< תהילים 25 >

לדוד אליך יהוה נפשי אשא 1
Salimo la Davide. Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
אלהי--בך בטחתי אל-אבושה אל-יעלצו אויבי לי 2
Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane.
גם כל-קויך לא יבשו יבשו הבוגדים ריקם 3
Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
דרכיך יהוה הודיעני ארחותיך למדני 4
Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu;
הדריכני באמתך ולמדני-- כי-אתה אלהי ישעי אותך קויתי כל-היום 5
tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
זכר-רחמיך יהוה וחסדיך כי מעולם המה 6
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale.
חטאות נעורי ופשעי-- אל-תזכר כחסדך זכר-לי-אתה-- למען טובך יהוה 7
Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
טוב-וישר יהוה על-כן יורה חטאים בדרך 8
Yehova ndi wabwino ndi wolungama; choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
ידרך ענוים במשפט וילמד ענוים דרכו 9
Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake.
כל-ארחות יהוה חסד ואמת-- לנצרי בריתו ועדתיו 10
Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
למען-שמך יהוה וסלחת לעוני כי רב-הוא 11
Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
מי-זה האיש ירא יהוה-- יורנו בדרך יבחר 12
Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
נפשו בטוב תלין וזרעו יירש ארץ 13
Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
סוד יהוה ליראיו ובריתו להודיעם 14
Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.
עיני תמיד אל-יהוה כי הוא-יוציא מרשת רגלי 15
Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse, pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.
פנה-אלי וחנני כי-יחיד ועני אני 16
Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
צרות לבבי הרחיבו ממצוקותי הוציאני 17
Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira; masuleni ku zowawa zanga.
ראה עניי ועמלי ושא לכל-חטאותי 18
Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga ndipo mufafanize machimo anga onse.
ראה-איבי כי-רבו ושנאת חמס שנאוני 19
Onani mmene adani anga achulukira ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
שמרה נפשי והצילני אל-אבוש כי-חסיתי בך 20
Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa; musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndimathawira kwa Inu.
תם-וישר יצרוני כי קויתיך 21
Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
פדה אלהים את-ישראל-- מכל צרותיו 22
Wombolani Israeli Inu Mulungu, ku mavuto ake onse!

< תהילים 25 >