< ירמיה 10 >

שִׁמְעוּ אֶת־הַדָּבָר אֲשֶׁר דִּבֶּר יְהֹוָה עֲלֵיכֶם בֵּית יִשְׂרָאֵֽל׃ 1
Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena.
כֹּה ׀ אָמַר יְהֹוָה אֶל־דֶּרֶךְ הַגּוֹיִם אַל־תִּלְמָדוּ וּמֵאֹתוֹת הַשָּׁמַיִם אַל־תֵּחָתּוּ כִּי־יֵחַתּוּ הַגּוֹיִם מֵהֵֽמָּה׃ 2
Yehova akuti, “Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
כִּֽי־חֻקּוֹת הָעַמִּים הֶבֶל הוּא כִּי־עֵץ מִיַּעַר כְּרָתוֹ מַעֲשֵׂה יְדֵי־חָרָשׁ בַּֽמַּעֲצָֽד׃ 3
Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe. Iwo amakadula mtengo ku nkhalango ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
בְּכֶסֶף וּבְזָהָב יְיַפֵּהוּ בְּמַסְמְרוֹת וּבְמַקָּבוֹת יְחַזְּקוּם וְלוֹא יָפִֽיק׃ 4
Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke.
כְּתֹמֶר מִקְשָׁה הֵמָּה וְלֹא יְדַבֵּרוּ נָשׂוֹא יִנָּשׂוּא כִּי לֹא יִצְעָדוּ אַל־תִּֽירְאוּ מֵהֶם כִּי־לֹא יָרֵעוּ וְגַם־הֵיטֵיב אֵין אוֹתָֽם׃ 5
Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka. Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe ndipo ayenera kunyamulidwa popeza sangathe nʼkuyenda komwe. Musachite nawo mantha popeza sangathe kukuchitani choyipa ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
מֵאֵין כָּמוֹךָ יְהֹוָה גָּדוֹל אַתָּה וְגָדוֹל שִׁמְךָ בִּגְבוּרָֽה׃ 6
Palibe wofanana nanu, Inu Yehova; Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
מִי לֹא יִרָֽאֲךָ מֶלֶךְ הַגּוֹיִם כִּי לְךָ יָאָתָה כִּי בְכׇל־חַכְמֵי הַגּוֹיִם וּבְכׇל־מַלְכוּתָם מֵאֵין כָּמֽוֹךָ׃ 7
Ndani amene angaleke kukuopani, inu Mfumu ya mitundu ya anthu? Chimenechi ndicho chokuyenerani. Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse a mitundu ya anthu, palibe wina wofanana nanu.
וּבְאַחַת יִבְעֲרוּ וְיִכְסָלוּ מוּסַר הֲבָלִים עֵץ הֽוּא׃ 8
Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru; malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
כֶּסֶף מְרֻקָּע מִתַּרְשִׁישׁ יוּבָא וְזָהָב מֵֽאוּפָז מַעֲשֵׂה חָרָשׁ וִידֵי צוֹרֵף תְּכֵלֶת וְאַרְגָּמָן לְבוּשָׁם מַעֲשֵׂה חֲכָמִים כֻּלָּֽם׃ 9
Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
וַיהֹוָה אֱלֹהִים אֱמֶת הֽוּא־אֱלֹהִים חַיִּים וּמֶלֶךְ עוֹלָם מִקִּצְפּוֹ תִּרְעַשׁ הָאָרֶץ וְלֹֽא־יָכִלוּ גוֹיִם זַעְמֽוֹ׃ 10
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya. Akakwiya, dziko limagwedezeka; anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.
כִּדְנָה תֵּאמְרוּן לְהוֹם אֱלָהַיָּא דִּֽי־שְׁמַיָּא וְאַרְקָא לָא עֲבַדוּ יֵאבַדוּ מֵאַרְעָא וּמִן־תְּחוֹת שְׁמַיָּא אֵֽלֶּה׃ 11
“Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’”
עֹשֵׂה אֶרֶץ בְּכֹחוֹ מֵכִין תֵּבֵל בְּחׇכְמָתוֹ וּבִתְבוּנָתוֹ נָטָה שָׁמָֽיִם׃ 12
Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.
לְקוֹל תִּתּוֹ הֲמוֹן מַיִם בַּשָּׁמַיִם וַיַּעֲלֶה נְשִׂאִים מִקְצֵה (ארץ) [הָאָרֶץ] בְּרָקִים לַמָּטָר עָשָׂה וַיּוֹצֵא רוּחַ מֵאֹצְרֹתָֽיו׃ 13
Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba; Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.
