< אֵיכָה 3 >
אֲנִ֤י הַגֶּ֙בֶר֙ רָאָ֣ה עֳנִ֔י בְּשֵׁ֖בֶט עֶבְרָתֹֽו׃ | 1 |
Ine ndine munthu amene ndaona masautso ndi ndodo ya ukali wake.
אֹותִ֥י נָהַ֛ג וַיֹּלַ֖ךְ חֹ֥שֶׁךְ וְלֹא־אֹֽור׃ | 2 |
Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa mu mdima osati mʼkuwala;
אַ֣ךְ בִּ֥י יָשֻׁ֛ב יַהֲפֹ֥ךְ יָדֹ֖ו כָּל־הַיֹּֽום׃ ס | 3 |
zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.
בִּלָּ֤ה בְשָׂרִי֙ וְעֹורִ֔י שִׁבַּ֖ר עַצְמֹותָֽי׃ | 4 |
Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo waphwanya mafupa anga.
בָּנָ֥ה עָלַ֛י וַיַּקַּ֖ף רֹ֥אשׁ וּתְלָאָֽה׃ | 5 |
Wandizinga ndi kundizungulira ndi zowawa ndi zolemetsa.
בְּמַחֲשַׁכִּ֥ים הֹושִׁיבַ֖נִי כְּמֵתֵ֥י עֹולָֽם׃ ס | 6 |
Wandikhazika mu mdima ngati amene anafa kale.
גָּדַ֧ר בַּעֲדִ֛י וְלֹ֥א אֵצֵ֖א הִכְבִּ֥יד נְחָשְׁתִּֽי׃ | 7 |
Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe, wandimanga ndi maunyolo.
גַּ֣ם כִּ֤י אֶזְעַק֙ וַאֲשַׁוֵּ֔עַ שָׂתַ֖ם תְּפִלָּתִֽי׃ | 8 |
Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo, amakana pemphero langa.
גָּדַ֤ר דְּרָכַי֙ בְּגָזִ֔ית נְתִיבֹתַ֖י עִוָּֽה׃ ס | 9 |
Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema; ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
דֹּ֣ב אֹרֵ֥ב הוּא֙ לִ֔י אַרְיֵה (אֲרִ֖י) בְּמִסְתָּרִֽים׃ | 10 |
Wandidikirira ngati chimbalangondo, wandibisalira ngati mkango.
דְּרָכַ֥י סֹורֵ֛ר וַֽיְפַשְּׁחֵ֖נִי שָׂמַ֥נִי שֹׁמֵֽם׃ | 11 |
Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba, ndipo wandisiya wopanda thandizo.
דָּרַ֤ךְ קַשְׁתֹּו֙ וַיַּצִּיבֵ֔נִי כַּמַּטָּרָ֖א לַחֵֽץ׃ ס | 12 |
Wakoka uta wake ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
הֵבִיא֙ בְּכִלְיֹותָ֔י בְּנֵ֖י אַשְׁפָּתֹֽו׃ | 13 |
Walasa mtima wanga ndi mivi ya mʼphodo mwake.
הָיִ֤יתִי שְּׂחֹק֙ לְכָל־עַמִּ֔י נְגִינָתָ֖ם כָּל־הַיֹּֽום׃ | 14 |
Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse; amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.
הִשְׂבִּיעַ֥נִי בַמְּרֹורִ֖ים הִרְוַ֥נִי לַעֲנָֽה׃ ס | 15 |
Wandidyetsa zowawa ndipo wandimwetsa ndulu.
וַיַּגְרֵ֤ס בֶּֽחָצָץ֙ שִׁנָּ֔י הִכְפִּישַׁ֖נִי בָּאֵֽפֶר׃ | 16 |
Wathyola mano anga ndi miyala; wandiviviniza mʼfumbi;
וַתִּזְנַ֧ח מִשָּׁלֹ֛ום נַפְשִׁ֖י נָשִׁ֥יתִי טֹובָֽה׃ | 17 |
Wandichotsera mtendere; ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.
