< ישעה 40 >

נַחֲמוּ נַחֲמוּ עַמִּי יֹאמַר אֱלֹֽהֵיכֶֽם׃ 1
Atonthozeni, atonthozeni anthu anga, akutero Mulungu wanu.
דַּבְּרוּ עַל־לֵב יְרוּשָׁלַ͏ִם וְקִרְאוּ אֵלֶיהָ כִּי מָֽלְאָה צְבָאָהּ כִּי נִרְצָה עֲוֺנָהּ כִּי לָֽקְחָה מִיַּד יְהֹוָה כִּפְלַיִם בְּכׇל־חַטֹּאתֶֽיהָ׃ 2
Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu ndipo muwawuzitse kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha, tchimo lawo lakhululukidwa. Ndawalanga mokwanira chifukwa cha machimo awo onse.
קוֹל קוֹרֵא בַּמִּדְבָּר פַּנּוּ דֶּרֶךְ יְהֹוָה יַשְּׁרוּ בָּעֲרָבָה מְסִלָּה לֵאלֹהֵֽינוּ׃ 3
Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti, “Konzani njira ya Yehova mʼchipululu; wongolani njira zake; msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
כׇּל־גֶּיא יִנָּשֵׂא וְכׇל־הַר וְגִבְעָה יִשְׁפָּלוּ וְהָיָה הֶֽעָקֹב לְמִישׁוֹר וְהָרְכָסִים לְבִקְעָֽה׃ 4
Chigwa chilichonse achidzaze. Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse; Dziko lokumbikakumbika alisalaze, malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
וְנִגְלָה כְּבוֹד יְהֹוָה וְרָאוּ כׇל־בָּשָׂר יַחְדָּו כִּי פִּי יְהֹוָה דִּבֵּֽר׃ 5
Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera, ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona, pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
קוֹל אֹמֵר קְרָא וְאָמַר מָה אֶקְרָא כׇּל־הַבָּשָׂר חָצִיר וְכׇל־חַסְדּוֹ כְּצִיץ הַשָּׂדֶֽה׃ 6
Wina ananena kuti, “Lengeza.” Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani? “Pakuti anthu onse ali ngati udzu ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
יָבֵשׁ חָצִיר נָבֵֽל־צִיץ כִּי רוּחַ יְהֹוָה נָשְׁבָה בּוֹ אָכֵן חָצִיר הָעָֽם׃ 7
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.” Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
יָבֵשׁ חָצִיר נָבֵֽל צִיץ וּדְבַר־אֱלֹהֵינוּ יָקוּם לְעוֹלָֽם׃ 8
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
עַל הַר־גָּבֹהַּ עֲלִי־לָךְ מְבַשֶּׂרֶת צִיּוֹן הָרִימִי בַכֹּחַ קוֹלֵךְ מְבַשֶּׂרֶת יְרוּשָׁלָ͏ִם הָרִימִי אַל־תִּירָאִי אִמְרִי לְעָרֵי יְהוּדָה הִנֵּה אֱלֹהֵיכֶֽם׃ 9
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni, kwera pa phiri lalitali. Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu, fuwula kwambiri, kweza mawu, usachite mantha; uza mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera!”
הִנֵּה אֲדֹנָי יֱהֹוִה בְּחָזָק יָבוֹא וּזְרֹעוֹ מֹשְׁלָה לוֹ הִנֵּה שְׂכָרוֹ אִתּוֹ וּפְעֻלָּתוֹ לְפָנָֽיו׃ 10
Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu, ndipo dzanja lake likulamulira, taonani akubwera ndi mphotho yake watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
כְּרֹעֶה עֶדְרוֹ יִרְעֶה בִּזְרֹעוֹ יְקַבֵּץ טְלָאִים וּבְחֵיקוֹ יִשָּׂא עָלוֹת יְנַהֵֽל׃ 11
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
מִֽי־מָדַד בְּשׇׁעֳלוֹ מַיִם וְשָׁמַיִם בַּזֶּרֶת תִּכֵּן וְכָל בַּשָּׁלִשׁ עֲפַר הָאָרֶץ וְשָׁקַל בַּפֶּלֶס הָרִים וּגְבָעוֹת בְּמֹאזְנָֽיִם׃ 12
Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu, kapena kuyeza kulemera kwa mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
מִֽי־תִכֵּן אֶת־רוּחַ יְהֹוָה וְאִישׁ עֲצָתוֹ יוֹדִיעֶֽנּוּ׃ 13
Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
אֶת־מִי נוֹעָץ וַיְבִינֵהוּ וַֽיְלַמְּדֵהוּ בְּאֹרַח מִשְׁפָּט וַיְלַמְּדֵהוּ דַעַת וְדֶרֶךְ תְּבוּנוֹת יוֹדִיעֶֽנּוּ׃ 14
Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya, kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru? Iye anapempha nzeru kwa yani ndi njira ya kumvetsa zinthu?
