< איוב 38 >
וַיַּֽעַן־יְהֹוָה אֶת־אִיּוֹב (מנהסערה) [מִן ׀ הַסְּעָרָה] וַיֹּאמַֽר׃ | 1 |
Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
מִי זֶה ׀ מַחְשִׁיךְ עֵצָה בְמִלִּין בְּֽלִי־דָֽעַת׃ | 2 |
“Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru?
אֱזׇר־נָא כְגֶבֶר חֲלָצֶיךָ וְאֶשְׁאָלְךָ וְהוֹדִיעֵֽנִי׃ | 3 |
Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe.
אֵיפֹה הָיִיתָ בְּיׇסְדִי־אָרֶץ הַגֵּד אִם־יָדַעְתָּ בִינָֽה׃ | 4 |
“Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa.
מִי־שָׂם מְמַדֶּיהָ כִּי תֵדָע אוֹ מִֽי־נָטָה עָלֶיהָ קָּֽו׃ | 5 |
Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
עַל־מָה אֲדָנֶיהָ הׇטְבָּעוּ אוֹ מִי־יָרָה אֶבֶן פִּנָּתָֽהּ׃ | 6 |
Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
בְּרׇן־יַחַד כּוֹכְבֵי בֹקֶר וַיָּרִיעוּ כׇּל־בְּנֵי אֱלֹהִֽים׃ | 7 |
pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
וַיָּסֶךְ בִּדְלָתַיִם יָם בְּגִיחוֹ מֵרֶחֶם יֵצֵֽא׃ | 8 |
“Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
בְּשׂוּמִי עָנָן לְבֻשׁוֹ וַעֲרָפֶל חֲתֻלָּתֽוֹ׃ | 9 |
pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
וָאֶשְׁבֹּר עָלָיו חֻקִּי וָאָשִׂים בְּרִיחַ וּדְלָתָֽיִם׃ | 10 |
pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
וָאֹמַר עַד־פֹּה תָבוֹא וְלֹא תֹסִיף וּפֹא־יָשִׁית בִּגְאוֹן גַּלֶּֽיךָ׃ | 11 |
Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
הֲֽמִיָּמֶיךָ צִוִּיתָ בֹּקֶר (ידעתה שחר) [יִדַּעְתָּ הַשַּׁחַר] מְקֹמֽוֹ׃ | 12 |
“Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa, kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
לֶאֱחֹז בְּכַנְפוֹת הָאָרֶץ וְיִנָּעֲרוּ רְשָׁ עִ ים מִמֶּֽנָּה׃ | 13 |
kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
תִּתְהַפֵּךְ כְּחֹמֶר חוֹתָם וְיִֽתְיַצְּבוּ כְּמוֹ לְבֽוּשׁ׃ | 14 |
Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo; zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
וְיִמָּנַע מֵרְשָׁ עִ ים אוֹרָם וּזְרוֹעַ רָמָה תִּשָּׁבֵֽר׃ | 15 |
Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa, ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
הֲבָאתָ עַד־נִבְכֵי־יָם וּבְחֵקֶר תְּהוֹם הִתְהַלָּֽכְתָּ׃ | 16 |
“Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja kapena pa magwero ake ozama?
הֲנִגְלוּ לְךָ שַׁעֲרֵי־מָוֶת וְשַׁעֲרֵי צַלְמָוֶת תִּרְאֶֽה׃ | 17 |
Kodi anakuonetsapo zipata za imfa? Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
הִתְבֹּנַנְתָּ עַד־רַחֲבֵי־אָרֶץ הַגֵּד אִם־יָדַעְתָּ כֻלָּֽהּ׃ | 18 |
Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa? Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
אֵי־זֶה הַדֶּרֶךְ יִשְׁכׇּן־אוֹר וְחֹשֶׁךְ אֵי־זֶה מְקֹמֽוֹ׃ | 19 |
“Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti? Nanga mdima umakhala kuti?
