< תהילים 38 >
מזמור לדוד להזכיר ב יהוה--אל-בקצפך תוכיחני ובחמתך תיסרני | 1 |
Salimo la Davide. Kupempha. Yehova musandidzudzule mutapsa mtima kapena kundilanga muli ndi ukali.
כי-חציך נחתו בי ותנחת עלי ידך | 2 |
Pakuti mivi yanu yandilasa, ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
אין-מתם בבשרי מפני זעמך אין-שלום בעצמי מפני חטאתי | 3 |
Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa; mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
כי עונתי עברו ראשי כמשא כבד יכבדו ממני | 4 |
Kulakwa kwanga kwandipsinja ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.
הבאישו נמקו חבורתי מפני אולתי | 5 |
Mabala anga akuwola ndipo akununkha chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
נעויתי שחתי עד-מאד כל-היום קדר הלכתי | 6 |
Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri; tsiku lonse ndimangolira.
כי-כסלי מלאו נקלה ואין מתם בבשרי | 7 |
Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika, mulibe thanzi mʼthupi langa.
נפוגותי ונדכיתי עד-מאד שאגתי מנהמת לבי | 8 |
Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu; ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.
אדני נגדך כל-תאותי ואנחתי ממך לא-נסתרה | 9 |
Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye, kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
לבי סחרחר עזבני כחי ואור-עיני גם-הם אין אתי | 10 |
Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha; ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
אהבי ורעי--מנגד נגעי יעמדו וקרובי מרחק עמדו | 11 |
Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga; anansi anga akhala kutali nane.
וינקשו מבקשי נפשי ודרשי רעתי דברו הוות ומרמות כל-היום יהגו | 12 |
Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo, oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga; tsiku lonse amakonza zachinyengo.
ואני כחרש לא אשמע וכאלם לא יפתח-פיו | 13 |
Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve, monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
ואהי--כאיש אשר לא-שמע ואין בפיו תוכחות | 14 |
Ndakhala ngati munthu amene samva, amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
כי-לך יהוה הוחלתי אתה תענה אדני אלהי | 15 |
Ndikudikira Inu Yehova; mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
כי-אמרתי פן-ישמחו-לי במוט רגלי עלי הגדילו | 16 |
Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”
כי-אני לצלע נכון ומכאובי נגדי תמיד | 17 |
Pakuti ndili pafupi kugwa, ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
כי-עוני אגיד אדאג מחטאתי | 18 |
Ndikuvomereza mphulupulu zanga; ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
ואיבי חיים עצמו ורבו שנאי שקר | 19 |
Ambiri ndi adani anga amphamvu; amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
ומשלמי רעה תחת טובה-- ישטנוני תחת רדופי- (רדפי-) טוב | 20 |
Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino amandinyoza pamene nditsatira zabwino.
אל-תעזבני יהוה אלהי אל-תרחק ממני | 21 |
Inu Yehova, musanditaye; musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
חושה לעזרתי אדני תשועתי | 22 |
Bwerani msanga kudzandithandiza, Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.