< תהילים 27 >
לדוד יהוה אורי וישעי--ממי אירא יהוה מעוז-חיי ממי אפחד | 1 |
Salimo la Davide. Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
בקרב עלי מרעים-- לאכל את-בשרי צרי ואיבי לי המה כשלו ונפלו | 2 |
Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane kudzadya mnofu wanga, pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo, iwo adzapunthwa ndi kugwa.
אם-תחנה עלי מחנה-- לא-יירא לבי אם-תקום עלי מלחמה-- בזאת אני בוטח | 3 |
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzaopa. Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane, ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.
אחת שאלתי מאת-יהוה-- אותה אבקש שבתי בבית-יהוה כל-ימי חיי לחזות בנעם-יהוה ולבקר בהיכלו | 4 |
Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
כי יצפנני בסכה-- ביום רעה יסתרני בסתר אהלו בצור ירוממני | 5 |
Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
ועתה ירום ראשי על איבי סביבותי ואזבחה באהלו זבחי תרועה אשירה ואזמרה ליהוה | 6 |
Kotero mutu wanga udzakwezedwa kuposa adani anga amene andizungulira; pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe; ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
שמע-יהוה קולי אקרא וחנני וענני | 7 |
Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
לך אמר לבי--בקשו פני את-פניך יהוה אבקש | 8 |
Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!” Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
אל-תסתר פניך ממני-- אל תט-באף עבדך עזרתי היית אל-תטשני ואל-תעזבני אלהי ישעי | 9 |
Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
כי-אבי ואמי עזבוני ויהוה יאספני | 10 |
Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya Yehova adzandisamala.
הורני יהוה דרכך ונחני בארח מישור--למען שוררי | 11 |
Phunzitseni njira yanu Inu Yehova, munditsogolere mʼnjira yowongoka chifukwa cha ondizunza.
אל-תתנני בנפש צרי כי קמו-בי עדי-שקר ויפח חמס | 12 |
Musandipereke ku zokhumba za adani anga, pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane ndipo zikundiopseza.
לולא--האמנתי לראות בטוב-יהוה בארץ חיים | 13 |
Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
קוה אל-יהוה חזק ויאמץ לבך וקוה אל-יהוה | 14 |
Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.