< זכריה 4 >
וישב המלאך הדבר בי ויעירני כאיש אשר יעור משנתו | 1 |
Kenaka mngelo amene amayankhula nane anabwerera nandidzutsa, ngati mmene amadzutsira munthu amene ali mʼtulo.
ויאמר אלי מה אתה ראה ויאמר (ואמר) ראיתי והנה מנורת זהב כלה וגלה על ראשה ושבעה נרתיה עליה--שבעה ושבעה מוצקות לנרות אשר על ראשה | 2 |
Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira.
ושנים זיתים עליה אחד מימין הגלה ואחד על שמאלה | 3 |
Ndiponso pambali pake pali mitengo ya olivi iwiri, umodzi uli kumanja kwa mbaleyo ndipo winawo kumanzere.”
ואען ואמר אל המלאך הדבר בי לאמר מה אלה אדני | 4 |
Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi nʼchiyani mbuye wanga?”
ויען המלאך הדבר בי ויאמר אלי הלוא ידעת מה המה אלה ואמר לא אדני | 5 |
Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ndinayankha kuti, “Ayi mbuye wanga.”
ויען ויאמר אלי לאמר זה דבר יהוה אל זרבבל לאמר לא בחיל ולא בכח--כי אם ברוחי אמר יהוה צבאות | 6 |
Choncho iye anandiwuza kuti, “Mawu a Yehova kwa Zerubabeli ndi awa: ‘Osati mwa nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi Mzimu wanga,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
מי אתה הר הגדול לפני זרבבל למישר והוציא את האבן הראשה--תשאות חן חן לה | 7 |
“Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’”
Ndipo Yehova anayankhulanso nane kuti,
ידי זרבבל יסדו הבית הזה--וידיו תבצענה וידעת כי יהוה צבאות שלחני אליכם | 9 |
“Manja a Zerubabeli ndiwo ayika maziko a Nyumbayi; adzatsiriza ndi manja ake omwewo. Pamenepo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye anakutuma.
כי מי בז ליום קטנות ושמחו וראו את האבן הבדיל ביד זרבבל שבעה אלה עיני יהוה המה משוטטים בכל הארץ | 10 |
“Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli. (“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)
ואען ואמר אליו מה שני הזיתים האלה על ימין המנורה ועל שמאולה | 11 |
Kenaka ndinafunsa mngelo uja kuti, “Kodi mitengo ya olivi iwiri ili kumanja ndi kumanzere kwa choyikapo nyalechi ikutanthauza chiyani?”
ואען שנית ואמר אליו מה שתי שבלי הזיתים אשר ביד שני צנתרות הזהב המריקים מעליהם הזהב | 12 |
Ndinamufunsanso kuti, “Kodi nthambi ziwiri za mtengo wa olivi zomwe zili pambali pa mipopi yodzera mafuta iwiri yagolide zikutanthauza chiyani?”
ויאמר אלי לאמר הלוא ידעת מה אלה ואמר לא אדני | 13 |
Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ine ndinati, “Ayi mbuye wanga.”
ויאמר אלה שני בני היצהר העמדים על אדון כל הארץ | 14 |
Choncho iye anati, “Amenewa ndi anthu awiri amene adzozedwa kuti atumikire Ambuye pa dziko lonse lapansi.”