< יְשַׁעְיָהוּ 8 >

וַיֹּ֤אמֶר יְהוָה֙ אֵלַ֔י קַח־לְךָ֖ גִּלָּיֹ֣ון גָּדֹ֑ול וּכְתֹ֤ב עָלָיו֙ בְּחֶ֣רֶט אֱנֹ֔ושׁ לְמַהֵ֥ר שָׁלָ֖ל חָ֥שׁ בַּֽז׃ 1
Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.
וְאָעִ֣ידָה לִּ֔י עֵדִ֖ים נֶאֱמָנִ֑ים אֵ֚ת אוּרִיָּ֣ה הַכֹּהֵ֔ן וְאֶת־זְכַרְיָ֖הוּ בֶּ֥ן יְבֶרֶכְיָֽהוּ׃ 2
Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
וָאֶקְרַב֙ אֶל־הַנְּבִיאָ֔ה וַתַּ֖הַר וַתֵּ֣לֶד בֵּ֑ן וַיֹּ֤אמֶר יְהוָה֙ אֵלַ֔י קְרָ֣א שְׁמֹ֔ו מַהֵ֥ר שָׁלָ֖ל חָ֥שׁ בַּֽז׃ 3
Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’
כִּ֗י בְּטֶ֙רֶם֙ יֵדַ֣ע הַנַּ֔עַר קְרֹ֖א אָבִ֣י וְאִמִּ֑י יִשָּׂ֣א ׀ אֶת־חֵ֣יל דַּמֶּ֗שֶׂק וְאֵת֙ שְׁלַ֣ל שֹׁמְרֹ֔ון לִפְנֵ֖י מֶ֥לֶךְ אַשּֽׁוּר׃ ס 4
Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
וַיֹּ֣סֶף יְהוָ֔ה דַּבֵּ֥ר אֵלַ֛י עֹ֖וד לֵאמֹֽר׃ 5
Yehova anayankhulanso ndi Ine;
יַ֗עַן כִּ֤י מָאַס֙ הָעָ֣ם הַזֶּ֔ה אֵ֚ת מֵ֣י הַשִּׁלֹ֔חַ הַהֹלְכִ֖ים לְאַ֑ט וּמְשֹׂ֥ושׂ אֶת־רְצִ֖ין וּבֶן־רְמַלְיָֽהוּ׃ 6
“Popeza anthu a dziko ili akana madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu, ndipo akukondwerera Rezini ndi mwana wa Remaliya,
וְלָכֵ֡ן הִנֵּ֣ה אֲדֹנָי֩ מַעֲלֶ֨ה עֲלֵיהֶ֜ם אֶת־מֵ֣י הַנָּהָ֗ר הָעֲצוּמִים֙ וְהָ֣רַבִּ֔ים אֶת־מֶ֥לֶךְ אַשּׁ֖וּר וְאֶת־כָּל־כְּבֹודֹ֑ו וְעָלָה֙ עַל־כָּל־אֲפִיקָ֔יו וְהָלַ֖ךְ עַל־כָּל־גְּדֹותָֽיו׃ 7
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo; mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo. Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse ndi mʼmagombe ake onse.
וְחָלַ֤ף בִּֽיהוּדָה֙ שָׁטַ֣ף וְעָבַ֔ר עַד־צַוָּ֖אר יַגִּ֑יעַ וְהָיָה֙ מֻטֹּ֣ות כְּנָפָ֔יו מְלֹ֥א רֹֽחַב־אַרְצְךָ֖ עִמָּ֥נוּ אֵֽל׃ ס 8
Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira, adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi. Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse, iwe Imanueli!”
רֹ֤עוּ עַמִּים֙ וָחֹ֔תּוּ וְהַֽאֲזִ֔ינוּ כֹּ֖ל מֶרְחַקֵּי־אָ֑רֶץ הִתְאַזְּר֣וּ וָחֹ֔תּוּ הִֽתְאַזְּר֖וּ וָחֹֽתּוּ׃ 9
Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere! Tamverani, inu mayiko onse akutali. Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere! Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
עֻ֥צוּ עֵצָ֖ה וְתֻפָ֑ר דַּבְּר֤וּ דָבָר֙ וְלֹ֣א יָק֔וּם כִּ֥י עִמָּ֖נוּ אֵֽל׃ ס 10
Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu, kambiranani zochita, koma zidzalephereka, pakuti Mulungu ali nafe.
