< יְחֶזְקֵאל 6 >
וַיְהִ֥י דְבַר־יְהוָ֖ה אֵלַ֥י לֵאמֹֽר׃ | 1 |
Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti,
בֶּן־אָדָ֕ם שִׂ֥ים פָּנֶ֖יךָ אֶל־הָרֵ֣י יִשְׂרָאֵ֑ל וְהִנָּבֵ֖א אֲלֵיהֶֽם׃ | 2 |
“Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku mapiri a Israeli; yankhula nawo modzudzula
וְאָ֣מַרְתָּ֔ הָרֵי֙ יִשְׂרָאֵ֔ל שִׁמְע֖וּ דְּבַר־אֲדֹנָ֣י יְהוִ֑ה כֹּה־אָמַ֣ר אֲדֹנָ֣י יְ֠הוִה לֶהָרִ֨ים וְלַגְּבָעֹ֜ות לָאֲפִיקִ֣ים וְלַגֵּאָיֹת (וְלַגֵּאָיֹ֗ות) הִנְנִ֨י אֲנִ֜י מֵבִ֤יא עֲלֵיכֶם֙ חֶ֔רֶב וְאִבַּדְתִּ֖י בָּמֹֽותֵיכֶֽם׃ | 3 |
kuti, ‘Inu mapiri a ku Israeli, imvani mawu a Ambuye Yehova. Iye akuwuza mapiri, magomo, mitsinje ndi zigwa kuti: Ine ndizakuthirani nkhondo ndipo ndidzawononga nyumba zanu mʼmene mukupembedzeramo mafano.
וְנָשַׁ֙מּוּ֙ מִזְבְּחֹ֣ותֵיכֶ֔ם וְנִשְׁבְּר֖וּ חַמָּֽנֵיכֶ֑ם וְהִפַּלְתִּי֙ חַלְלֵיכֶ֔ם לִפְנֵ֖י גִּלּוּלֵיכֶֽם׃ | 4 |
Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu.
וְנָתַתִּ֗י אֶת־פִּגְרֵי֙ בְּנֵ֣י יִשְׂרָאֵ֔ל לִפְנֵ֖י גִּלּֽוּלֵיהֶ֑ם וְזֵרִיתִי֙ אֶת־עַצְמֹ֣ותֵיכֶ֔ם סְבִיבֹ֖ות מִזְבְּחֹותֵיכֶֽם׃ | 5 |
Ine ndidzagoneka mitembo ya Aisraeli pamaso pa mafano awo, ndipo ndidzamwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu ansembe.
בְּכֹל֙ מֹושְׁבֹ֣ותֵיכֶ֔ם הֶעָרִ֣ים תֶּחֱרַ֔בְנָה וְהַבָּמֹ֖ות תִּישָׁ֑מְנָה לְמַעַן֩ יֶחֶרְב֨וּ וְיֶאְשְׁמ֜וּ מִזְבְּחֹֽותֵיכֶ֗ם וְנִשְׁבְּר֤וּ וְנִשְׁבְּתוּ֙ גִּלּ֣וּלֵיכֶ֔ם וְנִגְדְּעוּ֙ חַמָּ֣נֵיכֶ֔ם וְנִמְח֖וּ מַעֲשֵׂיכֶֽם׃ | 6 |
Konse kumene mumakhala, mizinda yanu idzasanduka bwinja. Nyumba zanu zopembedzera mafano zidzagumulidwa kotero kuti maguwa anu adzawonongedwa ndi kusakazidwa, mafano anu adzaphwanyidwa ndi kuwonongedwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa pansi ndipo zonse zimene munapanga zidzatheratu.
וְנָפַ֥ל חָלָ֖ל בְּתֹֽוכְכֶ֑ם וִֽידַעְתֶּ֖ם כִּֽי־אֲנִ֥י יְהוָֽה׃ | 7 |
Anthu anu adzaphedwa pakati panu, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
וְהֹותַרְתִּ֗י בִּהְיֹ֥ות לָכֶ֛ם פְּלִ֥יטֵי חֶ֖רֶב בַּגֹּויִ֑ם בְּהִזָּרֹֽותֵיכֶ֖ם בָּאֲרָצֹֽות׃ | 8 |
“Komabe ndidzasiya ena pangʼono opulumuka ku nkhondo. Iwowa ndidzawamwazira ku mayiko ena pakati pa anthu a mitundu ina.
