< שיר השירים 6 >
אָנָה הָלַךְ דּוֹדֵךְ הַיָּפָה בַּנָּשִׁים אָנָה פָּנָה דוֹדֵךְ וּנְבַקְשֶׁנּוּ עִמָּֽךְ׃ | 1 |
Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?
דּוֹדִי יָרַד לְגַנּוֹ לַעֲרֻגוֹת הַבֹּשֶׂם לִרְעוֹת בַּגַּנִּים וְלִלְקֹט שֽׁוֹשַׁנִּֽים׃ | 2 |
Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake, ku timinda ta zokometsera zakudya, akukadyetsa ziweto zake ku minda, ndiponso akuthyola maluwa okongola.
אֲנִי לְדוֹדִי וְדוֹדִי לִי הָרֹעֶה בַּשּׁוֹשַׁנִּֽים׃ | 3 |
Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.
יָפָה אַתְּ רַעְיָתִי כְּתִרְצָה נָאוָה כִּירוּשָׁלָ͏ִם אֲיֻמָּה כַּנִּדְגָּלֽוֹת׃ | 4 |
Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza, wokongola kwambiri ngati Yerusalemu, ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.
הָסֵבִּי עֵינַיִךְ מִנֶּגְדִּי שֶׁהֵם הִרְהִיבֻנִי שַׂעְרֵךְ כְּעֵדֶר הָֽעִזִּים שֶׁגָּלְשׁוּ מִן־הַגִּלְעָֽד׃ | 5 |
Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
שִׁנַּיִךְ כְּעֵדֶר הָֽרְחֵלִים שֶׁעָלוּ מִן־הָרַחְצָה שֶׁכֻּלָּם מַתְאִימוֹת וְשַׁכֻּלָה אֵין בָּהֶֽם׃ | 6 |
Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa, iliyonse ili ndi ana amapasa, palibe imene ili yokha.
כְּפֶלַח הָרִמּוֹן רַקָּתֵךְ מִבַּעַד לְצַמָּתֵֽךְ׃ | 7 |
Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu, masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.
שִׁשִּׁים הֵמָּה מְלָכוֹת וּשְׁמֹנִים פִּֽילַגְשִׁים וַעֲלָמוֹת אֵין מִסְפָּֽר׃ | 8 |
Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60, ndi azikazi 80, ndi anamwali osawerengeka;
אַחַת הִיא יוֹנָתִי תַמָּתִי אַחַת הִיא לְאִמָּהּ בָּרָה הִיא לְיֽוֹלַדְתָּהּ רָאוּהָ בָנוֹת וַֽיְאַשְּׁרוּהָ מְלָכוֹת וּפִֽילַגְשִׁים וַֽיְהַלְלֽוּהָ׃ | 9 |
koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.
מִי־זֹאת הַנִּשְׁקָפָה כְּמוֹ־שָׁחַר יָפָה כַלְּבָנָה בָּרָה כַּֽחַמָּה אֲיֻמָּה כַּנִּדְגָּלֽוֹת׃ | 10 |
Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha, wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja?
אֶל־גִּנַּת אֱגוֹז יָרַדְתִּי לִרְאוֹת בְּאִבֵּי הַנָּחַל לִרְאוֹת הֲפָֽרְחָה הַגֶּפֶן הֵנֵצוּ הָרִמֹּנִֽים׃ | 11 |
Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
לֹא יָדַעְתִּי נַפְשִׁי שָׂמַתְנִי מַרְכְּבוֹת עַמִּי נָדִֽיב׃ | 12 |
Ndisanazindikire kanthu, ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga.
שׁוּבִי שׁוּבִי הַשּׁוּלַמִּית שׁוּבִי שׁוּבִי וְנֶחֱזֶה־בָּךְ מַֽה־תֶּחֱזוּ בַּשּׁוּלַמִּית כִּמְחֹלַת הַֽמַּחֲנָֽיִם׃ | 13 |
Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami; bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe! Mwamuna Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami, pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?