< תהילים 107 >

הֹדוּ לַיהֹוָה כִּי־טוֹב כִּי לְעוֹלָם חַסְדּֽוֹ׃ 1
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.
יֹאמְרוּ גְּאוּלֵי יְהֹוָה אֲשֶׁר גְּאָלָם מִיַּד־צָֽר׃ 2
Owomboledwa a Yehova anene zimenezi amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
וּֽמֵאֲרָצוֹת קִבְּצָם מִמִּזְרָח וּמִֽמַּעֲרָב מִצָּפוֹן וּמִיָּֽם׃ 3
iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko, kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
תָּעוּ בַמִּדְבָּר בִּישִׁימוֹן דָּרֶךְ עִיר מוֹשָׁב לֹא מָצָֽאוּ׃ 4
Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu, osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
רְעֵבִים גַּם־צְמֵאִים נַפְשָׁם בָּהֶם תִּתְעַטָּֽף׃ 5
Iwo anamva njala ndi ludzu, ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
וַיִּצְעֲקוּ אֶל־יְהֹוָה בַּצַּר לָהֶם מִמְּצוּקוֹתֵיהֶם יַצִּילֵֽם׃ 6
Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
וַֽיַּדְרִיכֵם בְּדֶרֶךְ יְשָׁרָה לָלֶכֶת אֶל־עִיר מוֹשָֽׁב׃ 7
Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.
יוֹדוּ לַיהֹוָה חַסְדּוֹ וְנִפְלְאוֹתָיו לִבְנֵי אָדָֽם׃ 8
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
כִּֽי־הִשְׂבִּיעַ נֶפֶשׁ שֹׁקֵקָה וְנֶפֶשׁ רְעֵבָה מִלֵּא־טֽוֹב׃ 9
pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.
יֹשְׁבֵי חֹשֶׁךְ וְצַלְמָוֶת אֲסִירֵי עֳנִי וּבַרְזֶֽל׃ 10
Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,
כִּֽי־הִמְרוּ אִמְרֵי־אֵל וַעֲצַת עֶלְיוֹן נָאָֽצוּ׃ 11
pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.
וַיַּכְנַע בֶּעָמָל לִבָּם כָּשְׁלוּ וְאֵין עֹזֵֽר׃ 12
Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.
וַיִּזְעֲקוּ אֶל־יְהֹוָה בַּצַּר לָהֶם מִמְּצֻקוֹתֵיהֶם יוֹשִׁיעֵֽם׃ 13
Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
יוֹצִיאֵם מֵחֹשֶׁךְ וְצַלְמָוֶת וּמוֹסְרוֹתֵיהֶם יְנַתֵּֽק׃ 14
Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu ndipo anadula maunyolo awo.
יוֹדוּ לַיהֹוָה חַסְדּוֹ וְנִפְלְאוֹתָיו לִבְנֵי אָדָֽם׃ 15
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
כִּֽי־שִׁבַּר דַּלְתוֹת נְחֹשֶׁת וּבְרִיחֵי בַרְזֶל גִּדֵּֽעַ׃ 16
pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.
אֱוִלִים מִדֶּרֶךְ פִּשְׁעָם וּֽמֵעֲוֺנֹתֵיהֶם יִתְעַנּֽוּ׃ 17
Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira, ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
כׇּל־אֹכֶל תְּתַעֵב נַפְשָׁם וַיַּגִּיעוּ עַד־שַׁעֲרֵי־מָֽוֶת׃ 18
Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
וַיִּזְעֲקוּ אֶל־יְהֹוָה בַּצַּר לָהֶם מִמְּצֻקוֹתֵיהֶם יוֹשִׁיעֵֽם׃ 19
Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
יִשְׁלַח דְּבָרוֹ וְיִרְפָּאֵם וִימַלֵּט מִשְּׁחִֽיתוֹתָֽם׃ 20
Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa; anawalanditsa ku manda.
יוֹדוּ לַיהֹוָה חַסְדּוֹ וְנִפְלְאוֹתָיו לִבְנֵי אָדָֽם׃ 21
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
וְיִזְבְּחוּ זִבְחֵי תוֹדָה וִיסַפְּרוּ מַעֲשָׂיו בְּרִנָּֽה׃ 22
Apereke nsembe yachiyamiko ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
׆ יוֹרְדֵי הַיָּם בׇּאֳנִיּוֹת עֹשֵׂי מְלָאכָה בְּמַיִם רַבִּֽים׃ 23
Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi; Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.
