzidzi, iye adzazithira nkhondo zigawo zolemera kwambiri ndipo adzachita zimene makolo ake ngakhale agogo ake sanachitepo. Iye adzagawira zolanda, zofunkha ndi chuma kwa omutsatira. Adzachita chiwembu cholanda mizinda yotetezedwa koma kwa kanthawi kochepa.
וְיָעֵר֩ כֹּח֨וֹ וּלְבָב֜וֹ עַל־מֶ֣לֶךְ הַנֶּגֶב֮ בְּחַ֣יִל גָּדוֹל֒ וּמֶ֣לֶךְ הַנֶּ֗גֶב יִתְגָּרֶה֙ לַמִּלְחָמָ֔ה בְּחַֽיִל־גָּד֥וֹל וְעָצ֖וּם עַד־מְאֹ֑ד וְלֹ֣א יַעֲמֹ֔ד כִּֽי־יַחְשְׁב֥וּ עָלָ֖יו מַחֲשָׁבֽוֹת׃ 25
“Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera.
וְאֹכְלֵ֧י פַת־בָּג֛וֹ יִשְׁבְּר֖וּהוּ וְחֵיל֣וֹ יִשְׁט֑וֹף וְנָפְל֖וּ חֲלָלִ֥ים רַבִּֽים׃ 26
Amene amadya chakudya ndi mfumu adzamuukira; gulu lake lankhondo lidzagonjetsedwa, ndipo ambiri adzafera ku nkhondo.
וּשְׁנֵיהֶ֤ם הַמְּלָכִים֙ לְבָבָ֣ם לְמֵרָ֔ע וְעַל־שֻׁלְחָ֥ן אֶחָ֖ד כָּזָ֣ב יְדַבֵּ֑רוּ וְלֹ֣א תִצְלָ֔ח כִּי־ע֥וֹד קֵ֖ץ לַמּוֹעֵֽד׃ 27
Mafumu awiriwa mitima yawo idzalinga ku zoyipa. Azidzanamizana ali pa tebulo limodzi, koma zolinga zawo sizidzatheka chifukwa nthawi idzakhala isanakwane.
וְיָשֹׁ֤ב אַרְצוֹ֙ בִּרְכ֣וּשׁ גָּד֔וֹל וּלְבָב֖וֹ עַל־בְּרִ֣ית קֹ֑דֶשׁ וְעָשָׂ֖ה וְשָׁ֥ב לְאַרְצֽוֹ׃ 28
Mfumu ya kumpoto idzabwerera ku dziko la kwawo ndi chuma chambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa pangano lopatulika. Idzawononga panganolo ndipo kenaka idzabwerera ku dziko lake.
לַמּוֹעֵ֥ד יָשׁ֖וּב וּבָ֣א בַנֶּ֑גֶב וְלֹֽא־תִהְיֶ֥ה כָרִאשֹׁנָ֖ה וְכָאַחֲרֹנָֽה׃ 29
“Patapita nthawi mfumu ya kumpoto idzabwereranso kummwera koma sidzapambana monga inachitira kale.
וּבָ֨אוּ ב֜וֹ צִיִּ֤ים כִּתִּים֙ וְנִכְאָ֔ה וְשָׁ֛ב וְזָעַ֥ם עַל־בְּרִֽית־ק֖וֹדֶשׁ וְעָשָׂ֑ה וְשָׁ֣ב וְיָבֵ֔ן עַל־עֹזְבֵ֖י בְּרִ֥ית קֹֽדֶשׁ׃ 30
Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera.
וּזְרֹעִ֖ים מִמֶּ֣נּוּ יַעֲמֹ֑דוּ וְחִלְּל֞וּ הַמִּקְדָּ֤שׁ הַמָּעוֹז֙ וְהֵסִ֣ירוּ הַתָּמִ֔יד וְנָתְנ֖וּ הַשִּׁקּ֥וּץ מְשׁוֹמֵֽם׃ 31
“Ankhondo ake adzayipitsa linga la Nyumba ya Mulungu ndipo adzathetsa nsembe za tsiku ndi tsiku. Kenaka adzakhazikitsa chonyansa chimene chabweretsa chiwonongeko.
וּמַרְשִׁיעֵ֣י בְרִ֔ית יַחֲנִ֖יף בַּחֲלַקּ֑וֹת וְעַ֛ם יֹדְעֵ֥י אֱלֹהָ֖יו יַחֲזִ֥קוּ וְעָשֽׂוּ׃ 32
Ndi mawu oshashalika mfumuyo idzakopa amene anaphwanya pangano, koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzalimbika ndipo adzayikana mfumuyo kwathunthu.
וּמַשְׂכִּ֣ילֵי עָ֔ם יָבִ֖ינוּ לָֽרַבִּ֑ים וְנִכְשְׁל֞וּ בְּחֶ֧רֶב וּבְלֶהָבָ֛ה בִּשְׁבִ֥י וּבְבִזָּ֖ה יָמִֽים׃ 33
“Amene ndi anzeru adzalangiza ambiri. Koma patapita kanthawi adzaphedwa ndi lupanga kapena kutenthedwa, kapena kugwidwa kapena kulandidwa katundu.
וּבְהִכָּ֣שְׁלָ֔ם יֵעָזְר֖וּ עֵ֣זֶר מְעָ֑ט וְנִלְו֧וּ עֲלֵיהֶ֛ם רַבִּ֖ים בַּחֲלַקְלַקּֽוֹת׃ 34
Pa nthawi yozunzikayi ena adzawathandiza pangʼono, koma ambiri othandizawo adzakhala achinyengo.
