< תהילים 92 >

מזמור שיר ליום השבת ב טוב להדות ליהוה ולזמר לשמך עליון 1
Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata. Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
להגיד בבקר חסדך ואמונתך בלילות 2
Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
עלי-עשור ועלי-נבל עלי הגיון בכנור 3
kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze.
כי שמחתני יהוה בפעלך במעשי ידיך ארנן 4
Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
מה-גדלו מעשיך יהוה מאד עמקו מחשבתיך 5
Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!
איש-בער לא ידע וכסיל לא-יבין את-זאת 6
Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira,
בפרח רשעים כמו עשב ויציצו כל-פעלי און להשמדם עדי-עד 7
kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.
ואתה מרום-- לעלם יהוה 8
Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.
כי הנה איביך יהוה-- כי-הנה איביך יאבדו יתפרדו כל-פעלי און 9
Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
ותרם כראים קרני בלתי בשמן רענן 10
Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
ותבט עיני בשורי בקמים עלי מרעים-- תשמענה אזני 11
Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.
צדיק כתמר יפרח כארז בלבנון ישגה 12
Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
שתולים בבית יהוה בחצרות אלהינו יפריחו 13
odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
עוד ינובון בשיבה דשנים ורעננים יהיו 14
Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira,
להגיד כי-ישר יהוה צורי ולא-עלתה (עולתה) בו 15
kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”

< תהילים 92 >