< יחזקאל 30 >

וַיְהִי דְבַר־יְהֹוָה אֵלַי לֵאמֹֽר׃ 1
Yehova anandiyankhula kuti:
בֶּן־אָדָם הִנָּבֵא וְאָמַרְתָּ כֹּה אָמַר אֲדֹנָי יֱהֹוִה הֵילִילוּ הָהּ לַיּֽוֹם׃ 2
“Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. “‘Ufuwule mawu awa akuti, ‘Kalanga, tsiku lafika!’
כִּֽי־קָרוֹב יוֹם וְקָרוֹב יוֹם לַֽיהֹוָה יוֹם עָנָן עֵת גּוֹיִם יִהְיֶֽה׃ 3
Pakuti tsiku layandikira, tsiku la Yehova lili pafupi, tsiku la mitambo yakuda, tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
וּבָאָה חֶרֶב בְּמִצְרַיִם וְהָיְתָה חַלְחָלָה בְּכוּשׁ בִּנְפֹל חָלָל בְּמִצְרָיִם וְלָקְחוּ הֲמוֹנָהּ וְנֶהֶרְסוּ יְסֹדוֹתֶֽיהָ׃ 4
Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto ndipo mavuto adzafika pa Kusi. Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto, chuma chake chidzatengedwa ndipo maziko ake adzagumuka.
כּוּשׁ וּפוּט וְלוּד וְכׇל־הָעֶרֶב וְכוּב וּבְנֵי אֶרֶץ הַבְּרִית אִתָּם בַּחֶרֶב יִפֹּֽלוּ׃ 5
Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
כֹּה אָמַר יְהֹוָה וְנָֽפְלוּ סֹמְכֵי מִצְרַיִם וְיָרַד גְּאוֹן עֻזָּהּ מִמִּגְדֹּל סְוֵנֵה בַּחֶרֶב יִפְּלוּ־בָהּ נְאֻם אֲדֹנָי יֱהֹוִֽה׃ 6
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu. Adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’” ndikutero Ine Ambuye Yehova.
וְנָשַׁמּוּ בְּתוֹךְ אֲרָצוֹת נְשַׁמּוֹת וְעָרָיו בְּתוֹךְ־עָרִים נַחֲרָבוֹת תִּֽהְיֶֽינָה׃ 7
“‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja kupambana mabwinja ena onse opasuka, ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yonse.
וְיָדְעוּ כִּֽי־אֲנִי יְהֹוָה בְּתִתִּי־אֵשׁ בְּמִצְרַיִם וְנִשְׁבְּרוּ כׇּל־עֹֽזְרֶֽיהָ׃ 8
Nditatha kutentha Igupto ndi kupha onse omuthandiza, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
בַּיּוֹם הַהוּא יֵצְאוּ מַלְאָכִים מִלְּפָנַי בַּצִּים לְהַחֲרִיד אֶת־כּוּשׁ בֶּטַח וְהָיְתָה חַלְחָלָה בָהֶם בְּיוֹם מִצְרַיִם כִּי הִנֵּה בָּאָֽה׃ 9
“‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
כֹּה אָמַר אֲדֹנָי יֱהֹוִה וְהִשְׁבַּתִּי אֶת־הֲמוֹן מִצְרַיִם בְּיַד נְבוּכַדְרֶאצַּר מֶלֶךְ־בָּבֶֽל׃ 10
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
הוּא וְעַמּוֹ אִתּוֹ עָרִיצֵי גוֹיִם מוּבָאִים לְשַׁחֵת הָאָרֶץ וְהֵרִיקוּ חַרְבוֹתָם עַל־מִצְרַיִם וּמָלְאוּ אֶת־הָאָרֶץ חָלָֽל׃ 11
Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja adzabwera kudzawononga dzikolo. Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
וְנָתַתִּי יְאֹרִים חׇֽרָבָה וּמָכַרְתִּי אֶת־הָאָרֶץ בְּיַד־רָעִים וַהֲשִׁמֹּתִי אֶרֶץ וּמְלֹאָהּ בְּיַד־זָרִים אֲנִי יְהֹוָה דִּבַּֽרְתִּי׃ 12
Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa. Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo. Ine Yehova ndayankhula.
