< תהילים 42 >
למנצח משכיל לבני-קרח ב כאיל תערג על-אפיקי-מים-- כן נפשי תערג אליך אלהים | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
צמאה נפשי לאלהים-- לאל חי מתי אבוא ואראה פני אלהים | 2 |
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo. Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
היתה-לי דמעתי לחם יומם ולילה באמר אלי כל-היום איה אלהיך | 3 |
Misozi yanga yakhala chakudya changa usana ndi usiku, pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
אלה אזכרה ואשפכה עלי נפשי-- כי אעבר בסך אדדם עד-בית אלהים בקול-רנה ותודה המון חוגג | 4 |
Zinthu izi ndimazikumbukira pamene ndikukhuthula moyo wanga: momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu, kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko pakati pa anthu a pa chikondwerero.
מה-תשתוחחי נפשי-- ותהמי עלי הוחלי לאלהים כי-עוד אודנו-- ישועות פניו | 5 |
Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi
אלהי-- עלי נפשי תשתוחח על-כן--אזכרך מארץ ירדן וחרמונים מהר מצער | 6 |
Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga kotero ndidzakumbukira Inu kuchokera ku dziko la Yorodani, ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
תהום-אל-תהום קורא לקול צנוריך כל-משבריך וגליך עלי עברו | 7 |
Madzi akuya akuyitana madzi akuya mu mkokomo wa mathithi anu; mafunde anu onse obwera mwamphamvu andimiza.
יומם יצוה יהוה חסדו ובלילה שירה עמי-- תפלה לאל חיי | 8 |
Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake, nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane; pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
אומרה לאל סלעי-- למה שכחתני למה-קדר אלך-- בלחץ אויב | 9 |
Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”
ברצח בעצמותי-- חרפוני צוררי באמרם אלי כל-היום איה אלהיך | 10 |
Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo pamene adani anga akundinyoza, tsiku lonse akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
מה-תשתוחחי נפשי-- ומה-תהמי עלי הוחילי לאלהים כי-עוד אודנו-- ישועת פני ואלהי | 11 |
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.