נִבְעַר כׇּל־אָדָם מִדַּעַת הֹבִישׁ כׇּל־צוֹרֵף מִפָּסֶל כִּי שֶׁקֶר נִסְכּוֹ וְלֹא־רוּחַ בָּֽם׃ 14
Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo.
הֶבֶל הֵמָּה מַעֲשֵׂה תַּעְתֻּעִים בְּעֵת פְּקֻדָּתָם יֹאבֵֽדוּ׃ 15
Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
לֹא־כְאֵלֶּה חֵלֶק יַעֲקֹב כִּֽי־יוֹצֵר הַכֹּל הוּא וְיִשְׂרָאֵל שֵׁבֶט נַחֲלָתוֹ יְהֹוָה צְבָאוֹת שְׁמֽוֹ׃ 16
Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
אִסְפִּי מֵאֶרֶץ כִּנְעָתֵךְ (ישבתי) [יֹשֶׁבֶת] בַּמָּצֽוֹר׃ 17
Sonkhanitsani katundu wanu, inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
כִּי־כֹה אָמַר יְהֹוָה הִנְנִי קוֹלֵעַ אֶת־יוֹשְׁבֵי הָאָרֶץ בַּפַּעַם הַזֹּאת וַהֲצֵרֹתִי לָהֶם לְמַעַן יִמְצָֽאוּ׃ 18
Pakuti Yehova akuti, “Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse amene akukhala mʼdziko lino; adzakhala pa mavuto mpaka adzamvetsa.”
אוֹי לִי עַל־שִׁבְרִי נַחְלָה מַכָּתִי וַאֲנִי אָמַרְתִּי אַךְ זֶה חֳלִי וְאֶשָּׂאֶֽנּוּ׃ 19
Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga! Chilonda changa nʼchachikulu!” Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi, choncho ndingolipirira.”
אׇהֳלִי שֻׁדָּד וְכׇל־מֵיתָרַי נִתָּקוּ בָּנַי יְצָאֻנִי וְאֵינָם אֵין־נֹטֶה עוֹד אׇהֳלִי וּמֵקִים יְרִיעוֹתָֽי׃ 20
Tenti yanga yawonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso amene adzandimangire tenti, kapena kufunyulula nsalu yake.
כִּי נִבְעֲרוּ הָרֹעִים וְאֶת־יְהֹוָה לֹא דָרָשׁוּ עַל־כֵּן לֹא הִשְׂכִּילוּ וְכׇל־מַרְעִיתָם נָפֽוֹצָה׃ 21
Abusa ndi opusa ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova; choncho palibe chimene anapindula ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
קוֹל שְׁמוּעָה הִנֵּה בָאָה וְרַעַשׁ גָּדוֹל מֵאֶרֶץ צָפוֹן לָשׂוּם אֶת־עָרֵי יְהוּדָה שְׁמָמָה מְעוֹן תַּנִּֽים׃ 22
Tamvani! kukubwera mphekesera, phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto! Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda, malo okhala nkhandwe.
יָדַעְתִּי יְהֹוָה כִּי לֹא לָאָדָם דַּרְכּוֹ לֹֽא־לְאִישׁ הֹלֵךְ וְהָכִין אֶֽת־צַעֲדֽוֹ׃ 23
Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake; munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
יַסְּרֵנִי יְהֹוָה אַךְ־בְּמִשְׁפָּט אַל־בְּאַפְּךָ פֶּן־תַּמְעִטֵֽנִי׃ 24
Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo, osati ndi mkwiyo wanu, mungandiwononge kotheratu.
שְׁפֹךְ חֲמָתְךָ עַל־הַגּוֹיִם אֲשֶׁר לֹֽא־יְדָעוּךָ וְעַל מִשְׁפָּחוֹת אֲשֶׁר בְּשִׁמְךָ לֹא קָרָאוּ כִּֽי־אָכְלוּ אֶֽת־יַעֲקֹב וַֽאֲכָלֻהוּ וַיְכַלֻּהוּ וְאֶת־נָוֵהוּ הֵשַֽׁמּוּ׃ 25
Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani, ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba. Iwo aja anasakaza Yakobo; amusakaza kotheratu ndipo awononga dziko lake.

< ירמיה 10 >