< תהילים 35 >

לדוד ריבה יהוה את-יריבי לחם את-לחמי 1
Salimo la Davide. Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane; mumenyane nawo amene akumenyana nane.
החזק מגן וצנה וקומה בעזרתי 2
Tengani chishango ndi lihawo; dzukani ndipo bwerani mundithandize.
והרק חנית וסגר לקראת רדפי אמר לנפשי ישעתך אני 3
Tengani mkondo ndi nthungo, kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa. Uzani moyo wanga kuti, “Ine ndine chipulumutso chako.”
יבשו ויכלמו מבקשי נפשי יסגו אחור ויחפרו--חשבי רעתי 4
Iwo amene akufunafuna moyo wanga anyozedwe ndi kuchita manyazi; iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
יהיו כמץ לפני-רוח ומלאך יהוה דוחה 5
Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
יהי-דרכם חשך וחלקלקת ומלאך יהוה רדפם 6
Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
כי-חנם טמנו-לי שחת רשתם חנם חפרו לנפשי 7
Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
תבואהו שואה לא-ידע ורשתו אשר-טמן תלכדו בשואה יפל-בה 8
chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa ukonde umene iwo abisa uwakole, agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
ונפשי תגיל ביהוה תשיש בישועתו 9
Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
כל עצמותי תאמרנה-- יהוה מי כמוך מציל עני מחזק ממנו ועני ואביון מגזלו 10
Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
יקומון עדי חמס אשר לא-ידעתי ישאלוני 11
Mboni zopanda chisoni zinayimirira, zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
ישלמוני רעה תחת טובה שכול לנפשי 12
Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
ואני בחלותם לבושי שק-- עניתי בצום נפשי ותפלתי על-חיקי תשוב 13
Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya. Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
כרע-כאח לי התהלכתי כאבל-אם קדר שחותי 14
ndinayendayenda ndi kulira maliro, kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga. Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima kukhala ngati ndikulira amayi anga.
ובצלעי שמחו ונאספו נאספו עלי נכים ולא ידעתי קרעו ולא-דמו 15
Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala; ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa. Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
בחנפי לעגי מעוג-- חרק עלי שנימו 16
Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe; anandikukutira mano awo.
אדני כמה תראה השיבה נפשי משאיהם מכפירים יחידתי 17
Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana? Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo, moyo wanga wopambana ku mikango.
אודך בקהל רב בעם עצום אהללך 18
Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
אל-ישמחו-לי איבי שקר שנאי חנם יקרצו-עין 19
Musalole adani anga onyenga akondwere chifukwa cha masautso anga; musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
כי לא שלום ידברו ועל רגעי-ארץ--דברי מרמות יחשבון 20
Iwowo sayankhula mwamtendere, koma amaganizira zonamizira iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
וירחיבו עלי פיהם אמרו האח האח ראתה עיננו 21
Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa! Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
ראיתה יהוה אל-תחרש אדני אל-תרחק ממני 22
Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete. Ambuye musakhale kutali ndi ine.
העירה והקיצה למשפטי אלהי ואדני לריבי 23
Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza! Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
שפטני כצדקך יהוה אלהי ואל-ישמחו-לי 24
Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga. Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
אל-יאמרו בלבם האח נפשנו אל-יאמרו בלענוהו 25
Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!” Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
יבשו ויחפרו יחדו-- שמחי רעתי ילבשו-בשת וכלמה-- המגדילים עלי 26
Onse amene amakondwera ndi masautso anga achite manyazi ndi kusokonezeka. Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana, avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
ירנו וישמחו חפצי צדקי ויאמרו תמיד יגדל יהוה החפץ שלום עבדו 27
Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa, afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo. Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke, Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
ולשוני תהגה צדקך כל-היום תהלתך 28
Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu ndi za matamando anu tsiku lonse.

< תהילים 35 >