< תהילים 15 >

מִזְמוֹר לְדָוִד יְהֹוָה מִי־יָגוּר בְּאׇהֳלֶךָ מִֽי־יִשְׁכֹּן בְּהַר קׇדְשֶֽׁךָ׃ 1
Salimo la Davide. Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?
הוֹלֵךְ תָּמִים וּפֹעֵל צֶדֶק וְדֹבֵר אֱמֶת בִּלְבָבֽוֹ׃ 2
Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
לֹֽא־רָגַל ׀ עַל־לְשֹׁנוֹ לֹא־עָשָׂה לְרֵעֵהוּ רָעָה וְחֶרְפָּה לֹא־נָשָׂא עַל־קְרֹבֽוֹ׃ 3
ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
נִבְזֶה ׀ בְּֽעֵינָיו נִמְאָס וְאֶת־יִרְאֵי יְהֹוָה יְכַבֵּד נִשְׁבַּע לְהָרַע וְלֹא יָמִֽר׃ 4
amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka,
כַּסְפּוֹ ׀ לֹא־נָתַן בְּנֶשֶׁךְ וְשֹׁחַד עַל־נָקִי לֹא לָקָח עֹֽשֵׂה־אֵלֶּה לֹא יִמּוֹט לְעוֹלָֽם׃ 5
amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse.

< תהילים 15 >