< קֹהֶלֶת 8 >

מִי כְּהֶחָכָם וּמִי יוֹדֵעַ פֵּשֶׁר דָּבָר חׇכְמַת אָדָם תָּאִיר פָּנָיו וְעֹז פָּנָיו יְשֻׁנֶּֽא׃ 1
Ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu? Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.
אֲנִי פִּי־מֶלֶךְ שְׁמֹר וְעַל דִּבְרַת שְׁבוּעַת אֱלֹהִֽים׃ 2
Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu.
אַל־תִּבָּהֵל מִפָּנָיו תֵּלֵךְ אַֽל־תַּעֲמֹד בְּדָבָר רָע כִּי כׇּל־אֲשֶׁר יַחְפֹּץ יַעֲשֶֽׂה׃ 3
Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho.
בַּאֲשֶׁר דְּבַר־מֶלֶךְ שִׁלְטוֹן וּמִי יֹֽאמַר־לוֹ מַֽה־תַּעֲשֶֽׂה׃ 4
Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
שׁוֹמֵר מִצְוָה לֹא יֵדַע דָּבָר רָע וְעֵת וּמִשְׁפָּט יֵדַע לֵב חָכָֽם׃ 5
Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse, ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake.
כִּי לְכׇל־חֵפֶץ יֵשׁ עֵת וּמִשְׁפָּט כִּֽי־רָעַת הָאָדָם רַבָּה עָלָֽיו׃ 6
Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri.
כִּֽי־אֵינֶנּוּ יֹדֵעַ מַה־שֶּׁיִּֽהְיֶה כִּי כַּאֲשֶׁר יִֽהְיֶה מִי יַגִּיד לֽוֹ׃ 7
Popeza palibe munthu amene amadziwa zamʼtsogolo, ndani angamuwuze zomwe zidzachitika mʼtsogolo?
אֵין אָדָם שַׁלִּיט בָּרוּחַ לִכְלוֹא אֶת־הָרוּחַ וְאֵין שִׁלְטוֹן בְּיוֹם הַמָּוֶת וְאֵין מִשְׁלַחַת בַּמִּלְחָמָה וְלֹֽא־יְמַלֵּט רֶשַׁע אֶת־בְּעָלָֽיו׃ 8
Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yolamulira mpweya wa moyo kuti athe kuwusunga, choncho palibe amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa yake. Nkhondo sithawika; tsono anthu ochita zoyipa, kuyipa kwawoko sikudzawapulumutsa.
אֶת־כׇּל־זֶה רָאִיתִי וְנָתוֹן אֶת־לִבִּי לְכׇֽל־מַעֲשֶׂה אֲשֶׁר נַעֲשָׂה תַּחַת הַשָּׁמֶשׁ עֵת אֲשֶׁר שָׁלַט הָאָדָם בְּאָדָם לְרַע לֽוֹ׃ 9
Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza.
וּבְכֵן רָאִיתִי רְשָׁעִים קְבֻרִים וָבָאוּ וּמִמְּקוֹם קָדוֹשׁ יְהַלֵּכוּ וְיִֽשְׁתַּכְּחוּ בָעִיר אֲשֶׁר כֵּן־עָשׂוּ גַּם־זֶה הָֽבֶל׃ 10
Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.
אֲשֶׁר אֵין־נַעֲשָׂה פִתְגָם מַעֲשֵׂה הָרָעָה מְהֵרָה עַל־כֵּן מָלֵא לֵב בְּֽנֵי־הָאָדָם בָּהֶם לַעֲשׂוֹת רָֽע׃ 11
Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa.
אֲשֶׁר חֹטֶא עֹשֶׂה רָע מְאַת וּמַאֲרִיךְ לוֹ כִּי גַּם־יוֹדֵעַ אָנִי אֲשֶׁר יִהְיֶה־טּוֹב לְיִרְאֵי הָאֱלֹהִים אֲשֶׁר יִֽירְאוּ מִלְּפָנָֽיו׃ 12
Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu.
וְטוֹב לֹֽא־יִהְיֶה לָֽרָשָׁע וְלֹֽא־יַאֲרִיךְ יָמִים כַּצֵּל אֲשֶׁר אֵינֶנּוּ יָרֵא מִלִּפְנֵי אֱלֹהִֽים׃ 13
Koma popeza oyipa saopa Mulungu zinthu sizidzawayendera bwino, ndipo moyo wawo sudzakhalitsa monga mthunzi.
יֶשׁ־הֶבֶל אֲשֶׁר נַעֲשָׂה עַל־הָאָרֶץ אֲשֶׁר ׀ יֵשׁ צַדִּיקִים אֲשֶׁר מַגִּיעַ אֲלֵהֶם כְּמַעֲשֵׂה הָרְשָׁעִים וְיֵשׁ רְשָׁעִים שֶׁמַּגִּיעַ אֲלֵהֶם כְּמַעֲשֵׂה הַצַּדִּיקִים אָמַרְתִּי שֶׁגַּם־זֶה הָֽבֶל׃ 14
Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino.
וְשִׁבַּחְתִּֽי אֲנִי אֶת־הַשִּׂמְחָה אֲשֶׁר אֵֽין־טוֹב לָֽאָדָם תַּחַת הַשֶּׁמֶשׁ כִּי אִם־לֶאֱכֹל וְלִשְׁתּוֹת וְלִשְׂמוֹחַ וְהוּא יִלְוֶנּוּ בַעֲמָלוֹ יְמֵי חַיָּיו אֲשֶׁר־נָֽתַן־לוֹ הָאֱלֹהִים תַּחַת הַשָּֽׁמֶשׁ׃ 15
Nʼchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake amene Mulungu wamupatsa pansi pano.
כַּאֲשֶׁר נָתַתִּי אֶת־לִבִּי לָדַעַת חׇכְמָה וְלִרְאוֹת אֶת־הָעִנְיָן אֲשֶׁר נַעֲשָׂה עַל־הָאָרֶץ כִּי גַם בַּיּוֹם וּבַלַּיְלָה שֵׁנָה בְּעֵינָיו אֵינֶנּוּ רֹאֶֽה׃ 16
Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku,
וְרָאִיתִי אֶת־כׇּל־מַעֲשֵׂה הָאֱלֹהִים כִּי לֹא יוּכַל הָאָדָם לִמְצוֹא אֶת־הַֽמַּעֲשֶׂה אֲשֶׁר נַעֲשָׂה תַֽחַת־הַשֶּׁמֶשׁ בְּשֶׁל אֲשֶׁר יַעֲמֹל הָאָדָם לְבַקֵּשׁ וְלֹא יִמְצָא וְגַם אִם־יֹאמַר הֶֽחָכָם לָדַעַת לֹא יוּכַל לִמְצֹֽא׃ 17
pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.

< קֹהֶלֶת 8 >