וָאֹמַר֙ אָבַ֣ד נִצְחִ֔י וְתֹוחַלְתִּ֖י מֵיְהוָֽה׃ ס | 18 |
Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”
זְכָר־עָנְיִ֥י וּמְרוּדִ֖י לַעֲנָ֥ה וָרֹֽאשׁ׃ | 19 |
Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala, zili ngati zowawa ndi ndulu.
זָכֹ֣ור תִּזְכֹּ֔ור וְתָשִׁיחַ (וְתָשֹׁ֥וחַ) עָלַ֖י נַפְשִֽׁי׃ | 20 |
Ine ndikuzikumbukira bwino izi, ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
זֹ֛את אָשִׁ֥יב אֶל־לִבִּ֖י עַל־כֵּ֥ן אֹוחִֽיל׃ ס | 21 |
Komabe ndimakumbukira zimenezi, nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
חַֽסְדֵ֤י יְהוָה֙ כִּ֣י לֹא־תָ֔מְנוּ כִּ֥י לֹא־כָל֖וּ רַחֲמָֽיו׃ | 22 |
Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha.
חֲדָשִׁים֙ לַבְּקָרִ֔ים רַבָּ֖ה אֱמוּנָתֶֽךָ׃ | 23 |
Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
חֶלְקִ֤י יְהוָה֙ אָמְרָ֣ה נַפְשִׁ֔י עַל־כֵּ֖ן אֹוחִ֥יל לֹֽו׃ ס | 24 |
Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse; motero ndimamuyembekezera.”
טֹ֤וב יְהוָה֙ לְקֹוָ֔ו לְנֶ֖פֶשׁ תִּדְרְשֶֽׁנּוּ׃ | 25 |
Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;
טֹ֤וב וְיָחִיל֙ וְדוּמָ֔ם לִתְשׁוּעַ֖ת יְהוָֽה׃ | 26 |
nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha Yehova modekha.
טֹ֣וב לַגֶּ֔בֶר כִּֽי־יִשָּׂ֥א עֹ֖ל בִּנְעוּרָֽיו׃ ס | 27 |
Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli pamene ali wamngʼono.
יֵשֵׁ֤ב בָּדָד֙ וְיִדֹּ֔ם כִּ֥י נָטַ֖ל עָלָֽיו׃ | 28 |
Akhale chete pa yekha, chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.
יִתֵּ֤ן בֶּֽעָפָר֙ פִּ֔יהוּ אוּלַ֖י יֵ֥שׁ תִּקְוָֽה׃ | 29 |
Abise nkhope yake mʼfumbi mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.
יִתֵּ֧ן לְמַכֵּ֛הוּ לֶ֖חִי יִשְׂבַּ֥ע בְּחֶרְפָּֽה׃ ס | 30 |
Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye, ndipo amuchititse manyazi.
כִּ֣י לֹ֥א יִזְנַ֛ח לְעֹולָ֖ם אֲדֹנָֽי׃ | 31 |
Chifukwa Ambuye satayiratu anthu nthawi zonse.
כִּ֣י אִם־הֹוגָ֔ה וְרִחַ֖ם כְּרֹ֥ב חַסְדֹּו (חֲסָדָֽיו)׃ | 32 |
Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo, chifukwa chikondi chake ndi chosatha.
כִּ֣י לֹ֤א עִנָּה֙ מִלִּבֹּ֔ו וַיַּגֶּ֖ה בְּנֵי־אִֽישׁ׃ ס | 33 |
Pakuti sabweretsa masautso mwadala, kapena zowawa kwa ana a anthu.
