< תהילים 64 >
למנצח מזמור לדוד ב שמע-אלהים קולי בשיחי מפחד אויב תצר חיי | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga; tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.
תסתירני מסוד מרעים מרגשת פעלי און | 2 |
Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa, ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.
אשר שננו כחרב לשונם דרכו חצם דבר מר | 3 |
Iwo amanola malilime awo ngati malupanga, amaponya mawu awo olasa ngati mivi.
לירת במסתרים תם פתאם ירהו ולא ייראו | 4 |
Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa; amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.
יחזקו-למו דבר רע-- יספרו לטמון מוקשים אמרו מי יראה-למו | 5 |
Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
יחפשו עולת-- תמנו חפש מחפש וקרב איש ולב עמק | 6 |
Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati, “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!” Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.
וירם אלהים חץ פתאום--היו מכותם | 7 |
Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi; mwadzidzidzi adzakanthidwa.
ויכשילוהו עלימו לשונם יתנדדו כל-ראה בם | 8 |
Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa ndi kuwasandutsa bwinja; onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.
וייראו כל-אדם ויגידו פעל אלהים ומעשהו השכילו | 9 |
Anthu onse adzachita mantha; adzalengeza ntchito za Mulungu ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.
ישמח צדיק ביהוה וחסה בו ויתהללו כל-ישרי-לב | 10 |
Lolani wolungama akondwere mwa Yehova ndi kubisala mwa Iye, owongoka mtima onse atamande Iye!