< אִיּוֹב 34 >
וַיַּ֥עַן אֱלִיה֗וּא וַיֹּאמַֽר׃ | 1 |
Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
שִׁמְע֣וּ חֲכָמִ֣ים מִלָּ֑י וְ֝יֹדְעִ֗ים הַאֲזִ֥ינוּ לִֽי׃ | 2 |
“Imvani mawu anga, inu anthu anzeru; tcherani khutu inu anthu ophunzira.
כִּי־אֹ֭זֶן מִלִּ֣ין תִּבְחָ֑ן וְ֝חֵ֗ךְ יִטְעַ֥ם לֶאֱכֹֽל׃ | 3 |
Pakuti khutu limayesa mawu monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
מִשְׁפָּ֥ט נִבְחֲרָה־לָּ֑נוּ נֵדְעָ֖ה בֵינֵ֣ינוּ מַה־טֹּֽוב׃ | 4 |
Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera; tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
כִּֽי־אָ֭מַר אִיֹּ֣וב צָדַ֑קְתִּי וְ֝אֵ֗ל הֵסִ֥יר מִשְׁפָּטִֽי׃ | 5 |
“Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
עַל־מִשְׁפָּטִ֥י אֲכַזֵּ֑ב אָנ֖וּשׁ חִצִּ֣י בְלִי־פָֽשַׁע׃ | 6 |
Ngakhale ndine wolungama mtima, akundiyesa wabodza; ngakhale ndine wosachimwa, mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
מִי־גֶ֥בֶר כְּאִיֹּ֑וב יִֽשְׁתֶּה־לַּ֥עַג כַּמָּֽיִם׃ | 7 |
Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani, amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
וְאָרַ֣ח לְ֭חֶבְרָה עִם־פֹּ֣עֲלֵי אָ֑וֶן וְ֝לָלֶ֗כֶת עִם־אַנְשֵׁי־רֶֽשַׁע׃ | 8 |
Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa; amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
כִּֽי־אָ֭מַר לֹ֣א יִסְכָּן־גָּ֑בֶר בִּ֝רְצֹתֹ֗ו עִם־אֱלֹהִֽים׃ | 9 |
Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
לָכֵ֤ן ׀ אַ֥נֲשֵׁ֥י לֵבָ֗ב שִׁמְע֫וּ לִ֥י חָלִ֖לָה לָאֵ֥ל מֵרֶ֗שַׁע וְשַׁדַּ֥י מֵעָֽוֶל׃ | 10 |
“Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu. Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe, Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
כִּ֤י פֹ֣עַל אָ֭דָם יְשַׁלֶּם־לֹ֑ו וּֽכְאֹ֥רַח אִ֝֗ישׁ יַמְצִאֶֽנּוּ׃ | 11 |
Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake; Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
אַף־אָמְנָ֗ם אֵ֥ל לֹֽא־יַרְשִׁ֑יעַ וְ֝שַׁדַּ֗י לֹֽא־יְעַוֵּ֥ת מִשְׁפָּֽט׃ | 12 |
Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa, kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
מִֽי־פָקַ֣ד עָלָ֣יו אָ֑רְצָה וּמִ֥י שָׂ֝֗ם תֵּבֵ֥ל כֻּלָּֽהּ׃ | 13 |
Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani? Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
אִם־יָשִׂ֣ים אֵלָ֣יו לִבֹּ֑ו רוּחֹ֥ו וְ֝נִשְׁמָתֹ֗ו אֵלָ֥יו יֶאֱסֹֽף׃ | 14 |
Mulungu akanakhala ndi maganizo oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
יִגְוַ֣ע כָּל־בָּשָׂ֣ר יָ֑חַד וְ֝אָדָ֗ם עַל־עָפָ֥ר יָשֽׁוּב׃ | 15 |
zamoyo zonse zikanawonongekeratu ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
וְאִם־בִּ֥ינָה שִׁמְעָה־זֹּ֑את הַ֝אֲזִ֗ינָה לְקֹ֣ול מִלָּֽי׃ | 16 |
“Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi; mvetserani zimene ndikunena.
הַאַ֬ף שֹׂונֵ֣א מִשְׁפָּ֣ט יַחֲבֹ֑ושׁ וְאִם־צַדִּ֖יק כַּבִּ֣יר תַּרְשִֽׁיעַ׃ | 17 |
Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
הַאֲמֹ֣ר לְמֶ֣לֶךְ בְּלִיָּ֑עַל רָ֝שָׁ֗ע אֶל־נְדִיבִֽים׃ | 18 |
Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
אֲשֶׁ֤ר לֹֽא־נָשָׂ֨א ׀ פְּנֵ֥י שָׂרִ֗ים וְלֹ֣א נִכַּר־שֹׁ֖ועַ לִפְנֵי־דָ֑ל כִּֽי־מַעֲשֵׂ֖ה יָדָ֣יו כֻּלָּֽם׃ | 19 |
Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
רֶ֤גַע ׀ יָמֻתוּ֮ וַחֲצֹ֪ות לָ֥יְלָה יְגֹעֲשׁ֣וּ עָ֣ם וְיַעֲבֹ֑רוּ וְיָסִ֥ירוּ אַ֝בִּ֗יר לֹ֣א בְיָֽד׃ | 20 |
Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku; anthu amachita mantha ndipo amamwalira; munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
כִּי־עֵ֭ינָיו עַל־דַּרְכֵי־אִ֑ישׁ וְֽכָל־צְעָדָ֥יו יִרְאֶֽה׃ | 21 |
“Maso a Mulungu amapenya njira za munthu; amaona mayendedwe ake onse.
