< תְהִלִּים 131 >

שִׁ֥יר הַֽמַּֽעֲלֹ֗ות לְדָ֫וִ֥ד יְהוָ֤ה ׀ לֹא־גָבַ֣הּ לִ֭בִּי וְלֹא־רָמ֣וּ עֵינַ֑י וְלֹֽא־הִלַּ֓כְתִּי ׀ בִּגְדֹלֹ֖ות וּבְנִפְלָאֹ֣ות מִמֶּֽנִּי׃ 1
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide. Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza, maso anga siwonyada; sinditengeteka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
אִם־לֹ֤א שִׁוִּ֨יתִי ׀ וְדֹומַ֗מְתִּי נַ֫פְשִׁ֥י כְּ֭גָמֻל עֲלֵ֣י אִמֹּ֑ו כַּגָּמֻ֖ל עָלַ֣י נַפְשִֽׁי׃ 2
Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.
יַחֵ֣ל יִ֝שְׂרָאֵל אֶל־יְהוָ֑ה מֵֽ֝עַתָּ֗ה וְעַד־עֹולָֽם׃ 3
Yembekeza Yehova, iwe Israeli, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

< תְהִלִּים 131 >