< תהילים 148 >
הללו-יה הללו את-יהוה מן-השמים הללוהו במרומים | 1 |
Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
הללוהו כל-מלאכיו הללוהו כל-צבאו | 2 |
Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
הללוהו שמש וירח הללוהו כל-כוכבי אור | 3 |
Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
הללוהו שמי השמים והמים אשר מעל השמים | 4 |
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
יהללו את-שם יהוה כי הוא צוה ונבראו | 5 |
Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
ויעמידם לעד לעולם חק-נתן ולא יעבור | 6 |
Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha.
הללו את-יהוה מן-הארץ-- תנינים וכל-תהמות | 7 |
Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
אש וברד שלג וקיטור רוח סערה עשה דברו | 8 |
inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo, mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
ההרים וכל-גבעות עץ פרי וכל-ארזים | 9 |
inu mapiri ndi zitunda zonse, inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
החיה וכל-בהמה רמש וצפור כנף | 10 |
inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse, inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
מלכי-ארץ וכל-לאמים שרים וכל-שפטי ארץ | 11 |
Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
בחורים וגם-בתולות זקנים עם-נערים | 12 |
Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe.
יהללו את-שם יהוה-- כי-נשגב שמו לבדו הודו על-ארץ ושמים | 13 |
Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
וירם קרן לעמו תהלה לכל-חסידיו-- לבני ישראל עם קרבו הללו-יה | 14 |
Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.