כִּי֩ כֹ֨ה אָמַ֧ר יְהוָ֛ה אֵלַ֖י כְּחֶזְקַ֣ת הַיָּ֑ד וְיִסְּרֵ֕נִי מִלֶּ֛כֶת בְּדֶ֥רֶךְ הָֽעָם־הַזֶּ֖ה לֵאמֹֽר׃ 11
Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:
לֹא־תֹאמְר֣וּן קֶ֔שֶׁר לְכֹ֧ל אֲשֶׁר־יֹאמַ֛ר הָעָ֥ם הַזֶּ֖ה קָ֑שֶׁר וְאֶת־מֹורָאֹ֥ו לֹֽא־תִֽירְא֖וּ וְלֹ֥א תַעֲרִֽיצוּ׃ 12
“Usamanene kuti ndi chiwembu, chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu usamaope zimene anthuwa amaziopa, ndipo usamachite nazo mantha.
אֶת־יְהוָ֥ה צְבָאֹ֖ות אֹתֹ֣ו תַקְדִּ֑ישׁוּ וְה֥וּא מֹורַאֲכֶ֖ם וְה֥וּא מֽ͏ַעֲרִֽצְכֶֽם׃ 13
Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
וְהָיָ֖ה לְמִקְדָּ֑שׁ וּלְאֶ֣בֶן נֶ֠גֶף וּלְצ֨וּר מִכְשֹׁ֜ול לִשְׁנֵ֨י בָתֵּ֤י יִשְׂרָאֵל֙ לְפַ֣ח וּלְמֹוקֵ֔שׁ לְיֹושֵׁ֖ב יְרוּשָׁלָֽ͏ִם׃ 14
ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika; koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala mwala wopunthwitsa, mwala umene umapunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
וְכָ֥שְׁלוּ בָ֖ם רַבִּ֑ים וְנָפְל֣וּ וְנִשְׁבָּ֔רוּ וְנֹוקְשׁ֖וּ וְנִלְכָּֽדוּ׃ ס 15
Anthu ambiri adzapunthwapo adzagwa ndi kuthyokathyoka, adzakodwa ndi kugwidwa.”
צֹ֖ור תְּעוּדָ֑ה חֲתֹ֥ום תֹּורָ֖ה בְּלִמֻּדָֽי׃ 16
Manga umboniwu ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
וְחִכִּ֙יתִי֙ לַיהוָ֔ה הַמַּסְתִּ֥יר פָּנָ֖יו מִבֵּ֣ית יַעֲקֹ֑ב וְקִוֵּ֖יתִֽי־לֹֽו׃ 17
Ndidzayembekezera Yehova, amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo. Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
הִנֵּ֣ה אָנֹכִ֗י וְהַיְלָדִים֙ אֲשֶׁ֣ר נָֽתַן־לִ֣י יְהוָ֔ה לְאֹתֹ֥ות וּלְמֹופְתִ֖ים בְּיִשְׂרָאֵ֑ל מֵעִם֙ יְהוָ֣ה צְבָאֹ֔ות הַשֹּׁכֵ֖ן בְּהַ֥ר צִיֹּֽון׃ ס 18
Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
וְכִֽי־יֹאמְר֣וּ אֲלֵיכֶ֗ם דִּרְשׁ֤וּ אֶל־הָאֹבֹות֙ וְאֶל־הַיִּדְּעֹנִ֔ים הַֽמְצַפְצְפִ֖ים וְהַמַּהְגִּ֑ים הֲלֹוא־עַם֙ אֶל־אֱלֹהָ֣יו יִדְרֹ֔שׁ בְּעַ֥ד הַחַיִּ֖ים אֶל־הַמֵּתִֽים׃ 19
Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo,
לְתֹורָ֖ה וְלִתְעוּדָ֑ה אִם־לֹ֤א יֹֽאמְרוּ֙ כַּדָּבָ֣ר הַזֶּ֔ה אֲשֶׁ֥ר אֵֽין־לֹ֖ו שָֽׁחַר׃ 20
kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.
וְעָ֥בַר בָּ֖הּ נִקְשֶׁ֣ה וְרָעֵ֑ב וְהָיָ֨ה כִֽי־יִרְעַ֜ב וְהִתְקַצַּ֗ף וְקִלֵּ֧ל בְּמַלְכֹּ֛ו וּבֵאלֹהָ֖יו וּפָנָ֥ה לְמָֽעְלָה׃ 21
Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo.
וְאֶל־אֶ֖רֶץ יַבִּ֑יט וְהִנֵּ֨ה צָרָ֤ה וַחֲשֵׁכָה֙ מְע֣וּף צוּקָ֔ה וַאֲפֵלָ֖ה מְנֻדָּֽח׃ 22
Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.

< יְשַׁעְיָהוּ 8 >