< תהילים 91 >

ישב בסתר עליון בצל שדי יתלונן 1
Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
אמר--ליהוה מחסי ומצודתי אלהי אבטח-בו 2
Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.”
כי הוא יצילך מפח יקוש מדבר הוות 3
Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje ndi ku mliri woopsa;
באברתו יסך לך--ותחת-כנפיו תחסה צנה וסחרה אמתו 4
Adzakuphimba ndi nthenga zake, ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo; kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
לא-תירא מפחד לילה מחץ יעוף יומם 5
Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku, kapena muvi wowuluka masana,
מדבר באפל יהלך מקטב ישוד צהרים 6
kapena mliri umene umayenda mu mdima, kapena zowononga za pa nthawi ya masana.
יפל מצדך אלף--ורבבה מימינך אליך לא יגש 7
Anthu 1,000 atha kufa pambali pako, anthu 10,000 kudzanja lako lamanja, koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
רק בעיניך תביט ושלמת רשעים תראה 8
Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.
כי-אתה יהוה מחסי עליון שמת מעונך 9
Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo; wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
לא-תאנה אליך רעה ונגע לא-יקרב באהלך 10
Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
כי מלאכיו יצוה-לך לשמרך בכל-דרכיך 11
Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;
על-כפים ישאונך פן-תגף באבן רגלך 12
ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
על-שחל ופתן תדרך תרמס כפיר ותנין 13
Udzapondaponda mkango ndi njoka, udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.
כי בי חשק ואפלטהו אשגבהו כי-ידע שמי 14
“Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
יקראני ואענהו--עמו-אנכי בצרה אחלצהו ואכבדהו 15
Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
ארך ימים אשביעהו ואראהו בישועתי 16
Ndidzamupatsa moyo wautali ndi kumupulumutsa.”

< תהילים 91 >