< תהילים 37 >

לדוד אל-תתחר במרעים אל-תקנא בעשי עולה 1
Salimo la Davide. Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
כי כחציר מהרה ימלו וכירק דשא יבולון 2
pakuti monga udzu iwo adzafota msanga, ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.
בטח ביהוה ועשה-טוב שכן-ארץ ורעה אמונה 3
Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino; khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
והתענג על-יהוה ויתן-לך משאלת לבך 4
Udzikondweretse wekha mwa Yehova ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.
גול על-יהוה דרכך ובטח עליו והוא יעשה 5
Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
והוציא כאור צדקך ומשפטך כצהרים 6
Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha, chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.
דום ליהוה-- והתחולל-לו אל-תתחר במצליח דרכו באיש עשה מזמות 7
Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.
הרף מאף ועזב חמה אל-תתחר אך-להרע 8
Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali, usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
כי-מרעים יכרתון וקוי יהוה המה יירשו-ארץ 9
Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa, koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.
ועוד מעט ואין רשע והתבוננת על-מקומו ואיננו 10
Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso; ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
וענוים יירשו-ארץ והתענגו על-רב שלום 11
Koma ofatsa adzalandira dziko ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.
זמם רשע לצדיק וחרק עליו שניו 12
Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano;
אדני ישחק-לו כי-ראה כי-יבא יומו 13
koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.
חרב פתחו רשעים-- ודרכו קשתם להפיל עני ואביון לטבוח ישרי-דרך 14
Oyipa amasolola lupanga ndi kupinda uta kugwetsa osauka ndi osowa, kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.
חרבם תבוא בלבם וקשתותם תשברנה 15
Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka.
טוב-מעט לצדיק-- מהמון רשעים רבים 16
Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;
כי זרועות רשעים תשברנה וסומך צדיקים יהוה 17
pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka, koma Yehova amasunga olungama.
יודע יהוה ימי תמימם ונחלתם לעולם תהיה 18
Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova, ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.
לא-יבשו בעת רעה ובימי רעבון ישבעו 19
Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota; mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri.
כי רשעים יאבדו ואיבי יהוה כיקר כרים כלו בעשן כלו 20
Koma oyipa adzawonongeka; adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo, iwo adzazimirira ngati utsi.
לוה רשע ולא ישלם וצדיק חונן ונותן 21
Oyipa amabwereka ndipo sabweza koma olungama amapereka mowolowamanja.
כי מברכיו יירשו ארץ ומקלליו יכרתו 22
Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko, koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa.
מיהוה מצעדי-גבר כוננו ודרכו יחפץ 23
Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu, amakhazikitsa mayendedwe ake;
כי-יפל לא-יוטל כי-יהוה סומך ידו 24
ngakhale atapunthwa sadzagwa, pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.
נער הייתי-- גם-זקנתי ולא-ראיתי צדיק נעזב וזרעו מבקש-לחם 25
Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya.
כל-היום חונן ומלוה וזרעו לברכה 26
Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu; ana awo adzadalitsika.
סור מרע ועשה-טוב ושכן לעולם 27
Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya.
כי יהוה אהב משפט ולא-יעזב את-חסידיו לעולם נשמרו וזרע רשעים נכרת 28
Pakuti Yehova amakonda wolungama ndipo sadzasiya okhulupirika ake. Iwo adzatetezedwa kwamuyaya, koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa;
צדיקים יירשו-ארץ וישכנו לעד עליה 29
olungama adzalandira dziko ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.
פי-צדיק יהגה חכמה ולשונו תדבר משפט 30
Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru, ndipo lilime lake limayankhula zolungama.
תורת אלהיו בלבו לא תמעד אשריו 31
Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake; mapazi ake saterereka.
צופה רשע לצדיק ומבקש להמיתו 32
Oyipa amabisala kudikira olungama; kufunafuna miyoyo yawoyo;
יהוה לא-יעזבנו בידו ולא ירשיענו בהשפטו 33
koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu.
קוה אל-יהוה ושמר דרכו וירוממך לרשת ארץ בהכרת רשעים תראה 34
Khulupirira Yehova, ndipo sunga njira yake; Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako; udzaona anthu oyipa akuwonongeka.
ראיתי רשע עריץ ומתערה כאזרח רענן 35
Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake.
ויעבר והנה איננו ואבקשהו ולא נמצא 36
Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso; ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso.
שמר-תם וראה ישר כי-אחרית לאיש שלום 37
Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama; udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.
ופשעים נשמדו יחדו אחרית רשעים נכרתה 38
Koma anthu ochimwa adzawonongeka; iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe.
ותשועת צדיקים מיהוה מעוזם בעת צרה 39
Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova; Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.
ויעזרם יהוה ויפלטם יפלטם מרשעים ויושיעם--כי-חסו בו 40
Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa; Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa, pakuti amathawira kwa Iye.

< תהילים 37 >