< תהילים 26 >
לדוד שפטני יהוה-- כי-אני בתמי הלכתי וביהוה בטחתי לא אמעד | 1 |
Salimo la Davide. Weruzeni Inu Yehova pakuti ndakhala moyo wosalakwa. Ndadalira Yehova popanda kugwedezeka.
בחנני יהוה ונסני צרופה (צרפה) כליותי ולבי | 2 |
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni, santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
כי-חסדך לנגד עיני והתהלכתי באמתך | 3 |
pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse, ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
לא-ישבתי עם-מתי-שוא ועם נעלמים לא אבוא | 4 |
Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
שנאתי קהל מרעים ועם-רשעים לא אשב | 5 |
Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
ארחץ בנקיון כפי ואסבבה את-מזבחך יהוה | 6 |
Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
לשמע בקול תודה ולספר כל-נפלאותיך | 7 |
kulengeza mofuwula za matamando anu ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
יהוה--אהבתי מעון ביתך ומקום משכן כבודך | 8 |
Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo, malo amene ulemerero wanu umapezekako.
אל-תאסף עם-חטאים נפשי ועם-אנשי דמים חיי | 9 |
Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa, moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
אשר-בידיהם זמה וימינם מלאה שחד | 10 |
amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa, dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
ואני בתמי אלך פדני וחנני | 11 |
Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa; mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.
רגלי עמדה במישור במקהלים אברך יהוה | 12 |
Ndayima pa malo wopanda zovuta ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.