הֵן גּוֹיִם כְּמַר מִדְּלִי וּכְשַׁחַק מֹאזְנַיִם נֶחְשָׁבוּ הֵן אִיִּים כַּדַּק יִטּֽוֹל׃ 15
Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko. Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo; mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
וּלְבָנוֹן אֵין דֵּי בָּעֵר וְחַיָּתוֹ אֵין דֵּי עוֹלָֽה׃ 16
Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe, ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
כׇּל־הַגּוֹיִם כְּאַיִן נֶגְדּוֹ מֵאֶפֶס וָתֹהוּ נֶחְשְׁבוּ־לֽוֹ׃ 17
Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake; Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu ndi cha chabechabe.
וְאֶל־מִי תְּדַמְּיוּן אֵל וּמַה־דְּמוּת תַּעַרְכוּ לֽוֹ׃ 18
Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
הַפֶּסֶל נָסַךְ חָרָשׁ וְצֹרֵף בַּזָּהָב יְרַקְּעֶנּוּ וּרְתֻקוֹת כֶּסֶף צוֹרֵֽף׃ 19
Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide naliveka mkanda wasiliva.
הַֽמְסֻכָּן תְּרוּמָה עֵץ לֹא־יִרְקַב יִבְחָר חָרָשׁ חָכָם יְבַקֶּשׁ־לוֹ לְהָכִין פֶּסֶל לֹא יִמּֽוֹט׃ 20
Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere amasankha mtengo umene sudzawola, nafunafuna mʼmisiri waluso woti amupangire fano limene silingasunthike.
הֲלוֹא תֵֽדְעוּ הֲלוֹא תִשְׁמָעוּ הֲלוֹא הֻגַּד מֵרֹאשׁ לָכֶם הֲלוֹא הֲבִינוֹתֶם מוֹסְדוֹת הָאָֽרֶץ׃ 21
Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe? Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
הַיֹּשֵׁב עַל־חוּג הָאָרֶץ וְיֹשְׁבֶיהָ כַּחֲגָבִים הַנּוֹטֶה כַדֹּק שָׁמַיִם וַיִּמְתָּחֵם כָּאֹהֶל לָשָֽׁבֶת׃ 22
Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi, Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala. Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga, nayikunga ngati tenti yokhalamo.
הַנּוֹתֵן רוֹזְנִים לְאָיִן שֹׁפְטֵי אֶרֶץ כַּתֹּהוּ עָשָֽׂה׃ 23
Amatsitsa pansi mafumu amphamvu nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
אַף בַּל־נִטָּעוּ אַף בַּל־זֹרָעוּ אַף בַּל־שֹׁרֵשׁ בָּאָרֶץ גִּזְעָם וְגַם־נָשַׁף בָּהֶם וַיִּבָשׁוּ וּסְעָרָה כַּקַּשׁ תִּשָּׂאֵֽם׃ 24
Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene kapena kufesedwa chapompano, ndi kungoyamba kuzika mizu kumene ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
וְאֶל־מִי תְדַמְּיוּנִי וְאֶשְׁוֶה יֹאמַר קָדֽוֹשׁ׃ 25
Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani? Kapena kodi alipo wofanana nane?”
שְׂאוּ־מָרוֹם עֵינֵיכֶם וּרְאוּ מִי־בָרָא אֵלֶּה הַמּוֹצִיא בְמִסְפָּר צְבָאָם לְכֻלָּם בְּשֵׁם יִקְרָא מֵרֹב אוֹנִים וְאַמִּיץ כֹּחַ אִישׁ לֹא נֶעְדָּֽר׃ 26
Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani. Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi? Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo, nayitana iliyonse ndi dzina lake. Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri, palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
לָמָּה תֹאמַר יַֽעֲקֹב וּתְדַבֵּר יִשְׂרָאֵל נִסְתְּרָה דַרְכִּי מֵיְהֹוָה וּמֵאֱלֹהַי מִשְׁפָּטִי יַעֲבֽוֹר׃ 27
Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti, “Yehova sakudziwa mavuto anga, Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
הֲלוֹא יָדַעְתָּ אִם־לֹא שָׁמַעְתָּ אֱלֹהֵי עוֹלָם ׀ יְהֹוָה בּוֹרֵא קְצוֹת הָאָרֶץ לֹא יִיעַף וְלֹא יִיגָע אֵין חֵקֶר לִתְבוּנָתֽוֹ׃ 28
Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
נֹתֵן לַיָּעֵף כֹּחַ וּלְאֵין אוֹנִים עׇצְמָה יַרְבֶּֽה׃ 29
Iye amalimbitsa ofowoka ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
וְיִעֲפוּ נְעָרִים וְיִגָעוּ וּבַחוּרִים כָּשׁוֹל יִכָּשֵֽׁלוּ׃ 30
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka, ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
וְקוֹיֵ יְהֹוָה יַחֲלִיפוּ כֹחַ יַעֲלוּ אֵבֶר כַּנְּשָׁרִים יָרוּצוּ וְלֹא יִיגָעוּ יֵלְכוּ וְלֹא יִיעָֽפוּ׃ 31
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.

< ישעה 40 >