< איוב 23 >

וַיַּעַן אִיּוֹב וַיֹּאמַֽר׃ 1
Pamenepo Yobu anayankha kuti,
גַּם־הַיּוֹם מְרִי שִׂחִי יָדִי כָּבְדָה עַל־אַנְחָתִֽי׃ 2
“Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri; Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.
מִֽי־יִתֵּן יָדַעְתִּי וְאֶמְצָאֵהוּ אָבוֹא עַד־תְּכוּנָתֽוֹ׃ 3
Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu; ndikanangopita kumene amakhalako!
אֶעֶרְכָה לְפָנָיו מִשְׁפָּט וּפִי אֲמַלֵּא תוֹכָחֽוֹת׃ 4
Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.
אֵדְעָה מִלִּים יַעֲנֵנִי וְאָבִינָה מַה־יֹּאמַר־לִֽי׃ 5
Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha, ndi kulingalira bwino zimene akananena!
הַבְּרׇב־כֹּחַ יָרִיב עִמָּדִי לֹא אַךְ־הוּא יָשִׂם בִּֽי׃ 6
Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu? Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.
שָׁם יָשָׁר נוֹכָח עִמּוֹ וַאֲפַלְּטָה לָנֶצַח מִשֹּׁפְטִֽי׃ 7
Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake, ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.
הֵן קֶדֶם אֶהֱלֹךְ וְאֵינֶנּוּ וְאָחוֹר וְֽלֹא־אָבִין לֽוֹ׃ 8
“Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko, ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.
שְׂמֹאול בַּעֲשֹׂתוֹ וְלֹא־אָחַז יַעְטֹף יָמִין וְלֹא אֶרְאֶֽה׃ 9
Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko akapita kummwera, sindimuona.
כִּֽי־יָדַע דֶּרֶךְ עִמָּדִי בְּחָנַנִי כַּזָּהָב אֵצֵֽא׃ 10
Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.
בַּאֲשֻׁרוֹ אָחֲזָה רַגְלִי דַּרְכּוֹ שָׁמַרְתִּי וְלֹא־אָֽט׃ 11
Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake; ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.
מִצְוַת שְׂפָתָיו וְלֹא אָמִישׁ מֵחֻקִּי צָפַנְתִּי אִמְרֵי־פִֽיו׃ 12
Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.
וְהוּא בְאֶחָד וּמִי יְשִׁיבֶנּוּ וְנַפְשׁוֹ אִוְּתָה וַיָּֽעַשׂ׃ 13
“Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye? Iye amachita chilichonse chimene wafuna.
כִּי יַשְׁלִים חֻקִּי וְכָהֵנָּה רַבּוֹת עִמּֽוֹ׃ 14
Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire, ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.
עַל־כֵּן מִפָּנָיו אֶבָּהֵל אֶתְבּוֹנֵן וְאֶפְחַד מִמֶּֽנּוּ׃ 15
Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake; ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.
וְאֵל הֵרַךְ לִבִּי וְשַׁדַּי הִבְהִילָֽנִי׃ 16
Mulungu walefula mtima wanga; Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.
כִּֽי־לֹא נִצְמַתִּי מִפְּנֵי־חֹשֶׁךְ וּמִפָּנַי כִּסָּה־אֹֽפֶל׃ 17
Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima, ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.

< איוב 23 >