לְדַכֵּא֙ תַּ֣חַת רַגְלָ֔יו כֹּ֖ל אֲסִ֥ירֵי אָֽרֶץ׃ | 34 |
Kuphwanya ndi phazi a mʼndende onse a mʼdziko,
לְהַטֹּות֙ מִשְׁפַּט־גָּ֔בֶר נֶ֖גֶד פְּנֵ֥י עֶלְיֹֽון׃ | 35 |
kukaniza munthu ufulu wake pamaso pa Wammwambamwamba,
לְעַוֵּ֤ת אָדָם֙ בְּרִיבֹ֔ו אֲדֹנָ֖י לֹ֥א רָאָֽה׃ ס | 36 |
kumana munthu chiweruzo cholungama— kodi Ambuye saona zonsezi?
מִ֣י זֶ֤ה אָמַר֙ וַתֶּ֔הִי אֲדֹנָ֖י לֹ֥א צִוָּֽה׃ | 37 |
Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika ngati Ambuye sanavomereze?
מִפִּ֤י עֶלְיֹון֙ לֹ֣א תֵצֵ֔א הָרָעֹ֖ות וְהַטֹּֽוב׃ | 38 |
Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?
מַה־יִּתְאֹונֵן֙ אָדָ֣ם חָ֔י גֶּ֖בֶר עַל־חֶטְאֹו (חֲטָאָֽיו)׃ ס | 39 |
Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula akalangidwa chifukwa cha machimo ake?
נַחְפְּשָׂ֤ה דְרָכֵ֙ינוּ֙ וְֽנַחְקֹ֔רָה וְנָשׁ֖וּבָה עַד־יְהוָֽה׃ | 40 |
Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
נִשָּׂ֤א לְבָבֵ֙נוּ֙ אֶל־כַּפָּ֔יִם אֶל־אֵ֖ל בַּשָּׁמָֽיִם׃ | 41 |
Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
נַ֤חְנוּ פָשַׁ֙עְנוּ֙ וּמָרִ֔ינוּ אַתָּ֖ה לֹ֥א סָלָֽחְתָּ׃ ס | 42 |
“Ife tachimwa ndi kuwukira ndipo inu simunakhululuke.
סַכֹּ֤תָה בָאַף֙ וַֽתִּרְדְּפֵ֔נוּ הָרַ֖גְתָּ לֹ֥א חָמָֽלְתָּ׃ | 43 |
“Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo mwatitha mopanda chifundo.
סַכֹּ֤ותָה בֶֽעָנָן֙ לָ֔ךְ מֵעֲבֹ֖ור תְּפִלָּֽה׃ | 44 |
Mwadzikuta mu mtambo kotero mapemphero athu sakukufikani.
סְחִ֧י וּמָאֹ֛וס תְּשִׂימֵ֖נוּ בְּקֶ֥רֶב הָעַמִּֽים׃ ס | 45 |
Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala pakati pa mitundu ya anthu.
פָּצ֥וּ עָלֵ֛ינוּ פִּיהֶ֖ם כָּל־אֹיְבֵֽינוּ׃ | 46 |
“Adani anthu atitsekulira pakamwa.
פַּ֧חַד וָפַ֛חַת הָ֥יָה לָ֖נוּ הַשֵּׁ֥את וְהַשָּֽׁבֶר׃ | 47 |
Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje, tapasuka ndi kuwonongedwa.”
פַּלְגֵי־מַ֙יִם֙ תֵּרַ֣ד עֵינִ֔י עַל־שֶׁ֖בֶר בַּת־עַמִּֽי׃ ס | 48 |
Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe chifukwa anthu anga akuwonongedwa.
עֵינִ֧י נִגְּרָ֛ה וְלֹ֥א תִדְמֶ֖ה מֵאֵ֥ין הֲפֻגֹֽות׃ | 49 |
Misozi idzatsika kosalekeza, ndipo sidzasiya,
עַד־יַשְׁקִ֣יף וְיֵ֔רֶא יְהוָ֖ה מִשָּׁמָֽיִם׃ | 50 |
mpaka Yehova ayangʼane pansi kuchokera kumwamba ndi kuona.