כֹּֽה־אָמַר אֲדֹנָי יֱהֹוִה וְהַאֲבַדְתִּי גִלּוּלִים וְהִשְׁבַּתִּי אֱלִילִים מִנֹּף וְנָשִׂיא מֵאֶֽרֶץ־מִצְרַיִם לֹא יִֽהְיֶה־עוֹד וְנָתַתִּי יִרְאָה בְּאֶרֶץ מִצְרָֽיִם׃ 13
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndidzawononga mafano ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi. Simudzakhalanso mfumu mu Igupto, ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
וַֽהֲשִׁמֹּתִי אֶת־פַּתְרוֹס וְנָתַתִּי אֵשׁ בְּצֹעַן וְעָשִׂיתִי שְׁפָטִים בְּנֹֽא׃ 14
Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi, ndi kutentha mzinda wa Zowani. Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
וְשָׁפַכְתִּי חֲמָתִי עַל־סִין מָעוֹז מִצְרָיִם וְהִכְרַתִּי אֶת־הֲמוֹן נֹֽא׃ 15
Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Igupto, ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
וְנָתַתִּי אֵשׁ בְּמִצְרַיִם חוּל (תחיל) [תָּחוּל] סִין וְנֹא תִּֽהְיֶה לְהִבָּקֵעַ וְנֹף צָרֵי יוֹמָֽם׃ 16
Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto; Peluziumu adzazunzika ndi ululu. Malinga a Thebesi adzagumuka, ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
בַּחוּרֵי אָוֶן וּפִי־בֶסֶת בַּחֶרֶב יִפֹּלוּ וְהֵנָּה בַּשְּׁבִי תֵלַֽכְנָה׃ 17
Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
וּבִֽתְחַפְנְחֵס חָשַׂךְ הַיּוֹם בְּשִׁבְרִי־שָׁם אֶת־מֹטוֹת מִצְרַיִם וְנִשְׁבַּת־בָּהּ גְּאוֹן עֻזָּהּ הִיא עָנָן יְכַסֶּנָּה וּבְנוֹתֶיהָ בַּשְּׁבִי תֵלַֽכְנָה׃ 18
Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima pamene ndidzathyola goli la Igupto; motero kunyada kwake kudzatha. Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda, ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
וְעָשִׂיתִי שְׁפָטִים בְּמִצְרָיִם וְיָדְעוּ כִּֽי־אֲנִי יְהֹוָֽה׃ 19
Kotero ndidzalanga dziko la Igupto, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’”
וַיְהִי בְּאַחַת עֶשְׂרֵה שָׁנָה בָּרִאשׁוֹן בְּשִׁבְעָה לַחֹדֶשׁ הָיָה דְבַר־יְהֹוָה אֵלַי לֵאמֹֽר׃ 20
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
בֶּן־אָדָם אֶת־זְרוֹעַ פַּרְעֹה מֶלֶךְ־מִצְרַיִם שָׁבָרְתִּי וְהִנֵּה לֹֽא־חֻבְּשָׁה לָתֵת רְפֻאוֹת לָשׂוּם חִתּוּל לְחׇבְשָׁהּ לְחׇזְקָהּ לִתְפֹּשׂ בֶּחָֽרֶב׃ 21
“Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
לָכֵן כֹּה־אָמַר ׀ אֲדֹנָי יֱהֹוִה הִנְנִי אֶל־פַּרְעֹה מֶלֶךְ־מִצְרַיִם וְשָֽׁבַרְתִּי אֶת־זְרֹעֹתָיו אֶת־הַחֲזָקָה וְאֶת־הַנִּשְׁבָּרֶת וְהִפַּלְתִּי אֶת־הַחֶרֶב מִיָּדֽוֹ׃ 22
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake.
וַהֲפִצוֹתִי אֶת־מִצְרַיִם בַּגּוֹיִם וְזֵרִיתִם בָּאֲרָצֽוֹת׃ 23
Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri.
וְחִזַּקְתִּי אֶת־זְרֹעוֹת מֶלֶךְ בָּבֶל וְנָתַתִּי אֶת־חַרְבִּי בְּיָדוֹ וְשָֽׁבַרְתִּי אֶת־זְרֹעוֹת פַּרְעֹה וְנָאַק נַאֲקוֹת חָלָל לְפָנָֽיו׃ 24
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo.
וְהַחֲזַקְתִּי אֶת־זְרֹעוֹת מֶלֶךְ בָּבֶל וּזְרֹעוֹת פַּרְעֹה תִּפֹּלְנָה וְֽיָדְעוּ כִּי־אֲנִי יְהֹוָה בְּתִתִּי חַרְבִּי בְּיַד מֶֽלֶךְ־בָּבֶל וְנָטָה אוֹתָהּ אֶל־אֶרֶץ מִצְרָֽיִם׃ 25
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto.
וַהֲפִצוֹתִי אֶת־מִצְרַיִם בַּגּוֹיִם וְזֵרִיתִי אוֹתָם בָּאֲרָצוֹת וְיָדְעוּ כִּֽי־אֲנִי יְהֹוָֽה׃ 26
Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

< יחזקאל 30 >