אֵֽין־חֹ֖שֶׁךְ וְאֵ֣ין צַלְמָ֑וֶת לְהִסָּ֥תֶר שָׁ֝֗ם פֹּ֣עֲלֵי אָֽוֶן׃ | 22 |
Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
כִּ֤י לֹ֣א עַל־אִ֭ישׁ יָשִׂ֣ים עֹ֑וד לַהֲלֹ֥ךְ אֶל־אֵ֝֗ל בַּמִּשְׁפָּֽט׃ | 23 |
Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu, kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
יָרֹ֣עַ כַּבִּירִ֣ים לֹא־חֵ֑קֶר וַיַּעֲמֵ֖ד אֲחֵרִ֣ים תַּחְתָּֽם׃ | 24 |
Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
לָכֵ֗ן יַ֭כִּיר מַעְבָּֽדֵיהֶ֑ם וְהָ֥פַךְ לַ֝֗יְלָה וְיִדַּכָּֽאוּ׃ | 25 |
Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
תַּֽחַת־רְשָׁעִ֥ים סְפָקָ֗ם בִּמְקֹ֥ום רֹאִֽים׃ | 26 |
Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo, pamalo pamene aliyense akuwaona;
אֲשֶׁ֣ר עַל־כֵּ֭ן סָ֣רוּ מֵֽאַחֲרָ֑יו וְכָל־דְּ֝רָכָ֗יו לֹ֣א הִשְׂכִּֽילוּ׃ | 27 |
Chifukwa anasiya kumutsata ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
לְהָבִ֣יא עָ֭לָיו צַֽעֲקַת־דָּ֑ל וְצַעֲקַ֖ת עֲנִיִּ֣ים יִשְׁמָֽע׃ | 28 |
Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake, kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
וְה֤וּא יַשְׁקִ֨ט ׀ וּמִ֥י יַרְשִׁ֗עַ וְיַסְתֵּ֣ר פָּ֭נִים וּמִ֣י יְשׁוּרֶ֑נּוּ וְעַל־גֹּ֖וי וְעַל־אָדָ֣ם יָֽחַד׃ | 29 |
Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe? Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
מִ֭מְּלֹךְ אָדָ֥ם חָנֵ֗ף מִמֹּ֥קְשֵׁי עָֽם׃ | 30 |
kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza, kuti asatchere anthu misampha.
כִּֽי־אֶל־אֵ֭ל הֶאָמַ֥ר נָשָׂ֗אתִי לֹ֣א אֶחְבֹּֽל׃ | 31 |
“Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti, ‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
בִּלְעֲדֵ֣י אֶ֭חֱזֶה אַתָּ֣ה הֹרֵ֑נִי אִֽם־עָ֥וֶל פָּ֝עַ֗לְתִּי לֹ֣א אֹסִֽיף׃ | 32 |
ndiphunzitseni zimene sindikuziona ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
הַֽמֵעִמְּךָ֬ יְשַׁלְמֶ֨נָּה כִּֽי־מָאַ֗סְתָּ כִּי־אַתָּ֣ה תִבְחַ֣ר וְלֹא־אָ֑נִי וּֽמַה־יָדַ֥עְתָּ דַבֵּֽר׃ | 33 |
Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Chisankho nʼchanu, osati changa; tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
אַנְשֵׁ֣י לֵ֭בָב יֹ֣אמְרוּ לִ֑י וְגֶ֥בֶר חָ֝כָ֗ם שֹׁמֵ֥עַֽ לִֽי׃ | 34 |
“Anthu omvetsa zinthu adzakambirana, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
אִ֭יֹּוב לֹא־בְדַ֣עַת יְדַבֵּ֑ר וּ֝דְבָרָ֗יו לֹ֣א בְהַשְׂכֵּֽיל׃ | 35 |
‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru; mawu ake ndi opanda fundo.’
אָבִ֗י יִבָּחֵ֣ן אִיֹּ֣וב עַד־נֶ֑צַח עַל־תְּ֝שֻׁבֹ֗ת בְּאַנְשֵׁי־אָֽוֶן׃ | 36 |
Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
כִּ֥י יֹ֘סִ֤יף עַֽל־חַטָּאתֹ֣ו פֶ֭שַׁע בֵּינֵ֣ינוּ יִסְפֹּ֑וק וְיֶ֖רֶב אֲמָרָ֣יו לָאֵֽל׃ ס | 37 |
Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira; amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu, ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”