< ישעה 14 >
כִּי יְרַחֵם יְהֹוָה אֶֽת־יַעֲקֹב וּבָחַר עוֹד בְּיִשְׂרָאֵל וְהִנִּיחָם עַל־אַדְמָתָם וְנִלְוָה הַגֵּר עֲלֵיהֶם וְנִסְפְּחוּ עַל־בֵּית יַעֲקֹֽב׃ | 1 |
Yehova adzachitira chifundo Yakobo; adzasankhanso Israeli ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo. Alendo adzabwera kudzakhala nawo ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
וּלְקָחוּם עַמִּים וֶהֱבִיאוּם אֶל־מְקוֹמָם וְהִֽתְנַחֲלוּם בֵּֽית־יִשְׂרָאֵל עַל אַדְמַת יְהֹוָה לַעֲבָדִים וְלִשְׁפָחוֹת וְהָיוּ שֹׁבִים לְשֹׁבֵיהֶם וְרָדוּ בְּנֹגְשֵׂיהֶֽם׃ | 2 |
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli ku dziko lawo. Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova. Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo. Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
וְהָיָה בְּיוֹם הָנִיחַ יְהֹוָה לְךָ מֵֽעׇצְבְּךָ וּמִֽרׇגְזֶךָ וּמִן־הָעֲבֹדָה הַקָּשָׁה אֲשֶׁר עֻבַּד־בָּֽךְ׃ | 3 |
Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani,
וְנָשָׂאתָ הַמָּשָׁל הַזֶּה עַל־מֶלֶךְ בָּבֶל וְאָמָרְתָּ אֵיךְ שָׁבַת נֹגֵשׂ שָׁבְתָה מַדְהֵבָֽה׃ | 4 |
mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti, Wopsinja uja watha! Ukali wake uja watha!
שָׁבַר יְהֹוָה מַטֵּה רְשָׁעִים שֵׁבֶט מֹֽשְׁלִֽים׃ | 5 |
Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa, Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
מַכֶּה עַמִּים בְּעֶבְרָה מַכַּת בִּלְתִּי סָרָה רֹדֶה בָאַף גּוֹיִם מֻרְדָּף בְּלִי חָשָֽׂךְ׃ | 6 |
Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali powamenya kosalekeza, Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali ndikuwazunza kosalekeza.
נָחָה שָׁקְטָה כׇּל־הָאָרֶץ פָּצְחוּ רִנָּֽה׃ | 7 |
Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere; ndipo akuyimba mokondwa.
גַּם־בְּרוֹשִׁים שָׂמְחוּ לְךָ אַרְזֵי לְבָנוֹן מֵאָז שָׁכַבְתָּ לֹא־יַעֲלֶה הַכֹּרֵת עָלֵֽינוּ׃ | 8 |
Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti, “Chigwetsedwere chako pansi, palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
שְׁאוֹל מִתַּחַת רָגְזָה לְךָ לִקְרַאת בּוֹאֶךָ עוֹרֵר לְךָ רְפָאִים כׇּל־עַתּוּדֵי אָרֶץ הֵקִים מִכִּסְאוֹתָם כֹּל מַלְכֵי גוֹיִֽם׃ (Sheol ) | 9 |
Ku manda kwatekeseka kuti akulandire ukamabwera; mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri a dziko lapansi, yadzutsidwa. Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu ayimiritsidwa pa mipando yawo. (Sheol )
כֻּלָּם יַעֲנוּ וְיֹאמְרוּ אֵלֶיךָ גַּם־אַתָּה חֻלֵּיתָ כָמוֹנוּ אֵלֵינוּ נִמְשָֽׁלְתָּ׃ | 10 |
Onse adzayankha; adzanena kwa iwe kuti, “Iwenso watheratu mphamvu ngati ife; Iwe wafanana ndi ife.”
הוּרַד שְׁאוֹל גְּאוֹנֶךָ הֶמְיַת נְבָלֶיךָ תַּחְתֶּיךָ יֻצַּע רִמָּה וּמְכַסֶּיךָ תּוֹלֵעָֽה׃ (Sheol ) | 11 |
Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda, pamodzi ndi nyimbo za azeze ako; mphutsi zayalana pogona pako ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi. (Sheol )
אֵיךְ נָפַלְתָּ מִשָּׁמַיִם הֵילֵל בֶּן־שָׁחַר נִגְדַּעְתָּ לָאָרֶץ חוֹלֵשׁ עַל־גּוֹיִֽם׃ | 12 |
Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha! Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi, Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
וְאַתָּה אָמַרְתָּ בִֽלְבָבְךָ הַשָּׁמַיִם אֶעֱלֶה מִמַּעַל לְכוֹכְבֵי־אֵל אָרִים כִּסְאִי וְאֵשֵׁב בְּהַר־מוֹעֵד בְּיַרְכְּתֵי צָפֽוֹן׃ | 13 |
Mu mtima mwako unkanena kuti, “Ndidzakwera mpaka kumwamba; ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako, pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
אֶֽעֱלֶה עַל־בָּמֳתֵי עָב אֶדַּמֶּה לְעֶלְיֽוֹן׃ | 14 |
Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
אַךְ אֶל־שְׁאוֹל תּוּרָד אֶל־יַרְכְּתֵי־בֽוֹר׃ (Sheol ) | 15 |
Koma watsitsidwa mʼmanda pansi penipeni pa dzenje. (Sheol )
רֹאֶיךָ אֵלֶיךָ יַשְׁגִּיחוּ אֵלֶיךָ יִתְבּוֹנָנוּ הֲזֶה הָאִישׁ מַרְגִּיז הָאָרֶץ מַרְעִישׁ מַמְלָכֽוֹת׃ | 16 |
Anthu akufa adzakupenyetsetsa nadzamalingalira za iwe nʼkumati, “Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi ndi kunjenjemeretsa maufumu,
שָׂם תֵּבֵל כַּמִּדְבָּר וְעָרָיו הָרָס אֲסִירָיו לֹא־פָתַח בָּֽיְתָה׃ | 17 |
munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu, amene anagwetsa mizinda yake ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
כׇּל־מַלְכֵי גוֹיִם כֻּלָּם שָׁכְבוּ בְכָבוֹד אִישׁ בְּבֵיתֽוֹ׃ | 18 |
Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu aliyense mʼmanda akeake.
