< ישעה 60 >
קוּמִי אוֹרִי כִּי בָא אוֹרֵךְ וּכְבוֹד יְהֹוָה עָלַיִךְ זָרָֽח׃ | 1 |
“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
כִּֽי־הִנֵּה הַחֹשֶׁךְ יְכַסֶּה־אֶרֶץ וַעֲרָפֶל לְאֻמִּים וְעָלַיִךְ יִזְרַח יְהֹוָה וּכְבוֹדוֹ עָלַיִךְ יֵרָאֶֽה׃ | 2 |
Taona, mdima waphimba dziko lapansi ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina, koma Yehova adzakuwalira iwe, ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
וְהָלְכוּ גוֹיִם לְאוֹרֵךְ וּמְלָכִים לְנֹגַהּ זַרְחֵֽךְ׃ | 3 |
Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
שְׂאִֽי־סָבִיב עֵינַיִךְ וּרְאִי כֻּלָּם נִקְבְּצוּ בָֽאוּ־לָךְ בָּנַיִךְ מֵרָחוֹק יָבֹאוּ וּבְנוֹתַיִךְ עַל־צַד תֵּאָמַֽנָה׃ | 4 |
“Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika. Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe; ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
אָז תִּרְאִי וְנָהַרְתְּ וּפָחַד וְרָחַב לְבָבֵךְ כִּֽי־יֵהָפֵךְ עָלַיִךְ הֲמוֹן יָם חֵיל גּוֹיִם יָבֹאוּ לָֽךְ׃ | 5 |
Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
שִֽׁפְעַת גְּמַלִּים תְּכַסֵּךְ בִּכְרֵי מִדְיָן וְעֵיפָה כֻּלָּם מִשְּׁבָא יָבֹאוּ זָהָב וּלְבוֹנָה יִשָּׂאוּ וּתְהִלֹּת יְהֹוָה יְבַשֵּֽׂרוּ׃ | 6 |
Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova.
כׇּל־צֹאן קֵדָר יִקָּבְצוּ לָךְ אֵילֵי נְבָיוֹת יְשָֽׁרְתוּנֶךְ יַעֲלוּ עַל־רָצוֹן מִזְבְּחִי וּבֵית תִּפְאַרְתִּי אֲפָאֵֽר׃ | 7 |
Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu, nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani; zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe, ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
מִי־אֵלֶּה כָּעָב תְּעוּפֶינָה וְכַיּוֹנִים אֶל־אֲרֻבֹּתֵיהֶֽם׃ | 8 |
“Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo, ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
כִּי־לִי ׀ אִיִּים יְקַוּוּ וׇֽאֳנִיּוֹת תַּרְשִׁישׁ בָּרִאשֹׁנָה לְהָבִיא בָנַיִךְ מֵֽרָחוֹק כַּסְפָּם וּזְהָבָם אִתָּם לְשֵׁם יְהֹוָה אֱלֹהַיִךְ וְלִקְדוֹשׁ יִשְׂרָאֵל כִּי פֵאֲרָֽךְ׃ | 9 |
Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali; patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi, zikubweretsa ana ako ochokera kutali, pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo, kudzalemekeza Yehova Mulungu wako, Woyerayo wa Israeli, pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
וּבָנוּ בְנֵֽי־נֵכָר חֹמֹתַיִךְ וּמַלְכֵיהֶם יְשָֽׁרְתוּנֶךְ כִּי בְקִצְפִּי הִכִּיתִיךְ וּבִרְצוֹנִי רִחַמְתִּֽיךְ׃ | 10 |
“Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu awo adzakutumikira. Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
וּפִתְּחוּ שְׁעָרַיִךְ תָּמִיד יוֹמָם וָלַיְלָה לֹא יִסָּגֵרוּ לְהָבִיא אֵלַיִךְ חֵיל גּוֹיִם וּמַלְכֵיהֶם נְהוּגִֽים׃ | 11 |
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse, sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku, kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo, akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
כִּֽי־הַגּוֹי וְהַמַּמְלָכָה אֲשֶׁר לֹא־יַעַבְדוּךְ יֹאבֵדוּ וְהַגּוֹיִם חָרֹב יֶחֱרָֽבוּ׃ | 12 |
Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe; adzawonongeka kotheratu.
