< תהילים 75 >
למנצח אל-תשחת מזמור לאסף שיר ב הודינו לך אלהים--הודינו וקרוב שמך ספרו נפלאותיך | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
כי אקח מועד אני מישרים אשפט | 2 |
Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
נמגים ארץ וכל-ישביה אנכי תכנתי עמודיה סלה | 3 |
Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. (Sela)
אמרתי להוללים אל-תהלו ולרשעים אל-תרימו קרן | 4 |
Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
אל-תרימו למרום קרנכם תדברו בצואר עתק | 5 |
Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’”
כי לא ממוצא וממערב ולא ממדבר הרים | 6 |
Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.
כי-אלהים שפט זה ישפיל וזה ירים | 7 |
Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
כי כוס ביד-יהוה ויין חמר מלא מסך-- ויגר מזה אך-שמריה ימצו ישתו כל רשעי-ארץ | 8 |
Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.
ואני אגיד לעלם אזמרה לאלהי יעקב | 9 |
Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
וכל-קרני רשעים אגדע תרוממנה קרנות צדיק | 10 |
Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.