כִּי תִקָּחֶנּוּ אֶל־גְּבוּלוֹ וְכִי־תָבִין נְתִיבוֹת בֵּיתֽוֹ׃ | 20 |
Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi? Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
יָדַעְתָּ כִּי־אָז תִּוָּלֵד וּמִסְפַּר יָמֶיךָ רַבִּֽים׃ | 21 |
Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale! Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
הֲבָאתָ אֶל־אֹצְרוֹת שָׁלֶג וְאוֹצְרוֹת בָּרָד תִּרְאֶֽה׃ | 22 |
“Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
אֲשֶׁר־חָשַׂכְתִּי לְעֶת־צָר לְיוֹם קְרָב וּמִלְחָמָֽה׃ | 23 |
zimene ndazisungira nthawi ya mavuto ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
אֵי־זֶה הַדֶּרֶךְ יֵחָלֶק אוֹר יָפֵץ קָדִים עֲלֵי־אָֽרֶץ׃ | 24 |
Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
מִֽי־פִלַּג לַשֶּׁטֶף תְּעָלָה וְדֶרֶךְ לַחֲזִיז קֹלֽוֹת׃ | 25 |
Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula, nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
לְהַמְטִיר עַל־אֶרֶץ לֹא־אִישׁ מִדְבָּר לֹא־אָדָם בּֽוֹ׃ | 26 |
kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu, chipululu chopandamo munthu,
לְהַשְׂבִּיעַ שֹׁאָה וּמְשֹׁאָה וּלְהַצְמִיחַ מֹצָא דֶֽשֶׁא׃ | 27 |
kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa ndi kumeretsamo udzu?
הֲיֵשׁ־לַמָּטָר אָב אוֹ מִי־הוֹלִיד אֶגְלֵי־טָֽל׃ | 28 |
Kodi mvula ili ndi abambo ake? Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
מִבֶּטֶן מִי יָצָא הַקָּרַח וּכְפֹר שָׁמַיִם מִי יְלָדֽוֹ׃ | 29 |
Kodi madzi owundana anawabereka ndani? Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
כָּאֶבֶן מַיִם יִתְחַבָּאוּ וּפְנֵי תְהוֹם יִתְלַכָּֽדוּ׃ | 30 |
pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala, pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
הַֽתְקַשֵּׁר מַעֲדַנּוֹת כִּימָה אֽוֹ־מֹשְׁכוֹת כְּסִיל תְּפַתֵּֽחַ׃ | 31 |
“Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi? Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
הֲתֹצִיא מַזָּרוֹת בְּעִתּוֹ וְעַיִשׁ עַל־בָּנֶיהָ תַנְחֵֽם׃ | 32 |
Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
הֲיָדַעְתָּ חֻקּוֹת שָׁמָיִם אִם־תָּשִׂים מִשְׁטָרוֹ בָאָֽרֶץ׃ | 33 |
Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa? Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
הֲתָרִים לָעָב קוֹלֶךָ וְֽשִׁפְעַת־מַיִם תְּכַסֶּֽךָּ׃ | 34 |
“Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula?
הַֽתְשַׁלַּח בְּרָקִים וְיֵלֵכוּ וְיֹֽאמְרוּ לְךָ הִנֵּֽנוּ׃ | 35 |
Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime? Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
מִי־שָׁת בַּטֻּחוֹת חׇכְמָה אוֹ מִֽי־נָתַן לַשֶּׂכְוִי בִינָֽה׃ | 36 |
Kodi ndani anayika nzeru mu mtima, ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
מִֽי־יְסַפֵּר שְׁחָקִים בְּחׇכְמָה וְנִבְלֵי שָׁמַיִם מִי יַשְׁכִּֽיב׃ | 37 |
Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo? Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
בְּצֶקֶת עָפָר לַמּוּצָק וּרְגָבִים יְדֻבָּֽקוּ׃ | 38 |
pamene fumbi limasanduka matope, ndipo matopewo amawumbika?
הֲתָצוּד לְלָבִיא טָרֶף וְחַיַּת כְּפִירִים תְּמַלֵּֽא׃ | 39 |
“Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi ndi kukhutitsa misona ya mikango
כִּֽי־יָשֹׁחוּ בַמְּעוֹנוֹת יֵֽשְׁבוּ בַסֻּכָּה לְמוֹ־אָֽרֶב׃ | 40 |
pamene ili khale mʼmapanga mwawo kapena pamene ikubisala pa tchire?
מִי יָכִין לָעֹרֵב צֵידוֹ כִּֽי־יְלָדָו אֶל־אֵל יְשַׁוֵּעוּ יִתְעוּ לִבְלִי־אֹֽכֶל׃ | 41 |
Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani pamene ana ake akulirira kwa Mulungu ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?