וְזָכְר֨וּ פְלִֽיטֵיכֶ֜ם אֹותִ֗י בַּגֹּויִם֮ אֲשֶׁ֣ר נִשְׁבּוּ־שָׁם֒ אֲשֶׁ֨ר נִשְׁבַּ֜רְתִּי אֶת־לִבָּ֣ם הַזֹּונֶ֗ה אֲשֶׁר־סָר֙ מֵֽעָלַ֔י וְאֵת֙ עֵֽינֵיהֶ֔ם הַזֹּנֹ֕ות אַחֲרֵ֖י גִּלּֽוּלֵיהֶ֑ם וְנָקֹ֙טּוּ֙ בִּפְנֵיהֶ֔ם אֶל־הָֽרָעֹות֙ אֲשֶׁ֣ר עָשׂ֔וּ לְכֹ֖ל תֹּועֲבֹתֵיהֶֽם׃ | 9 |
Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata.
וְיָדְע֖וּ כִּֽי־אֲנִ֣י יְהוָ֑ה לֹ֤א אֶל־חִנָּם֙ דִּבַּ֔רְתִּי לַעֲשֹׂ֥ות לָהֶ֖ם הָרָעָ֥ה הַזֹּֽאת׃ פ | 10 |
Ndipo iwo adzadziwa kuti ndine Yehova ndi kuti sindinkawaopseza chabe pamene ndinanena kuti ndidzawawononga.
כֹּֽה־אָמַ֞ר אֲדֹנָ֣י יְהוִ֗ה הַכֵּ֨ה בְכַפְּךָ֜ וּרְקַ֤ע בְּרַגְלְךָ֙ וֶֽאֱמָר־אָ֔ח אֶ֛ל כָּל־תֹּועֲבֹ֥ות רָעֹ֖ות בֵּ֣ית יִשְׂרָאֵ֑ל אֲשֶׁ֗ר בַּחֶ֛רֶב בָּרָעָ֥ב וּבַדֶּ֖בֶר יִפֹּֽלוּ׃ | 11 |
“Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri.
הָרָחֹ֞וק בַּדֶּ֣בֶר יָמ֗וּת וְהַקָּרֹוב֙ בַּחֶ֣רֶב יִפֹּ֔ול וְהַנִּשְׁאָר֙ וְהַנָּצ֔וּר בָּרָעָ֖ב יָמ֑וּת וְכִלֵּיתִ֥י חֲמָתִ֖י בָּֽם׃ | 12 |
Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo.
וִֽידַעְתֶּם֙ כִּֽי־אֲנִ֣י יְהוָ֔ה בִּֽהְיֹ֣ות חַלְלֵיהֶ֗ם בְּתֹוךְ֙ גִּלּ֣וּלֵיהֶ֔ם סְבִיבֹ֖ות מִזְבְּחֹֽותֵיהֶ֑ם אֶל֩ כָּל־גִּבְעָ֨ה רָמָ֜ה בְּכֹ֣ל ׀ רָאשֵׁ֣י הֶהָרִ֗ים וְתַ֨חַת כָּל־עֵ֤ץ רַֽעֲנָן֙ וְתַ֙חַת֙ כָּל־אֵלָ֣ה עֲבֻתָּ֔ה מְקֹ֗ום אֲשֶׁ֤ר נָֽתְנוּ־שָׁם֙ רֵ֣יחַ נִיחֹ֔חַ לְכֹ֖ל גִּלּוּלֵיהֶֽם׃ | 13 |
Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse.
וְנָטִ֤יתִי אֶת־יָדִי֙ עֲלֵיהֶ֔ם וְנָתַתִּ֨י אֶת־הָאָ֜רֶץ שְׁמָמָ֤ה וּמְשַׁמָּה֙ מִמִּדְבַּ֣ר דִּבְלָ֔תָה בְּכֹ֖ל מֹושְׁבֹֽותֵיהֶ֑ם וְיָדְע֖וּ כִּֽי־אֲנִ֥י יְהוָֽה׃ פ | 14 |
Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”