< מִשְׁלֵי 10 >
מִשְׁלֵי שְׁלֹמֹה בֵּן חָכָם יְשַׂמַּח־אָב וּבֵן כְּסִיל תּוּגַת אִמּֽוֹ׃ | 1 |
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
לֹֽא־יוֹעִילוּ אוֹצְרוֹת רֶשַׁע וּצְדָקָה תַּצִּיל מִמָּֽוֶת׃ | 2 |
Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
לֹא־יַרְעִיב יְהֹוָה נֶפֶשׁ צַדִּיק וְהַוַּת רְשָׁעִים יֶהְדֹּֽף׃ | 3 |
Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
רָאשׁ עֹשֶׂה כַף־רְמִיָּה וְיַד חָרוּצִים תַּעֲשִֽׁיר׃ | 4 |
Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
אֹגֵר בַּקַּיִץ בֵּן מַשְׂכִּיל נִרְדָּם בַּקָּצִיר בֵּן מֵבִֽישׁ׃ | 5 |
Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
בְּרָכוֹת לְרֹאשׁ צַדִּיק וּפִי רְשָׁעִים יְכַסֶּה חָמָֽס׃ | 6 |
Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama, koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
זֵכֶר צַדִּיק לִבְרָכָה וְשֵׁם רְשָׁעִים יִרְקָֽב׃ | 7 |
Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso, koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
חֲכַם־לֵב יִקַּח מִצְוֺת וֶאֱוִיל שְׂפָתַיִם יִלָּבֵֽט׃ | 8 |
Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
הוֹלֵךְ בַּתֹּם יֵלֶךְ בֶּטַח וּמְעַקֵּשׁ דְּרָכָיו יִוָּדֵֽעַ׃ | 9 |
Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
קֹרֵֽץ עַיִן יִתֵּן עַצָּבֶת וֶאֱוִיל שְׂפָתַיִם יִלָּבֵֽט׃ | 10 |
Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto, koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
מְקוֹר חַיִּים פִּי צַדִּיק וּפִי רְשָׁעִים יְכַסֶּה חָמָֽס׃ | 11 |
Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
שִׂנְאָה תְּעֹרֵר מְדָנִים וְעַל כׇּל־פְּשָׁעִים תְּכַסֶּה אַהֲבָֽה׃ | 12 |
Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
בְּשִׂפְתֵי נָבוֹן תִּמָּצֵא חׇכְמָה וְשֵׁבֶט לְגֵו חֲסַר־לֵֽב׃ | 13 |
Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu, koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
חֲכָמִים יִצְפְּנוּ־דָעַת וּפִֽי־אֱוִיל מְחִתָּה קְרֹבָֽה׃ | 14 |
Anzeru amasunga chidziwitso koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
הוֹן עָשִׁיר קִרְיַת עֻזּוֹ מְחִתַּת דַּלִּים רֵישָֽׁם׃ | 15 |
Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
פְּעֻלַּת צַדִּיק לְחַיִּים תְּבוּאַת רָשָׁע לְחַטָּֽאת׃ | 16 |
Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama, koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
אֹרַח לְחַיִּים שׁוֹמֵר מוּסָר וְעֹזֵב תּוֹכַחַת מַתְעֶֽה׃ | 17 |
Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo, koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
מְכַסֶּה שִׂנְאָה שִׂפְתֵי־שָׁקֶר וּמוֹצִא דִבָּה הוּא כְסִֽיל׃ | 18 |
Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
בְּרֹב דְּבָרִים לֹא יֶחְדַּל־פָּשַׁע וְחוֹשֵׂךְ שְׂפָתָיו מַשְׂכִּֽיל׃ | 19 |
Mawu akachuluka zolakwa sizisowa, koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
כֶּסֶף נִבְחָר לְשׁוֹן צַדִּיק לֵב רְשָׁעִים כִּמְעָֽט׃ | 20 |
Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
שִׂפְתֵי צַדִּיק יִרְעוּ רַבִּים וֶאֱוִילִים בַּחֲסַר־לֵב יָמֽוּתוּ׃ | 21 |
Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
בִּרְכַּת יְהֹוָה הִיא תַעֲשִׁיר וְלֹֽא־יוֹסִף עֶצֶב עִמָּֽהּ׃ | 22 |
Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
כִּשְׂחוֹק לִכְסִיל עֲשׂוֹת זִמָּה וְחׇכְמָה לְאִישׁ תְּבוּנָֽה׃ | 23 |
Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
מְגוֹרַת רָשָׁע הִיא תְבוֹאֶנּוּ וְתַאֲוַת צַדִּיקִים יִתֵּֽן׃ | 24 |
Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira; chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
כַּעֲבוֹר סוּפָה וְאֵין רָשָׁע וְצַדִּיק יְסוֹד עוֹלָֽם׃ | 25 |
Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa, koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
כַּחֹמֶץ ׀ לַשִּׁנַּיִם וְכֶעָשָׁן לָעֵינָיִם כֵּן הֶעָצֵל לְשֹׁלְחָֽיו׃ | 26 |
Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso, ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
יִרְאַת יְהֹוָה תּוֹסִיף יָמִים וּשְׁנוֹת רְשָׁעִים תִּקְצֹֽרְנָה׃ | 27 |
Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo; koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
תּוֹחֶלֶת צַדִּיקִים שִׂמְחָה וְתִקְוַת רְשָׁעִים תֹּאבֵֽד׃ | 28 |
Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe, koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
מָעוֹז לַתֹּם דֶּרֶךְ יְהֹוָה וּמְחִתָּה לְפֹעֲלֵי אָֽוֶן׃ | 29 |
Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino, koma wochita zoyipa adzawonongeka.
צַדִּיק לְעוֹלָם בַּל־יִמּוֹט וּרְשָׁעִים לֹא יִשְׁכְּנוּ־אָֽרֶץ׃ | 30 |
Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
פִּֽי־צַדִּיק יָנוּב חׇכְמָה וּלְשׁוֹן תַּהְפֻּכוֹת תִּכָּרֵֽת׃ | 31 |
Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru, koma lilime lokhota lidzadulidwa.
שִׂפְתֵי צַדִּיק יֵדְעוּן רָצוֹן וּפִי רְשָׁעִים תַּהְפֻּכֽוֹת׃ | 32 |
Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula, koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.