< איוב 24 >
מַדּוּעַ מִשַּׁדַּי לֹא־נִצְפְּנוּ עִתִּים וְיֹדְעָו לֹא־חָזוּ יָמָֽיו׃ | 1 |
“Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze? Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
גְּבֻלוֹת יַשִּׂיגוּ עֵדֶר גָּזְלוּ וַיִּרְעֽוּ׃ | 2 |
Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba.
חֲמוֹר יְתוֹמִים יִנְהָגוּ יַחְבְּלוּ שׁוֹר אַלְמָנָֽה׃ | 3 |
Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
יַטּוּ אֶבְיֹנִים מִדָּרֶךְ יַחַד חֻבְּאוּ עֲנִיֵּי־אָֽרֶץ׃ | 4 |
Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
הֵן פְּרָאִים ׀ בַּמִּדְבָּר יָצְאוּ בְּפׇעֳלָם מְשַׁחֲרֵי לַטָּרֶף עֲרָבָה לוֹ לֶחֶם לַנְּעָרִֽים׃ | 5 |
Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
בַּשָּׂדֶה בְּלִילוֹ (יקצירו) [יִקְצוֹרוּ] וְכֶרֶם רָשָׁע יְלַקֵּֽשׁוּ׃ | 6 |
Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
עָרוֹם יָלִינוּ מִבְּלִי לְבוּשׁ וְאֵין כְּסוּת בַּקָּרָֽה׃ | 7 |
Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
מִזֶּרֶם הָרִים יִרְטָבוּ וּֽמִבְּלִי מַחְסֶה חִבְּקוּ־צֽוּר׃ | 8 |
Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
יִגְזְלוּ מִשֹּׁד יָתוֹם וְֽעַל־עָנִי יַחְבֹּֽלוּ׃ | 9 |
Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
עָרוֹם הִלְּכוּ בְּלִי לְבוּשׁ וּרְעֵבִים נָשְׂאוּ עֹֽמֶר׃ | 10 |
Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
בֵּין־שׁוּרֹתָם יַצְהִירוּ יְקָבִים דָּרְכוּ וַיִּצְמָֽאוּ׃ | 11 |
Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa; amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
מֵעִיר מְתִים ׀ יִנְאָקוּ וְנֶֽפֶשׁ־חֲלָלִים תְּשַׁוֵּעַ וֶאֱלוֹהַּ לֹֽא־יָשִׂים תִּפְלָֽה׃ | 12 |
Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
הֵמָּה ׀ הָיוּ בְּֽמֹרְדֵי ־ אוֹר לֹא־הִכִּירוּ דְרָכָיו וְלֹא יָשְׁבוּ בִּנְתִיבֹתָֽיו׃ | 13 |
“Pali ena amene amakana kuwala, amene safuna kuyenda mʼkuwalako kapena kukhala mʼnjira zake.
לָאוֹר יָקוּם רוֹצֵחַ יִֽקְטׇל־עָנִי וְאֶבְיוֹן וּבַלַּיְלָה יְהִי כַגַּנָּֽב׃ | 14 |
Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
וְעֵין נֹאֵף ׀ שָׁמְרָֽה נֶשֶׁף לֵאמֹר לֹא־תְשׁוּרֵנִי עָיִן וְסֵתֶר פָּנִים יָשִֽׂים׃ | 15 |
Munthu wachigololo amadikira chisisira; iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’ ndipo amaphimba nkhope yake.
חָתַר בַּחֹשֶׁךְ בָּתִּים יוֹמָם חִתְּמוּ־לָמוֹ לֹא־יָדְעוּ אֽוֹר׃ | 16 |
Mbala zimathyola nyumba usiku, koma masana zimadzitsekera; izo zimathawa kuwala.
כִּי יַחְדָּו ׀ בֹּקֶר לָמוֹ צַלְמָוֶת כִּֽי־יַכִּיר בַּלְהוֹת צַלְמָֽוֶת׃ | 17 |
Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera. Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
קַל־הוּא ׀ עַל־פְּנֵי־מַיִם תְּקֻלַּל חֶלְקָתָם בָּאָרֶץ לֹא־יִפְנֶה דֶּרֶךְ כְּרָמִֽים׃ | 18 |
“Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi; minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
צִיָּה גַם־חֹם יִגְזְלוּ מֵֽימֵי־שֶׁלֶג שְׁאוֹל חָטָֽאוּ׃ (Sheol ) | 19 |
Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa. (Sheol )
יִשְׁכָּחֵהוּ רֶחֶם ׀ מְתָקוֹ רִמָּה עוֹד לֹֽא־יִזָּכֵר וַתִּשָּׁבֵר כָּעֵץ עַוְלָֽה׃ | 20 |
Mayi wowabereka amawayiwala, mphutsi zimasangalala powadya; anthu oyipa sakumbukiridwanso koma amathyoka ngati mtengo.
רֹעֶה עֲקָרָה לֹא תֵלֵד וְאַלְמָנָה לֹא יְיֵטִֽיב׃ | 21 |
Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana, ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
וּמָשַׁךְ אַבִּירִים בְּכֹחוֹ יָקוּם וְֽלֹא־יַאֲמִין בַּֽחַיִּֽין׃ | 22 |
Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake; ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
יִתֶּן־לוֹ לָבֶטַח וְיִשָּׁעֵן וְעֵינֵיהוּ עַל־דַּרְכֵיהֶֽם׃ | 23 |
Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka, koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
רוֹמּוּ מְּעַט ׀ וְֽאֵינֶנּוּ וְֽהֻמְּכוּ כַּכֹּל יִקָּפְצוּן וּכְרֹאשׁ שִׁבֹּלֶת יִמָּֽלוּ׃ | 24 |
Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso; amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse; amadulidwa ngati ngala za tirigu.
וְאִם־לֹא אֵפוֹ מִי יַכְזִיבֵנִי וְיָשֵׂם לְאַל מִלָּתִֽי׃ | 25 |
“Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”