וְאַתָּה הׇשְׁלַכְתָּ מִֽקִּבְרְךָ כְּנֵצֶר נִתְעָב לְבֻשׁ הֲרֻגִים מְטֹעֲנֵי חָרֶב יוֹרְדֵי אֶל־אַבְנֵי־בוֹר כְּפֶגֶר מוּבָֽס׃ | 19 |
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yowola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa; amene anabayidwa ndi lupanga, anatsikira mʼdzenje lamiyala ngati mtembo woponderezedwa.
לֹֽא־תֵחַד אִתָּם בִּקְבוּרָה כִּי־אַרְצְךָ שִׁחַתָּ עַמְּךָ הָרָגְתָּ לֹא־יִקָּרֵא לְעוֹלָם זֶרַע מְרֵעִֽים׃ | 20 |
Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu, chifukwa unawononga dziko lako ndi kupha anthu ako. Zidzukulu za anthu oyipa sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
הָכִינוּ לְבָנָיו מַטְבֵּחַ בַּעֲוֺן אֲבוֹתָם בַּל־יָקֻמוּ וְיָרְשׁוּ אָרֶץ וּמָלְאוּ פְנֵי־תֵבֵל עָרִֽים׃ | 21 |
Konzani malo woti muphere ana ake aamuna chifukwa cha machimo a makolo awo; kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
וְקַמְתִּי עֲלֵיהֶם נְאֻם יְהֹוָה צְבָאוֹת וְהִכְרַתִּי לְבָבֶל שֵׁם וּשְׁאָר וְנִין וָנֶכֶד נְאֻם־יְהֹוָֽה׃ | 22 |
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni. Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo. Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,” akutero Yehova.
וְשַׂמְתִּיהָ לְמוֹרַשׁ קִפֹּד וְאַגְמֵי־מָיִם וְטֵאטֵאתִיהָ בְּמַטְאֲטֵא הַשְׁמֵד נְאֻם יְהֹוָה צְבָאֽוֹת׃ | 23 |
“Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu ndiponso dambo lamatope; ndidzawusesa ndi tsache lowononga,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
נִשְׁבַּע יְהֹוָה צְבָאוֹת לֵאמֹר אִם־לֹא כַּאֲשֶׁר דִּמִּיתִי כֵּן הָיָתָה וְכַאֲשֶׁר יָעַצְתִּי הִיא תָקֽוּם׃ | 24 |
Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
לִשְׁבֹּר אַשּׁוּר בְּאַרְצִי וְעַל־הָרַי אֲבוּסֶנּוּ וְסָר מֵֽעֲלֵיהֶם עֻלּוֹ וְסֻבֳּלוֹ מֵעַל שִׁכְמוֹ יָסֽוּר׃ | 25 |
Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa; ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga; ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga, ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
זֹאת הָעֵצָה הַיְּעוּצָה עַל־כׇּל־הָאָרֶץ וְזֹאת הַיָּד הַנְּטוּיָה עַל־כׇּל־הַגּוֹיִֽם׃ | 26 |
Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi, ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
כִּֽי־יְהֹוָה צְבָאוֹת יָעָץ וּמִי יָפֵר וְיָדוֹ הַנְּטוּיָה וּמִי יְשִׁיבֶֽנָּה׃ | 27 |
Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse? Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
בִּשְׁנַת־מוֹת הַמֶּלֶךְ אָחָז הָיָה הַמַּשָּׂא הַזֶּֽה׃ | 28 |
Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
אַֽל־תִּשְׂמְחִי פְלֶשֶׁת כֻּלֵּךְ כִּי נִשְׁבַּר שֵׁבֶט מַכֵּךְ כִּֽי־מִשֹּׁרֶשׁ נָחָשׁ יֵצֵא צֶפַע וּפִרְיוֹ שָׂרָף מְעוֹפֵֽף׃ | 29 |
Musakondwere inu Afilisti nonse kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa; chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri, ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
וְרָעוּ בְּכוֹרֵי דַלִּים וְאֶבְיוֹנִים לָבֶטַח יִרְבָּצוּ וְהֵמַתִּי בָרָעָב שׇׁרְשֵׁךְ וּשְׁאֵרִיתֵךְ יַהֲרֹֽג׃ | 30 |
Osaukitsitsa adzapeza chakudya ndipo amphawi adzakhala mwamtendere. Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala, ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
הֵילִילִֽי שַׁעַר זַֽעֲקִי־עִיר נָמוֹג פְּלֶשֶׁת כֻּלֵּךְ כִּי מִצָּפוֹן עָשָׁן בָּא וְאֵין בּוֹדֵד בְּמוֹעָדָֽיו׃ | 31 |
Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda! Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse! Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto, ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
וּמַֽה־יַּעֲנֶה מַלְאֲכֵי־גוֹי כִּי יְהֹוָה יִסַּד צִיּוֹן וּבָהּ יֶחֱסוּ עֲנִיֵּי עַמּֽוֹ׃ | 32 |
Kodi tidzawayankha chiyani amithenga a ku Filisitiya? “Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”