כְּבוֹד הַלְּבָנוֹן אֵלַיִךְ יָבוֹא בְּרוֹשׁ תִּדְהָר וּתְאַשּׁוּר יַחְדָּו לְפָאֵר מְקוֹם מִקְדָּשִׁי וּמְקוֹם רַגְלַי אֲכַבֵּֽד׃ | 13 |
“Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini, mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika; ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
וְהָלְכוּ אֵלַיִךְ שְׁחוֹחַ בְּנֵי מְעַנַּיִךְ וְהִֽשְׁתַּחֲווּ עַל־כַּפּוֹת רַגְלַיִךְ כׇּל־מְנַֽאֲצָיִךְ וְקָרְאוּ לָךְ עִיר יְהֹוָה צִיּוֹן קְדוֹשׁ יִשְׂרָאֵֽל׃ | 14 |
Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani; onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu. Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova; Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
תַּחַת הֱיוֹתֵךְ עֲזוּבָה וּשְׂנוּאָה וְאֵין עוֹבֵר וְשַׂמְתִּיךְ לִגְאוֹן עוֹלָם מְשׂוֹשׂ דּוֹר וָדֽוֹר׃ | 15 |
“Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe, koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe cha anthu amibado yonse.
וְיָנַקְתְּ חֲלֵב גּוֹיִם וְשֹׁד מְלָכִים תִּינָקִי וְיָדַעַתְּ כִּי אֲנִי יְהֹוָה מֽוֹשִׁיעֵךְ וְגֹאֲלֵךְ אֲבִיר יַעֲקֹֽב׃ | 16 |
Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu ndi kuleredwa pa maere aufumu, motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako, Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
תַּחַת הַנְּחֹשֶׁת אָבִיא זָהָב וְתַחַת הַבַּרְזֶל אָבִיא כֶסֶף וְתַחַת הָעֵצִים נְחֹשֶׁת וְתַחַת הָאֲבָנִים בַּרְזֶל וְשַׂמְתִּי פְקֻדָּתֵךְ שָׁלוֹם וְנֹגְשַׂיִךְ צְדָקָֽה׃ | 17 |
Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa, ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo. Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala. Olamulira ako adzakhala a mtendere. Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
לֹא־יִשָּׁמַע עוֹד חָמָס בְּאַרְצֵךְ שֹׁד וָשֶׁבֶר בִּגְבוּלָיִךְ וְקָרָאת יְשׁוּעָה חוֹמֹתַיִךְ וּשְׁעָרַיִךְ תְּהִלָּֽה׃ | 18 |
Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako, bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako, ndidzakhala malinga ako okuteteza ndipo udzanditamanda.
לֹא־יִֽהְיֶה־לָּךְ עוֹד הַשֶּׁמֶשׁ לְאוֹר יוֹמָם וּלְנֹגַהּ הַיָּרֵחַ לֹא־יָאִיר לָךְ וְהָֽיָה־לָךְ יְהֹוָה לְאוֹר עוֹלָם וֵאלֹהַיִךְ לְתִפְאַרְתֵּֽךְ׃ | 19 |
Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
לֹא־יָבוֹא עוֹד שִׁמְשֵׁךְ וִירֵחֵךְ לֹא יֵֽאָסֵף כִּי יְהֹוָה יִֽהְיֶה־לָּךְ לְאוֹר עוֹלָם וְשָׁלְמוּ יְמֵי אֶבְלֵֽךְ׃ | 20 |
Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzazimiriranso; Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya, ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
וְעַמֵּךְ כֻּלָּם צַדִּיקִים לְעוֹלָם יִירְשׁוּ אָרֶץ נֵצֶר (מטעו) [מַטָּעַי] מַעֲשֵׂה יָדַי לְהִתְפָּאֵֽר׃ | 21 |
Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.
הַקָּטֹן יִהְיֶה לָאֶלֶף וְהַצָּעִיר לְגוֹי עָצוּם אֲנִי יְהֹוָה בְּעִתָּהּ אֲחִישֶֽׁנָּה׃ | 22 |
Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko, kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu. Ine ndine Yehova, nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”