וּמִן־הַמַּשְׂכִּילִ֣ים יִכָּֽשְׁל֗וּ לִצְר֥וֹף בָּהֶ֛ם וּלְבָרֵ֥ר וְלַלְבֵּ֖ן עַד־עֵ֣ת קֵ֑ץ כִּי־ע֖וֹד לַמּוֹעֵֽד׃ 35
Ena mwa anzeruwo adzaphedwa ndi cholinga chakuti ayengedwe, otsala mwa iwo ayeretsedwe ndi kukhala wopanda banga kufikira nthawi yomaliza, popeza idzafika ndithu nthawi imene Mulungu wayika.
וְעָשָׂ֨ה כִרְצוֹנ֜וֹ הַמֶּ֗לֶךְ וְיִתְרוֹמֵ֤ם וְיִתְגַּדֵּל֙ עַל־כָּל־אֵ֔ל וְעַל֙ אֵ֣ל אֵלִ֔ים יְדַבֵּ֖ר נִפְלָא֑וֹת וְהִצְלִ֙יחַ֙ עַד־כָּ֣לָה זַ֔עַם כִּ֥י נֶחֱרָצָ֖ה נֶעֱשָֽׂתָה׃ 36
“Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika.
וְעַל־אֱלֹהֵ֤י אֲבֹתָיו֙ לֹ֣א יָבִ֔ין וְעַל־חֶמְדַּ֥ת נָשִׁ֛ים וְעַֽל־כָּל־אֱל֖וֹהַּ לֹ֣א יָבִ֑ין כִּ֥י עַל־כֹּ֖ל יִתְגַּדָּֽל׃ 37
Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse.
וְלֶאֱלֹ֙הַּ֙ מָֽעֻזִּ֔ים עַל־כַּנּ֖וֹ יְכַבֵּ֑ד וְלֶאֱל֜וֹהַּ אֲשֶׁ֧ר לֹא־יְדָעֻ֣הוּ אֲבֹתָ֗יו יְכַבֵּ֛ד בְּזָהָ֥ב וּבְכֶ֛סֶף וּבְאֶ֥בֶן יְקָרָ֖ה וּבַחֲמֻדֽוֹת׃ 38
Mʼmalo mwa onsewo, idzachitira ulemu mulungu wachitetezo; mulungu wosadziwika ndi makolo ake. Iyo idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, ndi miyala yokongola, ndiponso mphatso za pamwamba kwambiri.
וְעָשָׂ֞ה לְמִבְצְרֵ֤י מָֽעֻזִּים֙ עִם־אֱל֣וֹהַּ נֵכָ֔ר אֲשֶׁ֥ר יַכִּ֖יר יַרְבֶּ֣ה כָב֑וֹד וְהִמְשִׁילָם֙ בָּֽרַבִּ֔ים וַאֲדָמָ֖ה יְחַלֵּ֥ק בִּמְחִֽיר׃ 39
Anthu opembedza mulungu wachilendo adzakhala ngati linga lake. Idzalemekeza iwowa kwambiri, ndipo idzawayika kuti alamulire anthu ambiri. Idzawagawira dziko ngati malipiro awo.
וּבְעֵ֣ת קֵ֗ץ יִתְנַגַּ֤ח עִמּוֹ֙ מֶ֣לֶךְ הַנֶּ֔גֶב וְיִשְׂתָּעֵ֨ר עָלָ֜יו מֶ֣לֶךְ הַצָּפ֗וֹן בְּרֶ֙כֶב֙ וּבְפָ֣רָשִׁ֔ים וּבָאֳנִיּ֖וֹת רַבּ֑וֹת וּבָ֥א בַאֲרָצ֖וֹת וְשָׁטַ֥ף וְעָבָֽר׃ 40
“Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira.
וּבָא֙ בְּאֶ֣רֶץ הַצְּבִ֔י וְרַבּ֖וֹת יִכָּשֵׁ֑לוּ וְאֵ֙לֶּה֙ יִמָּלְט֣וּ מִיָּד֔וֹ אֱד֣וֹם וּמוֹאָ֔ב וְרֵאשִׁ֖ית בְּנֵ֥י עַמּֽוֹן׃ 41
Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka.
וְיִשְׁלַ֥ח יָד֖וֹ בַּאֲרָצ֑וֹת וְאֶ֣רֶץ מִצְרַ֔יִם לֹ֥א תִהְיֶ֖ה לִפְלֵיטָֽה׃ 42
Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka.
וּמָשַׁ֗ל בְּמִכְמַנֵּי֙ הַזָּהָ֣ב וְהַכֶּ֔סֶף וּבְכֹ֖ל חֲמֻד֣וֹת מִצְרָ֑יִם וְלֻבִ֥ים וְכֻשִׁ֖ים בְּמִצְעָדָֽיו׃ 43
Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo.
וּשְׁמֻע֣וֹת יְבַהֲלֻ֔הוּ מִמִּזְרָ֖ח וּמִצָּפ֑וֹן וְיָצָא֙ בְּחֵמָ֣א גְדֹלָ֔ה לְהַשְׁמִ֥יד וּֽלְהַחֲרִ֖ים רַבִּֽים׃ 44
Koma uthenga wochokera kummawa ndi kumpoto udzayiopsa, ndipo idzapita ndi ukali kukawononga ndi kutheratu anthu ambiri.
וְיִטַּע֙ אָהֳלֶ֣י אַפַּדְנ֔וֹ בֵּ֥ין יַמִּ֖ים לְהַר־צְבִי־קֹ֑דֶשׁ וּבָא֙ עַד־קִצּ֔וֹ וְאֵ֥ין עוֹזֵ֖ר לֽוֹ׃ 45
Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”

< דָּנִיֵּאל 11 >