< תהילים 22 >
למנצח על-אילת השחר מזמור לדוד ב אלי אלי למה עזבתני רחוק מישועתי דברי שאגתי | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide. Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya? Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe? Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
אלהי--אקרא יומם ולא תענה ולילה ולא-דמיה לי | 2 |
Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha, usikunso, ndipo sindikhala chete.
ואתה קדוש-- יושב תהלות ישראל | 3 |
Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu; ndinu matamando a Israeli.
בך בטחו אבתינו בטחו ותפלטמו | 4 |
Pa inu makolo athu anadalira; iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
אליך זעקו ונמלטו בך בטחו ולא-בושו | 5 |
Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa. Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.
ואנכי תולעת ולא-איש חרפת אדם ובזוי עם | 6 |
Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu, wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
כל-ראי ילעגו לי יפטירו בשפה יניעו ראש | 7 |
Onse amene amandiona amandiseka; amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
גל אל-יהוה יפלטהו יצילהו כי חפץ בו | 8 |
“Iyeyu amadalira Yehova, musiyeni Yehovayo amulanditse. Musiyeni Yehova amupulumutse popeza amakondwera mwa Yehovayo.”
כי-אתה גחי מבטן מבטיחי על-שדי אמי | 9 |
Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
עליך השלכתי מרחם מבטן אמי אלי אתה | 10 |
Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu; kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
אל-תרחק ממני כי-צרה קרובה כי-אין עוזר | 11 |
Musakhale kutali ndi ine, pakuti mavuto ali pafupi ndipo palibe wina wondipulumutsa.
סבבוני פרים רבים אבירי בשן כתרוני | 12 |
Ngʼombe zazimuna zandizungulira; ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
פצו עלי פיהם אריה טרף ושאג | 13 |
Mikango yobangula pokadzula nyama, yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
כמים נשפכתי-- והתפרדו כל-עצמותי היה לבי כדונג נמס בתוך מעי | 14 |
Ine ndatayika pansi ngati madzi ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake. Mtima wanga wasanduka phula; wasungunuka mʼkati mwanga.
יבש כחרש כחי ולשוני מדבק מלקוחי ולעפר-מות תשפתני | 15 |
Mphamvu zanga zauma ngati phale, ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada; mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
כי סבבוני כלבים עדת מרעים הקיפוני כארי ידי ורגלי | 16 |
Agalu andizungulira; gulu la anthu oyipa landizinga. Alasa manja ndi mapazi anga.
אספר כל-עצמותי המה יביטו יראו-בי | 17 |
Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse; anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
יחלקו בגדי להם ועל-לבושי יפילו גורל | 18 |
Iwo agawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.
ואתה יהוה אל-תרחק אילותי לעזרתי חושה | 19 |
Koma Inu Yehova, musakhale kutali; Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
הצילה מחרב נפשי מיד-כלב יחידתי | 20 |
Pulumutsani moyo wanga ku lupanga, moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
הושיעני מפי אריה ומקרני רמים עניתני | 21 |
Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango; pulumutseni ku nyanga za njati.
אספרה שמך לאחי בתוך קהל אהללך | 22 |
Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga; ndidzakutamandani mu msonkhano.
יראי יהוה הללוהו-- כל-זרע יעקב כבדוהו וגורו ממנו כל-זרע ישראל | 23 |
Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
כי לא-בזה ולא שקץ ענות עני-- ולא-הסתיר פניו ממנו ובשועו אליו שמע | 24 |
Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
מאתך תהלתי בקהל רב--נדרי אשלם נגד יראיו | 25 |
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
יאכלו ענוים וישבעו-- יהללו יהוה דרשיו יחי לבבכם לעד | 26 |
Osauka adzadya ndipo adzakhuta; iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda. Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
יזכרו וישבו אל-יהוה-- כל-אפסי-ארץ וישתחוו לפניך כל-משפחות גוים | 27 |
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye, ndipo mabanja a mitundu ya anthu adzawerama pamaso pake,
כי ליהוה המלוכה ומשל בגוים | 28 |
pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.
אכלו וישתחוו כל-דשני-ארץ-- לפניו יכרעו כל-יורדי עפר ונפשו לא חיה | 29 |
Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
זרע יעבדנו יספר לאדני לדור | 30 |
Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye; mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
יבאו ויגידו צדקתו לעם נולד כי עשה | 31 |
Iwo adzalengeza za chilungamo chake kwa anthu amene pano sanabadwe pakuti Iye wachita zimenezi.