< תהילים 63 >

מִזְמוֹר לְדָוִד בִּהְיוֹתוֹ בְּמִדְבַּר יְהוּדָֽה׃ אֱלֹהִים ׀ אֵלִי אַתָּה אֲֽשַׁחֲרֶךָּ צָמְאָה לְךָ ׀ נַפְשִׁי כָּמַהּ לְךָ בְשָׂרִי בְּאֶֽרֶץ־צִיָּה וְעָיֵף בְּלִי־מָֽיִם׃ 1
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.
כֵּן בַּקֹּדֶשׁ חֲזִיתִךָ לִרְאוֹת עֻזְּךָ וּכְבוֹדֶֽךָ׃ 2
Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
כִּי־טוֹב חַסְדְּךָ מֵחַיִּים שְׂפָתַי יְשַׁבְּחֽוּנְךָ׃ 3
Chifukwa chikondi chanu ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
כֵּן אֲבָרֶכְךָ בְחַיָּי בְּשִׁמְךָ אֶשָּׂא כַפָּֽי׃ 4
Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
כְּמוֹ חֵלֶב וָדֶשֶׁן תִּשְׂבַּע נַפְשִׁי וְשִׂפְתֵי רְנָנוֹת יְהַלֶּל־פִּֽי׃ 5
Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
אִם־זְכַרְתִּיךָ עַל־יְצוּעָי בְּאַשְׁמֻרוֹת אֶהְגֶּה־בָּֽךְ׃ 6
Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
כִּֽי־הָיִיתָ עֶזְרָתָה לִּי וּבְצֵל כְּנָפֶיךָ אֲרַנֵּֽן׃ 7
Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
דָּבְקָה נַפְשִׁי אַחֲרֶיךָ בִּי תָּמְכָה יְמִינֶֽךָ׃ 8
Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
וְהֵמָּה לְשׁוֹאָה יְבַקְשׁוּ נַפְשִׁי יָבֹאוּ בְּֽתַחְתִּיּוֹת הָאָֽרֶץ׃ 9
Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
יַגִּירֻהוּ עַל־יְדֵי־חָרֶב מְנָת שֻׁעָלִים יִהְיֽוּ׃ 10
Iwo adzaperekedwa ku lupanga ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.
וְהַמֶּלֶךְ יִשְׂמַח בֵּאלֹהִים יִתְהַלֵּל כׇּל־הַנִּשְׁבָּע בּוֹ כִּי יִסָּכֵר פִּי דוֹבְרֵי־שָֽׁקֶר׃ 11
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.

< תהילים 63 >