< הושע 14 >
שׁוּבָה יִשְׂרָאֵל עַד יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ כִּי כָשַׁלְתָּ בַּעֲוֺנֶֽךָ׃ | 1 |
Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako. Machimo anu ndi amene akugwetsani!
קְחוּ עִמָּכֶם דְּבָרִים וְשׁוּבוּ אֶל־יְהֹוָה אִמְרוּ אֵלָיו כׇּל־תִּשָּׂא עָוֺן וְקַח־טוֹב וּֽנְשַׁלְּמָה פָרִים שְׂפָתֵֽינוּ׃ | 2 |
Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
אַשּׁוּר ׀ לֹא יוֹשִׁיעֵנוּ עַל־סוּס לֹא נִרְכָּב וְלֹא־נֹאמַר עוֹד אֱלֹהֵינוּ לְמַעֲשֵׂה יָדֵינוּ אֲשֶׁר־בְּךָ יְרֻחַם יָתֽוֹם׃ | 3 |
Asiriya sangatipulumutse; ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo, sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’ kwa zimene manja athu omwe anazipanga, pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
אֶרְפָּא מְשׁוּבָתָם אֹהֲבֵם נְדָבָה כִּי שָׁב אַפִּי מִמֶּֽנּוּ׃ | 4 |
Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo ndipo ndidzawakonda mwaufulu pakuti ndaleka kuwakwiyira.
אֶהְיֶה כַטַּל לְיִשְׂרָאֵל יִפְרַח כַּשּׁוֹשַׁנָּה וְיַךְ שׇׁרָשָׁיו כַּלְּבָנֽוֹן׃ | 5 |
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo. Adzazika mizu yake pansi ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
יֵֽלְכוּ יֹֽנְקוֹתָיו וִיהִי כַזַּיִת הוֹדוֹ וְרֵיחַֽ לוֹ כַּלְּבָנֽוֹן׃ | 6 |
mphukira zake zidzakula. Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi, kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
יָשֻׁבוּ יֹשְׁבֵי בְצִלּוֹ יְחַיּוּ דָגָן וְיִפְרְחוּ כַגָּפֶן זִכְרוֹ כְּיֵין לְבָנֽוֹן׃ | 7 |
Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake. Iye adzakula bwino ngati tirigu. Adzachita maluwa ngati mphesa ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
אֶפְרַיִם מַה־לִּי עוֹד לָעֲצַבִּים אֲנִי עָנִיתִי וַאֲשׁוּרֶנּוּ אֲנִי כִּבְרוֹשׁ רַעֲנָן מִמֶּנִּי פֶּרְיְךָ נִמְצָֽא׃ | 8 |
Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano? Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira. Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira; zipatso zako zimachokera kwa Ine.”
מִי חָכָם וְיָבֵֽן אֵלֶּה נָבוֹן וְיֵדָעֵם כִּֽי־יְשָׁרִים דַּרְכֵי יְהֹוָה וְצַדִּקִים יֵלְכוּ בָם וּפֹשְׁעִים יִכָּשְׁלוּ בָֽם׃ | 9 |
Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi. Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi. Njira za Yehova ndi zolungama; anthu olungama amayenda mʼmenemo, koma anthu owukira amapunthwamo.