< ישעה 51 >

שִׁמְעוּ אֵלַי רֹדְפֵי צֶדֶק מְבַקְשֵׁי יְהֹוָה הַבִּיטוּ אֶל־צוּר חֻצַּבְתֶּם וְאֶל־מַקֶּבֶת בּוֹר נֻקַּרְתֶּֽם׃ 1
“Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso ndiponso amene mumafunafuna Yehova: Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
הַבִּיטוּ אֶל־אַבְרָהָם אֲבִיכֶם וְאֶל־שָׂרָה תְּחוֹלֶלְכֶם כִּֽי־אֶחָד קְרָאתִיו וַאֲבָרְכֵהוּ וְאַרְבֵּֽהוּ׃ 2
taganizani za Abrahamu, kholo lanu, ndi Sara, amene anakubalani. Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana, koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
כִּֽי־נִחַם יְהֹוָה צִיּוֹן נִחַם כׇּל־חׇרְבֹתֶיהָ וַיָּשֶׂם מִדְבָּרָהּ כְּעֵדֶן וְעַרְבָתָהּ כְּגַן־יְהֹוָה שָׂשׂוֹן וְשִׂמְחָה יִמָּצֵא בָהּ תּוֹדָה וְקוֹל זִמְרָֽה׃ 3
Yehova adzatonthozadi Ziyoni, ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse; Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni, malo ake owuma ngati munda wa Yehova. Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda ndi kundiyamika.
הַקְשִׁיבוּ אֵלַי עַמִּי וּלְאוּמִּי אֵלַי הַאֲזִינוּ כִּי תוֹרָה מֵאִתִּי תֵצֵא וּמִשְׁפָּטִי לְאוֹר עַמִּים אַרְגִּֽיעַ׃ 4
“Mverani Ine, anthu anga: tcherani khutu, inu mtundu wanga: malangizo adzachokera kwa Ine; cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
קָרוֹב צִדְקִי יָצָא יִשְׁעִי וּזְרֹעַי עַמִּים יִשְׁפֹּטוּ אֵלַי אִיִּים יְקַוּוּ וְאֶל־זְרֹעִי יְיַחֵלֽוּן׃ 5
Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga. Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga; ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse. Mayiko akutali akundiyembekezera. Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
שְׂאוּ לַשָּׁמַיִם עֵֽינֵיכֶם וְֽהַבִּיטוּ אֶל־הָאָרֶץ מִתַּחַת כִּֽי־שָׁמַיִם כֶּעָשָׁן נִמְלָחוּ וְהָאָרֶץ כַּבֶּגֶד תִּבְלֶה וְיֹשְׁבֶיהָ כְּמוֹ־כֵן יְמוּתוּן וִישֽׁוּעָתִי לְעוֹלָם תִּֽהְיֶה וְצִדְקָתִי לֹא תֵחָֽת׃ 6
Kwezani maso anu mlengalenga, yangʼanani pansi pa dziko; mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
שִׁמְעוּ אֵלַי יֹדְעֵי צֶדֶק עַם תּוֹרָתִי בְלִבָּם אַל־תִּֽירְאוּ חֶרְפַּת אֱנוֹשׁ וּמִגִּדֻּפֹתָם אַל־תֵּחָֽתּוּ׃ 7
“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi, anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu; musaope kudzudzulidwa ndi anthu kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
כִּי כַבֶּגֶד יֹאכְלֵם עָשׁ וְכַצֶּמֶר יֹאכְלֵם סָס וְצִדְקָתִי לְעוֹלָם תִּֽהְיֶה וִישׁוּעָתִי לְדוֹר דּוֹרִֽים׃ 8
Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala; mbozi idzawadya ngati thonje. Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya, chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
עוּרִי עוּרִי לִבְשִׁי־עֹז זְרוֹעַ יְהֹוָה עוּרִי כִּימֵי קֶדֶם דֹּרוֹת עוֹלָמִים הֲלוֹא אַתְּ־הִיא הַמַּחְצֶבֶת רַהַב מְחוֹלֶלֶת תַּנִּֽין׃ 9
Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe, Inu Yehova; dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana, monga nthawi ya mibado yakale. Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe, amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?
