< איוב 33 >

וְֽאוּלָם שְׁמַֽע־נָא אִיּוֹב מִלָּי וְֽכׇל־דְּבָרַי הַאֲזִֽינָה׃ 1
“Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga; mutcherere khutu zonse zimene ndinene.
הִנֵּה־נָא פָּתַחְתִּי פִי דִּבְּרָה לְשׁוֹנִי בְחִכִּֽי׃ 2
Tsopano ndiyamba kuyankhula; mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.
יֹשֶׁר־לִבִּי אֲמָרָי וְדַעַת שְׂפָתַי בָּרוּר מִלֵּֽלוּ׃ 3
Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama; pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.
רֽוּחַ־אֵל עָשָׂתְנִי וְנִשְׁמַת שַׁדַּי תְּחַיֵּֽנִי׃ 4
Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
אִם־תּוּכַל הֲשִׁיבֵנִי עֶרְכָהֿ לְפָנַי הִתְיַצָּֽבָה׃ 5
Mundiyankhe ngati mungathe; konzekani tsopano kuti munditsutse.
הֵן־אֲנִי כְפִיךָ לָאֵל מֵחֹמֶר קֹרַצְתִּי גַם־אָֽנִי׃ 6
Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi.
הִנֵּה אֵמָתִי לֹא תְבַעֲתֶךָּ וְאַכְפִּי עָלֶיךָ לֹֽא־יִכְבָּֽד׃ 7
Musachite mantha ndipo musandiope ayi, Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.
אַךְ אָמַרְתָּ בְאׇזְנָי וְקוֹל מִלִּין אֶשְׁמָֽע׃ 8
“Koma inu mwayankhula ine ndikumva, ndamva mawu anuwo onena kuti,
זַךְ אֲנִי בְּֽלִי ־ פָשַׁע חַ ף אָנֹכִי וְלֹא עָוֺן לִֽי׃ 9
‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo; ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.
הֵן תְּנוּאוֹת עָלַי יִמְצָא יַחְשְׁבֵנִי לְאוֹיֵב לֽוֹ׃ 10
Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo; Iye akundiyesa ngati mdani wake.
יָשֵׂם בַּסַּד רַגְלָי יִשְׁמֹר כׇּל־אׇרְחֹתָֽי׃ 11
Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’
הֶן־זֹאת לֹא־צָדַקְתָּ אֶעֱנֶךָּ כִּי־יִרְבֶּה אֱלוֹהַּ מֵאֱנֽוֹשׁ׃ 12
“Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi, pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
מַדּוּעַ אֵלָיו רִיבוֹתָ כִּי כׇל־דְּבָרָיו לֹא יַעֲנֶֽה׃ 13
Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?
כִּֽי־בְאַחַת יְדַבֶּר־אֵל וּבִשְׁתַּיִם לֹא יְשׁוּרֶֽנָּה׃ 14
Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana, ngakhale munthu sazindikira zimenezi.
בַּחֲלוֹם ׀ חֶזְיוֹן לַיְלָה בִּנְפֹל תַּרְדֵּמָה עַל־אֲנָשִׁים בִּתְנוּמוֹת עֲלֵי מִשְׁכָּֽב׃ 15
Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku, pamene anthu ali mʼtulo tofa nato pamene akungosinza chabe pa bedi,
אָז יִגְלֶה אֹזֶן אֲנָשִׁים וּבְמֹסָרָם יַחְתֹּֽם׃ 16
amawanongʼoneza mʼmakutu ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,
לְהָסִיר אָדָם מַעֲשֶׂה וְגֵוָה מִגֶּבֶר יְכַסֶּֽה׃ 17
kumuchotsa munthu ku zoyipa, ndi kuthetseratu kunyada kwake,
יַחְשֹׂךְ נַפְשׁוֹ מִנִּי־שָׁחַת וְחַיָּתוֹ מֵעֲבֹר בַּשָּֽׁלַח׃ 18
kumulanditsa munthu ku manda, kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.
וְהוּכַח בְּמַכְאוֹב עַל־מִשְׁכָּבוֹ (וריב) [וְרוֹב] עֲצָמָיו אֵתָֽן׃ 19
“Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake, nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,
וְזִהֲמַתּוּ חַיָּתוֹ לָחֶם וְנַפְשׁוֹ מַאֲכַל תַּאֲוָֽה׃ 20
kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya, ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.
יִכֶל בְּשָׂרוֹ מֵרֹאִי (ושפי) [וְשֻׁפּוּ] עַצְמֹתָיו לֹא רֻאּֽוּ׃ 21
Thupi lake limawonda ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.
וַתִּקְרַב לַשַּׁחַת נַפְשׁוֹ וְחַיָּתוֹ לַֽמְמִתִֽים׃ 22
Munthuyo amayandikira ku manda, moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.
אִם־יֵשׁ עָלָיו ׀ מַלְאָךְ מֵלִיץ אֶחָד מִנִּי־אָלֶף לְהַגִּיד לְאָדָם יׇשְׁרֽוֹ׃ 23
“Koma patakhala mngelo ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri oterewa, adzafotokoza zimene zili zoyenera,
וַיְחֻנֶּנּוּ וַיֹּאמֶר פְּדָעֵהוּ מֵרֶדֶת שָׁחַת מָצָאתִי כֹֽפֶר׃ 24
kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’
רֻֽטְפַשׁ בְּשָׂרוֹ מִנֹּעַר יָשׁוּב לִימֵי עֲלוּמָֽיו׃ 25
pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana; ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.
יֶעְתַּר אֶל־אֱלוֹהַּ ׀ וַיִּרְצֵהוּ וַיַּרְא פָּנָיו בִּתְרוּעָה וַיָּשֶׁב לֶאֱנוֹשׁ צִדְקָתֽוֹ׃ 26
Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa. Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.
יָשֹׁר ׀ עַל־אֲנָשִׁים וַיֹּאמֶר חָטָאתִי וְיָשָׁר הֶעֱוֵיתִי וְלֹא־שָׁוָה לִֽי׃ 27
Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti, ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama, koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
פָּדָה (נפשי) [נַפְשׁוֹ] מֵעֲבֹר בַּשָּׁחַת (וחיתי) [וְחַיָּתוֹ] בָּאוֹר תִּרְאֶֽה׃ 28
Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda, ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’
הֶן־כׇּל־אֵלֶּה יִפְעַל־אֵל פַּעֲמַיִם שָׁלוֹשׁ עִם־גָּֽבֶר׃ 29
“Mulungu amachita zonsezi kwa munthu kawirikawiri,
לְהָשִׁיב נַפְשׁוֹ מִנִּי־שָׁחַת לֵאוֹר בְּאוֹר הַחַיִּֽים׃ 30
kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda, kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.
הַקְשֵׁב אִיּוֹב שְֽׁמַֽע־לִי הַחֲרֵשׁ וְאָנֹכִי אֲדַבֵּֽר׃ 31
“Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere; khalani chete kuti ndiyankhule.
אִם־יֵשׁ־מִלִּין הֲשִׁיבֵנִי דַּבֵּר כִּֽי־חָפַצְתִּי צַדְּקֶֽךָּ׃ 32
Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni; yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.
אִם־אַיִן אַתָּה שְֽׁמַֽע־לִי הַחֲרֵשׁ וַאֲאַלֶּפְךָ חׇכְמָֽה׃ 33
Koma ngati sichoncho, mundimvere; khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”

< איוב 33 >