< תהילים 47 >

למנצח לבני-קרח מזמור ב כל-העמים תקעו-כף הריעו לאלהים בקול רנה 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
כי-יהוה עליון נורא מלך גדול על-כל-הארץ 2
Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
ידבר עמים תחתינו ולאמים תחת רגלינו 3
Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.
יבחר-לנו את-נחלתנו את גאון יעקב אשר-אהב סלה 4
Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. (Sela)
עלה אלהים בתרועה יהוה בקול שופר 5
Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
זמרו אלהים זמרו זמרו למלכנו זמרו 6
Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
כי מלך כל-הארץ אלהים-- זמרו משכיל 7
Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando.
מלך אלהים על-גוים אלהים ישב על-כסא קדשו 8
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
נדיבי עמים נאספו-- עם אלהי אברהם כי לאלהים מגני-ארץ-- מאד נעלה 9
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.

< תהילים 47 >