עֵינִי֙ עֹֽולְלָ֣ה לְנַפְשִׁ֔י מִכֹּ֖ל בְּנֹ֥ות עִירִֽי׃ ס | 51 |
Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.
צֹ֥וד צָד֛וּנִי כַּצִּפֹּ֖ור אֹיְבַ֥י חִנָּֽם׃ | 52 |
Akundisaka ngati mbalame, amene anali adani anga, popanda chifukwa.
צָֽמְת֤וּ בַבֹּור֙ חַיָּ֔י וַיַּדּוּ־אֶ֖בֶן בִּֽי׃ | 53 |
Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje ndi kundiponya miyala;
צָֽפוּ־מַ֥יִם עַל־רֹאשִׁ֖י אָמַ֥רְתִּי נִגְזָֽרְתִּי׃ ס | 54 |
madzi anamiza mutu wanga ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.
קָרָ֤אתִי שִׁמְךָ֙ יְהוָ֔ה מִבֹּ֖ור תַּחְתִּיֹּֽות׃ | 55 |
Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova, kuchokera mʼdzenje lozama.
קֹולִ֖י שָׁמָ֑עְתָּ אַל־תַּעְלֵ֧ם אָזְנְךָ֛ לְרַוְחָתִ֖י לְשַׁוְעָתִֽי׃ | 56 |
Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere kulira kwanga kopempha thandizo.”
קָרַ֙בְתָּ֙ בְּיֹ֣ום אֶקְרָאֶ֔ךָּ אָמַ֖רְתָּ אַל־תִּירָֽא׃ ס | 57 |
Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani, ndipo munati, “Usaope.”
רַ֧בְתָּ אֲדֹנָ֛י רִיבֵ֥י נַפְשִׁ֖י גָּאַ֥לְתָּ חַיָּֽי׃ | 58 |
Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga; munapulumutsa moyo wanga.
רָאִ֤יתָה יְהוָה֙ עַוָּ֣תָתִ֔י שָׁפְטָ֖ה מִשְׁפָּטִֽי׃ | 59 |
Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira. Mundiweruzire ndinu!
רָאִ֙יתָה֙ כָּל־נִקְמָתָ֔ם כָּל־מַחְשְׁבֹתָ֖ם לִֽי׃ ס | 60 |
Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine.
שָׁמַ֤עְתָּ חֶרְפָּתָם֙ יְהוָ֔ה כָּל־מַחְשְׁבֹתָ֖ם עָלָֽי׃ | 61 |
Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine,
שִׂפְתֵ֤י קָמַי֙ וְהֶגְיֹונָ֔ם עָלַ֖י כָּל־הַיֹּֽום׃ | 62 |
manongʼonongʼo a adani anga ondiwukira ine tsiku lonse.
שִׁבְתָּ֤ם וְקִֽימָתָם֙ הַבִּ֔יטָה אֲנִ֖י מַנְגִּינָתָֽם׃ ס | 63 |
Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira, akundinyoza mu nyimbo zawo.
תָּשִׁ֨יב לָהֶ֥ם גְּמ֛וּל יְהוָ֖ה כְּמַעֲשֵׂ֥ה יְדֵיהֶֽם׃ | 64 |
Inu Yehova, muwabwezere chowayenera, chifukwa cha zimene manja awo achita.
תִּתֵּ֤ן לָהֶם֙ מְגִנַּת־לֵ֔ב תַּאֲלָֽתְךָ֖ לָהֶֽם׃ | 65 |
Phimbani mitima yawo, ndipo matemberero anu akhale pa iwo!
תִּרְדֹּ֤ף בְּאַף֙ וְתַשְׁמִידֵ֔ם מִתַּ֖חַת שְׁמֵ֥י יְהוָֽה׃ פ | 66 |
Muwalondole mwaukali ndipo muwawonongeretu pa dziko lapansi.