< תהילים 87 >

לבני-קרח מזמור שיר יסודתו בהררי-קדש 1
Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
אהב יהוה שערי ציון-- מכל משכנות יעקב 2
Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
נכבדות מדבר בך-- עיר האלהים סלה 3
Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: (Sela)
אזכיר רהב ובבל-- לידעי הנה פלשת וצר עם-כוש זה ילד-שם 4
“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’”
ולציון יאמר-- איש ואיש ילד-בה והוא יכוננה עליון 5
Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
יהוה--יספר בכתוב עמים זה ילד-שם סלה 6
Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” (Sela)
ושרים כחללים-- כל-מעיני בך 7
Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

< תהילים 87 >