׆ הֵמָּה רָאוּ מַעֲשֵׂי יְהֹוָה וְנִפְלְאוֹתָיו בִּמְצוּלָֽה׃ 24
Anaona ntchito za Yehova, machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.
׆ וַיֹּאמֶר וַֽיַּעֲמֵד רוּחַ סְעָרָה וַתְּרוֹמֵם גַּלָּֽיו׃ 25
Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho imene inabweretsa mafunde ataliatali.
׆ יַעֲלוּ שָׁמַיִם יֵרְדוּ תְהוֹמוֹת נַפְשָׁם בְּרָעָה תִתְמוֹגָֽג׃ 26
Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya; pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.
׆ יָחוֹגּוּ וְיָנוּעוּ כַּשִּׁכּוֹר וְכׇל־חׇכְמָתָם תִּתְבַּלָּֽע׃ 27
Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera; anali pa mapeto a moyo wawo.
׆ וַיִּצְעֲקוּ אֶל־יְהֹוָה בַּצַּר לָהֶם וּֽמִמְּצוּקֹתֵיהֶם יוֹצִיאֵֽם׃ 28
Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.
יָקֵם סְעָרָה לִדְמָמָה וַיֶּחֱשׁוּ גַּלֵּיהֶֽם׃ 29
Yehova analetsa namondwe, mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.
וַיִּשְׂמְחוּ כִֽי־יִשְׁתֹּקוּ וַיַּנְחֵם אֶל־מְחוֹז חֶפְצָֽם׃ 30
Anali osangalala pamene kunakhala bata, ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.
יוֹדוּ לַיהֹוָה חַסְדּוֹ וְנִפְלְאוֹתָיו לִבְנֵי אָדָֽם׃ 31
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
וִֽירוֹמְמוּהוּ בִּקְהַל־עָם וּבְמוֹשַׁב זְקֵנִים יְהַלְלֽוּהוּ׃ 32
Akuze Iye mu msonkhano wa anthu ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.
יָשֵׂם נְהָרוֹת לְמִדְבָּר וּמֹצָאֵי מַיִם לְצִמָּאֽוֹן׃ 33
Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu, akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
אֶרֶץ פְּרִי לִמְלֵחָה מֵרָעַת יוֹשְׁבֵי בָֽהּ׃ 34
ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere, chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
יָשֵׂם מִדְבָּר לַאֲגַם־מַיִם וְאֶרֶץ צִיָּה לְמֹצָאֵי מָֽיִם׃ 35
Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
וַיּוֹשֶׁב שָׁם רְעֵבִים וַיְכוֹנְנוּ עִיר מוֹשָֽׁב׃ 36
kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako, ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
וַיִּזְרְעוּ שָׂדוֹת וַיִּטְּעוּ כְרָמִים וַיַּעֲשׂוּ פְּרִי תְבוּאָֽה׃ 37
Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa ndipo anakolola zipatso zochuluka;
וַיְבָרְכֵם וַיִּרְבּוּ מְאֹד וּבְהֶמְתָּם לֹא יַמְעִֽיט׃ 38
Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri, ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.
וַיִּמְעֲטוּ וַיָּשֹׁחוּ מֵעֹצֶר רָעָה וְיָגֽוֹן׃ 39
Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;
׆ שֹׁפֵךְ בּוּז עַל־נְדִיבִים וַיַּתְעֵם בְּתֹהוּ לֹא־דָֽרֶךְ׃ 40
Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.
וַיְשַׂגֵּב אֶבְיוֹן מֵעוֹנִי וַיָּשֶׂם כַּצֹּאן מִשְׁפָּחֽוֹת׃ 41
Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo ngati magulu a nkhosa.
יִרְאוּ יְשָׁרִים וְיִשְׂמָחוּ וְכׇל־עַוְלָה קָפְצָה פִּֽיהָ׃ 42
Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala, koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.
מִי־חָכָם וְיִשְׁמׇר־אֵלֶּה וְיִתְבּוֹנְנוּ חַֽסְדֵי יְהֹוָֽה׃ 43
Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.

< תהילים 107 >