< מִשְׁלֵי 19 >
טֽוֹב־רָשׁ הוֹלֵךְ בְּתֻמּוֹ מֵעִקֵּשׁ שְׂפָתָיו וְהוּא כְסִֽיל׃ | 1 |
Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.
גַּם בְּלֹא־דַעַת נֶפֶשׁ לֹא־טוֹב וְאָץ בְּרַגְלַיִם חוֹטֵֽא׃ | 2 |
Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru; ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.
אִוֶּלֶת אָדָם תְּסַלֵּף דַּרְכּוֹ וְעַל־יְהֹוָה יִזְעַף לִבּֽוֹ׃ | 3 |
Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta, mtima wake umakwiyira Yehova.
הוֹן יֹסִיף רֵעִים רַבִּים וְדָל מֵרֵעֵהוּ יִפָּרֵֽד׃ | 4 |
Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.
עֵד שְׁקָרִים לֹא יִנָּקֶה וְיָפִיחַ כְּזָבִים לֹא יִמָּלֵֽט׃ | 5 |
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.
רַבִּים יְחַלּוּ פְנֵֽי־נָדִיב וְכׇל־הָרֵעַ לְאִישׁ מַתָּֽן׃ | 6 |
Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima, ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.
כׇּל ־ אֲחֵי־רָשׁ ׀ שְֽׂנֵאֻהוּ אַף כִּי מְרֵעֵהוּ רָחֲקוּ מִמֶּנּוּ מְרַדֵּף אֲמָרִים (לא) [לוֹ־]הֵֽמָּה׃ | 7 |
Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo adzamuthawa kupita kutali. Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.
קֹֽנֶה־לֵּב אֹהֵב נַפְשׁוֹ שֹׁמֵר תְּבוּנָה לִמְצֹא־טֽוֹב׃ | 8 |
Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
עֵד שְׁקָרִים לֹא יִנָּקֶה וְיָפִיחַ כְּזָבִים יֹאבֵֽד׃ | 9 |
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
לֹא־נָאוֶה לִכְסִיל תַּעֲנוּג אַף כִּֽי־לְעֶבֶד ׀ מְשֹׁל בְּשָׂרִֽים׃ | 10 |
Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
שֵׂכֶל אָדָם הֶאֱרִיךְ אַפּוֹ וְתִפְאַרְתּוֹ עֲבֹר עַל־פָּֽשַׁע׃ | 11 |
Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
נַהַם כַּכְּפִיר זַעַף מֶלֶךְ וּכְטַל עַל־עֵשֶׂב רְצוֹנֽוֹ׃ | 12 |
Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
הַוֺּת לְאָבִיו בֵּן כְּסִיל וְדֶלֶף טֹרֵד מִדְיְנֵי אִשָּֽׁה׃ | 13 |
Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.
בַּיִת וָהוֹן נַחֲלַת אָבוֹת וּמֵיְהֹוָה אִשָּׁה מַשְׂכָּֽלֶת׃ | 14 |
Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo; koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
עַצְלָה תַּפִּיל תַּרְדֵּמָה וְנֶפֶשׁ רְמִיָּה תִרְעָֽב׃ | 15 |
Ulesi umagonetsa tulo tofa nato ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.
שֹׁמֵר מִצְוָה שֹׁמֵר נַפְשׁוֹ בּוֹזֵה דְרָכָיו (יומת) [יָמֽוּת]׃ | 16 |
Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake, koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.
מַלְוֵה יְהֹוָה חוֹנֵֽן דָּל וּגְמֻלוֹ יְשַׁלֶּם־לֽוֹ׃ | 17 |
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
יַסֵּר בִּנְךָ כִּֽי־יֵשׁ תִּקְוָה וְאֶל־הֲמִיתוֹ אַל־תִּשָּׂא נַפְשֶֽׁךָ׃ | 18 |
Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.
(גרל) [גְּֽדׇל־]חֵמָה נֹשֵׂא עֹנֶשׁ כִּי אִם־תַּצִּיל וְעוֹד תּוֹסִֽף׃ | 19 |
Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango; pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.
שְׁמַע עֵצָה וְקַבֵּל מוּסָר לְמַעַן תֶּחְכַּם בְּאַחֲרִיתֶֽךָ׃ | 20 |
Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
רַבּוֹת מַחֲשָׁבוֹת בְּלֶב־אִישׁ וַעֲצַת יְהֹוָה הִיא תָקֽוּם׃ | 21 |
Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
תַּאֲוַת אָדָם חַסְדּוֹ וְטֽוֹב־רָשׁ מֵאִישׁ כָּזָֽב׃ | 22 |
Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
יִרְאַת יְהֹוָה לְחַיִּים וְשָׂבֵעַ יָלִין בַּל־יִפָּקֶד רָֽע׃ | 23 |
Kuopa Yehova kumabweretsa moyo; wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
טָמַן עָצֵל יָדוֹ בַּצַּלָּחַת גַּם־אֶל־פִּיהוּ לֹא יְשִׁיבֶֽנָּה׃ | 24 |
Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale; koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.
לֵץ תַּכֶּה וּפֶתִי יַעְרִם וְהוֹכִיחַ לְנָבוֹן יָבִין דָּֽעַת׃ | 25 |
Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo; dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.
מְֽשַׁדֶּד־אָב יַבְרִיחַ אֵם בֵּן מֵבִישׁ וּמַחְפִּֽיר׃ | 26 |
Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake, ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.
חֲֽדַל־בְּנִי לִשְׁמֹעַ מוּסָר לִשְׁגוֹת מֵאִמְרֵי־דָֽעַת׃ | 27 |
Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.
עֵד בְּלִיַּעַל יָלִיץ מִשְׁפָּט וּפִי רְשָׁעִים יְבַלַּע־אָֽוֶן׃ | 28 |
Mboni yopanda pake imanyoza cholungama, ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.
נָכוֹנוּ לַלֵּצִים שְׁפָטִים וּמַהֲלֻמוֹת לְגֵו כְּסִילִֽים׃ | 29 |
Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa, ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.