הֲלוֹא אַתְּ־הִיא הַמַּחֲרֶבֶת יָם מֵי תְּהוֹם רַבָּה הַשָּׂמָה מַֽעֲמַקֵּי־יָם דֶּרֶךְ לַעֲבֹר גְּאוּלִֽים׃ 10
Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu, madzi ozama kwambiri aja? Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama, kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
וּפְדוּיֵי יְהֹוָה יְשׁוּבוּן וּבָאוּ צִיּוֹן בְּרִנָּה וְשִׂמְחַת עוֹלָם עַל־רֹאשָׁם שָׂשׂוֹן וְשִׂמְחָה יַשִּׂיגוּן נָסוּ יָגוֹן וַאֲנָחָֽה׃ 11
Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa; chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe, chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
אָנֹכִי אָנֹכִי הוּא מְנַחֶמְכֶם מִי־אַתְּ וַתִּֽירְאִי מֵאֱנוֹשׁ יָמוּת וּמִבֶּן־אָדָם חָצִיר יִנָּתֵֽן׃ 12
Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima. Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa? Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
וַתִּשְׁכַּח יְהֹוָה עֹשֶׂךָ נוֹטֶה שָׁמַיִם וְיֹסֵד אָרֶץ וַתְּפַחֵד תָּמִיד כׇּל־הַיּוֹם מִפְּנֵי חֲמַת הַמֵּצִיק כַּאֲשֶׁר כּוֹנֵן לְהַשְׁחִית וְאַיֵּה חֲמַת הַמֵּצִֽיק׃ 13
Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu, amene anayala za mlengalenga ndi kuyika maziko a dziko lapansi. Inu nthawi zonse mumaopsezedwa chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani amene angofuna kukuwonongani. Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
מִהַר צֹעֶה לְהִפָּתֵחַ וְלֹא־יָמוּת לַשַּׁחַת וְלֹא יֶחְסַר לַחְמֽוֹ׃ 14
Amʼndende adzamasulidwa posachedwa; sadzalowa mʼmanda awo, kapena kusowa chakudya.
וְאָֽנֹכִי יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ רֹגַע הַיָּם וַיֶּהֱמוּ גַּלָּיו יְהֹוָה צְבָאוֹת שְׁמֽוֹ׃ 15
Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
וָאָשִׂם דְּבָרַי בְּפִיךָ וּבְצֵל יָדִי כִּסִּיתִיךָ לִנְטֹעַ שָׁמַיִם וְלִיסֹד אָרֶץ וְלֵאמֹר לְצִיּוֹן עַמִּי־אָֽתָּה׃ 16
Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa. Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga, ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi, ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’”
הִתְעוֹרְרִי הִֽתְעוֹרְרִי קוּמִי יְרוּשָׁלַ͏ִם אֲשֶׁר שָׁתִית מִיַּד יְהֹוָה אֶת־כּוֹס חֲמָתוֹ אֶת־קֻבַּעַת כּוֹס הַתַּרְעֵלָה שָׁתִית מָצִֽית׃ 17
Dzambatuka, dzambatuka! Imirira iwe Yerusalemu. Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo chimene Yehova anakupatsa. Iwe amene unagugudiza chikho chochititsa chizwezwe.
אֵין־מְנַהֵל לָהּ מִכׇּל־בָּנִים יָלָדָה וְאֵין מַחֲזִיק בְּיָדָהּ מִכׇּל־בָּנִים גִּדֵּֽלָה׃ 18
Mwa ana onse amene anabereka, panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera; mwa ana onse amene analera, panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
שְׁתַּיִם הֵנָּה קֹרְאֹתַיִךְ מִי יָנוּד לָךְ הַשֹּׁד וְהַשֶּׁבֶר וְהָרָעָב וְהַחֶרֶב מִי אֲנַחֲמֵֽךְ׃ 19
Mavuto awiriwa akugwera iwe. Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga. Ndani angakumvere chisoni? Ndani angakutonthoze?
בָּנַיִךְ עֻלְּפוּ שָׁכְבוּ בְּרֹאשׁ כׇּל־חוּצוֹת כְּתוֹא מִכְמָר הַֽמְלֵאִים חֲמַת־יְהֹוָה גַּעֲרַת אֱלֹהָֽיִךְ׃ 20
Ana ako akomoka; ali lambalamba pa msewu, ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde. Ukali wa Yehova ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
לָכֵן שִׁמְעִי־נָא זֹאת עֲנִיָּה וּשְׁכֻרַת וְלֹא מִיָּֽיִן׃ 21
Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika, iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
כֹּה־אָמַר אֲדֹנַיִךְ יְהֹוָה וֵאלֹהַיִךְ יָרִיב עַמּוֹ הִנֵּה לָקַחְתִּי מִיָּדֵךְ אֶת־כּוֹס הַתַּרְעֵלָה אֶת־קֻבַּעַת כּוֹס חֲמָתִי לֹא־תוֹסִיפִי לִשְׁתּוֹתָהּ עֽוֹד׃ 22
Ambuye Yehova wanu, Mulungu amene amateteza anthu ake akuti, “Taona, ndachotsa mʼdzanja lako chikho chimene chimakuchititsa kudzandira; sudzamwanso chikho cha ukali wanga.
וְשַׂמְתִּיהָ בְּיַד־מוֹגַיִךְ אֲשֶׁר־אָמְרוּ לְנַפְשֵׁךְ שְׁחִי וְנַעֲבֹרָה וַתָּשִׂימִי כָאָרֶץ גֵּוֵךְ וְכַחוּץ לַעֹבְרִֽים׃ 23
Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza, amene ankakuwuza kuti, ‘gona pansi tikuyende pa msana.’ Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo, ngati msewu woti ayendepo.”

< ישעה 51 >