< דניאל 12 >
וּבָעֵת הַהִיא יַעֲמֹד מִֽיכָאֵל הַשַּׂר הַגָּדוֹל הָעֹמֵד עַל־בְּנֵי עַמֶּךָ וְהָיְתָה עֵת צָרָה אֲשֶׁר לֹֽא־נִהְיְתָה מִֽהְיוֹת גּוֹי עַד הָעֵת הַהִיא וּבָעֵת הַהִיא יִמָּלֵט עַמְּךָ כׇּל־הַנִּמְצָא כָּתוּב בַּסֵּֽפֶר׃ | 1 |
“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa.
וְרַבִּים מִיְּשֵׁנֵי אַדְמַת־עָפָר יָקִיצוּ אֵלֶּה לְחַיֵּי עוֹלָם וְאֵלֶּה לַחֲרָפוֹת לְדִרְאוֹן עוֹלָֽם׃ | 2 |
Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha.
וְהַמַּשְׂכִּלִים יַזְהִרוּ כְּזֹהַר הָרָקִיעַ וּמַצְדִּיקֵי הָֽרַבִּים כַּכּוֹכָבִים לְעוֹלָם וָעֶֽד׃ | 3 |
Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.
וְאַתָּה דָֽנִיֵּאל סְתֹם הַדְּבָרִים וַחֲתֹם הַסֵּפֶר עַד־עֵת קֵץ יְשֹׁטְטוּ רַבִּים וְתִרְבֶּה הַדָּֽעַת׃ | 4 |
Koma iweyo, Danieli, sungitsa mawuwa, umate bukuli kufikira nthawi ya chimaliziro. Anthu ambiri adzapita uku ndi uko ndipo nzeru zidzanka zikukulirakulira.”
וְרָאִיתִי אֲנִי דָנִיֵּאל וְהִנֵּה שְׁנַיִם אֲחֵרִים עֹמְדִים אֶחָד הֵנָּה לִשְׂפַת הַיְאֹר וְאֶחָד הֵנָּה לִשְׂפַת הַיְאֹֽר׃ | 5 |
Kenaka ine Danieli poyangʼana ndinaona anthu ena awiri atayima, wina tsidya lino la mtsinje, wina tsidya linalo.
וַיֹּאמֶר לָאִישׁ לְבוּשׁ הַבַּדִּים אֲשֶׁר מִמַּעַל לְמֵימֵי הַיְאֹר עַד־מָתַי קֵץ הַפְּלָאֽוֹת׃ | 6 |
Mmodzi mwa awiriwo anafunsa munthu wovala chovala chosalala amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja kuti, “Kodi padzapita nthawi yayitali bwanji kuti zodabwitsazi zidzakwaniritsidwe?”
וָאֶשְׁמַע אֶת־הָאִישׁ ׀ לְבוּשׁ הַבַּדִּים אֲשֶׁר מִמַּעַל לְמֵימֵי הַיְאֹר וַיָּרֶם יְמִינוֹ וּשְׂמֹאלוֹ אֶל־הַשָּׁמַיִם וַיִּשָּׁבַע בְּחֵי הָעוֹלָם כִּי לְמוֹעֵד מֽוֹעֲדִים וָחֵצִי וּכְכַלּוֹת נַפֵּץ יַד־עַם־קֹדֶשׁ תִּכְלֶינָה כׇל־אֵֽלֶּה׃ | 7 |
Munthu wovala chovala chosalala, amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja, anakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, ndipo ndinamumva akulumbira mʼdzina la Wamoyo ku nthawi zonse uja kuti, “Zidzachitika patapita zaka zitatu ndi theka. Zinthu zonsezi zidzachitika akadzatha masautso amene agwera anthu olungama.”
וַאֲנִי שָׁמַעְתִּי וְלֹא אָבִין וָאֹמְרָה אֲדֹנִי מָה אַחֲרִית אֵֽלֶּה׃ | 8 |
Ndinamva, koma sindinamvetsetse. Choncho ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, nanga matsiriziro a zonsezi adzakhala chiyani?”
וַיֹּאמֶר לֵךְ דָּנִיֵּאל כִּֽי־סְתֻמִים וַחֲתֻמִים הַדְּבָרִים עַד־עֵת קֵֽץ׃ | 9 |
Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro.
יִתְבָּֽרְרוּ וְיִֽתְלַבְּנוּ וְיִצָּֽרְפוּ רַבִּים וְהִרְשִׁיעוּ רְשָׁעִים וְלֹא יָבִינוּ כׇּל־רְשָׁעִים וְהַמַּשְׂכִּלִים יָבִֽינוּ׃ | 10 |
Anthu ambiri adzayeretsedwa nakhala olungama wopanda chodetsa, koma oyipa adzakhala chiyipire. Palibe mmodzi wa anthu oyipa amene adzamvetsetsa koma okhawo amene ali anzeru adzamvetsetsa.
וּמֵעֵת הוּסַר הַתָּמִיד וְלָתֵת שִׁקּוּץ שֹׁמֵם יָמִים אֶלֶף מָאתַיִם וְתִשְׁעִֽים׃ | 11 |
“Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290.
אַשְׁרֵי הַֽמְחַכֶּה וְיַגִּיעַ לְיָמִים אֶלֶף שְׁלֹשׁ מֵאוֹת שְׁלֹשִׁים וַחֲמִשָּֽׁה׃ | 12 |
Wodala munthu amene adikirabe nadzafika pa mapeto a masiku 1,335.
וְאַתָּה לֵךְ לַקֵּץ וְתָנוּחַ וְתַעֲמֹד לְגֹרָלְךָ לְקֵץ הַיָּמִֽין׃ | 13 |
“Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.”